bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
John 5
John 5
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
← Chapter 4
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 6 →
1
Pambuyo pake kunali chikondwerero chachipembedzo cha Ayuda, ndipo Yesu adapitako ku Yerusalemuko.
2
Kumeneko kuli dziŵe, dzina lake pa Chiyuda ndi Betesida. Dziŵeli lili pafupi ndi Chipata cha Nkhosa, ndipo nlozingidwa ndi makonde asanu.
3
M'makondemo munkagona anthu ambiri odwala, akhungu, opunduka miyendo ndi opuwala ziwalo. [Iwoŵa ankadikira kuti madzi agwedezeke.
4
Pakuti nthaŵi zina mngelo wa Ambuye ankatsikira m'dziŵemo nkuvundula madziwo. Woyamba kuloŵamo madzi atavundulidwa, ankachira ngakhale akhale ndi nthenda yanji.]
5
Pakati pa anthu odwalawo panali wina amene adaadwala zaka 38.
6
Yesu adamuwona ali gone, nadziŵa kuti adaadwala nthaŵi yaitali. Tsono adamufunsa kuti, “Kodi ukufuna kuchira?”
7
Wodwalayo adati, “Ambuye, ndilibe munthu wondiloŵetsa m'dziŵemu madzi akavundulidwa. Ndikati ndiloŵemo, wina waloŵa kale.”
8
Yesu adamlamula kuti, “Dzuka, tenga mphasa yako, yamba kuyenda.”
9
Pompo munthuyo adachiradi, nanyamula mphasa yake nkuyamba kuyenda. Tsikulo linali la Sabata.
10
Choncho Ayuda adauza munthu amene adachirayo kuti, “Lero mpa Sabata. Malamulo athu sakulola kunyamula mphasa yako.”
11
Koma iye adati, “Amene wandichiritsa ndiye wandiwuza kuti, ‘Nyamula mphasa yako, yenda.’ ”
12
Iwo adamufunsa kuti, “Munthuyo ndani amene wakuuza kuti unyamule mphasa yako, uyende?”
13
Koma wochirayo sadamdziŵe, popeza kuti Yesu anali ataloŵerera m'kati mwa anthu ambiri amene anali pamenepo.
14
Pambuyo pake Yesu adapeza wochira uja m'Nyumba ya Mulungu, namuuza kuti, “Ona, wachira tsopano. Usakachimwenso, kuti chingakugwere choopsa china kuposa pamenepa.”
15
Munthuyo adapita nakauza Ayuda kuti Yesu ndiye amene wamchiritsa.
16
Popeza kuti linali tsiku la Sabata pamene Yesu adaachita zimenezi, Ayuda adayamba kumuvutitsa.
17
Koma Yesu adaŵauza kuti, “Atate anga akugwira ntchito mpaka tsopano, nanenso ndikugwira ntchito.”
18
Pamenepo ndiye Ayuda adankirankira kufuna kumupha. Ankati Yesu akuphwanya lamulo lokhudza Sabata, ndiponso ponena kuti Mulungu ndi Atate ake, ankadzilinganiza ndi Mulungu.
19
Tsono Yesu adati, “Kunena zoona Ine Mwanane sindingathe kuchita kanthu pandekha. Ndimangochita zimene ndikuwona Atate anga akuchita. Zimene Atate amachita, Mwana amachitanso zomwezo.
20
Pakuti Atate amakonda Mwana, namuwonetsa zonse zimene Iwo akuchita. Atate adzamuwonetsanso ntchito zoposa zimenezi, kuti inu muzizwe.
21
Monga Atate amaukitsa akufa, naŵapatsa moyo, moteronso Mwana amapatsa moyo kwa amene Iye afuna.
22
Atate saweruza munthu aliyense, koma adaika Mwana wake kuti akhale woweruza pa zonse.
23
Atate amafuna kuti anthu onse azilemekeza Mwana, monga momwe amalemekezera Atate. Munthu amene salemekeza Mwana, salemekezanso Atate amene adamtuma.
24
“Ndithu ndikunenetsa kuti munthu womva mau anga, nakhulupirira Iye amene adandituma, ameneyo ali ndi moyo wosatha. Iyeyo sazengedwa mlandu, koma watuluka kale mu imfa, ndipo waloŵa m'moyo.
25
Ndikunenetsanso kuti ikudza nthaŵi, ndipo yafika kale, pamene anthu amene ali ngati akufa adzamva mau a Mwana wa Mulungu, ndipo amene adzaŵakhulupirira adzakhala ndi moyo.
26
Monga Atate ali gwelo la moyo, momwemonso adaika Mwana wake kuti nayenso akhale gwelo la moyo.
27
Ndipo adapatsa Mwanayo mphamvu ya kuweruza anthu, chifukwa ndi Mwana wa Munthu.
28
Musadabwe nazo zimenezi, pakuti ikudza nthaŵi pamene anthu onse amene ali m'manda adzamva mau ake nadzatuluka.
29
Anthu amene adachita zabwino, adzauka kuti akhale ndi moyo, koma amene adachita zoipa, adzauka kuti azengedwe mlandu.”
30
“Ine sindingathe kuchita kanthu pandekha. Ndimaweruza monga momwe Atate amandiwuzira. Ndipo ndimaweruza molungama, popeza kuti sinditsata zimene ndifuna Ineyo, koma zimene afuna Atate amene adandituma.
31
“Ngati ndidzichitira ndekha umboni, umboni wangawo ngwosakwanira.
32
Pali wina wondichitira umboni, ndipo ndikudziŵa kuti umboni umene iye amandichitirawo ngwoona.
33
Inu nomwe mudaatuma amithenga anu kwa Yohane Mbatizi, ndipo iye adachitira umboni choona.
34
Sikuti Ine ndikudalira umboni wa munthu, koma ndikunena izi kuti inu mupulumuke.
35
Yohane anali ngati nyale yoyaka ndi yoŵala, ndipo inu mudafuna kukondwerera kuŵala kwakeko pa kanthaŵi.
36
Koma Ine ndili ndi umboni woposa wa Yohane. Atate adandipatsa ntchito zimene ndiyenera kuzichita, ndipo ntchito ndikuchitazi zikutsimikiza kuti Atate ndiwo adandituma.
37
Ndipo Atate omwewo amene adandituma, adandichitira umboni. Koma inu simudamve konse liwu lao, maonekedwe aonso simudaŵaone.
38
Mau ao sakhala mwa inu, chifukwa simumkhulupirira amene Atatewo adamtuma.
39
Mumaphunzira Malembo mozama, chifukwa mumaganiza kuti mupezamo moyo wosatha. Ndipotu ndi Malembo omwewo amene akundichitira umboni!
40
Komabe inu simufuna kudza kwa Ine kuti mukhale ndi moyo.
41
“Sindikufunafuna ulemu wa anthu ai.
42
Koma ndikukudziŵani, mulibe chikondi cha Mulungu mumtima mwanu.
43
Ine ndidadza m'dzina la Atate anga, ndipo inu simukundilandira. Koma wina atabwera m'dzina la iye yekha, iyeyo ndiye mungamlandire.
44
Mukamapatsana ulemu nokhanokha mumasangalala, koma simufuna konse kulandira ulemu wochokera kwa amene Iye yekha ndiye Mulungu. Nanga mungakhulupirire bwanji?
45
Musayese kuti ndine amene ndidzakunenezeni kwa Atate, ai. Wodzakunenezani alipo. Ndi Mose yemwe uja amene inu mumamdalira.
46
Mukadakhulupirira Mose moona, bwenzi mutakhulupiriranso Ine, pakuti iye adaalemba za Ine.
47
Koma ngati simukhulupirira zimene iyeyo adalemba, nanga mungakhulupirire bwanji mau anga?”
← Chapter 4
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 6 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21