bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
John 9
John 9
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
← Chapter 8
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 10 →
1
Pamene Yesu ankayenda, adaona munthu wa khungu lobadwa nalo.
2
Ophunzira ake adamufunsa kuti, “Aphunzitsi, kodi adachimwa ndani kuti munthu ameneyu abadwe wakhungu? Adachimwa ndi iyeyu kapena makolo ake?”
3
Yesu adati, “Sikuti iyeyu adachimwa kapena makolo ake ai. Koma adabadwa wakhungu kuti Mulungu aonetse ntchito zake mwa iye.
4
Kukali usana tizigwira ntchito za Atate amene adandituma. Usiku ukudza pamene munthu sangathe kugwira ntchito.
5
Pamene ndili pansi pano, ndine kuŵala kounikira anthu onse.”
6
Atanena zimenezi, Yesu adalavulira malovu pansi, nakanda thope ndi malovuwo. Kenaka adapaka thopelo m'maso mwa munthuyo,
7
namuuza kuti, “Pita ukasambe ku dziŵe la Siloamu.” (Tanthauzo la Siloamu ndiye kuti, Wotumidwa.) Munthuyo adapitadi, adakasamba, nabwerako akupenya.
8
Pamenepo anzake ndi anthu amene kale ankamuwona akupemphapempha adati, “Kodi uyu si uja ankakhala pansi apa nkumangopempha?”
9
Ena adati, “Ndiye amene.” Ena nkumati, “Iyai, akungofanafana naye.” Koma mwiniwakeyo adati, “Ai ndithu, ndine amene.”
10
Apo anthu aja adamufunsa kuti, “Nanga maso ako apenya bwanji?”
11
Iyeyo adati, “Munthu uja amati Yesuyu anakanda thope nalipaka m'maso mwangamu. Kenaka anandiwuza kuti, ‘Pita, ukasambe ku Siloamu. Ndinapitadi, ndipo nditasamba, ndayamba kupenya.’ ”
12
Anthuwo adamufunsa kuti, “Iyeyo ali kuti?” Munthu uja adati, “Kaya, sindikudziŵa.”
13
Tsono munthu uja kale sankapenyayu adapita naye kwa Afarisi.
14
Tsiku limene Yesu adaakanda thope namchiritsalo linali la Sabata.
15
Tsono Afarisi nawonso adamufunsa munthu uja kuti, “Iwe, wapenya bwanji?” Iye adaŵauza kuti, “Anandipaka thope m'maso mwanga, ine nkukasamba, ndipo tsopano ndikupenya.”
16
Afarisi ena adati, “Munthu amene uja ngwosachokera kwa Mulungu, chifukwa satsata lamulo lokhudza tsiku la Sabata.” Koma ena adati, “Kodi inu, munthu wochimwa nkuchita zizindikiro zozizwitsa zotere?” Choncho panali kutsutsana.
17
Tsono Afarisi aja adamufunsanso munthu uja kale sankapenyayu, adati, “Kodi iweyo ukuti chiyani za Iyeyo, m'mene wakuchiritsamu?” Iye adati, “Ndi mneneritu basi.”
18
Koma akulu a Ayudawo sadakhulupirire kuti munthuyo kale sankapenya ndipo tsopano akupenya, mpaka adaitanitsa makolo ake.
19
Tsono adaŵafunsa kuti, “Kodi inu, uyu ndi mwana wanu? Ndiye mukuti adaabadwadi wosapenya? Nanga zatani kuti tsopano akupenya?”
20
Makolo ake adati, “Chimene tikudziŵa ife nchakuti ameneyu ndi mwana wathu, ndipo adaabadwadi wosapenya.
21
Koma kuti tsopano akupenya, sitikudziŵa m'mene zachitikira. Zoti wamupenyetsa ndani kaya, ife sitikudziŵanso. Mufunseni mwiniwakeyu, ngwamkulu, afotokoze yekha.”
22
Makolo akewo adaatero chifukwa ankaopa akulu a Ayuda. Pakuti Ayuda anali atapangana kale kuti, ngati munthu adzavomereza kuti Yesu ndiye Mpulumutsi wolonjezedwa uja, adzamdula ku mpingo.
23
Nchifukwa chake makolo akewo adati, “Ngwamkulu, mufunseni mwiniwakeyu.”
24
Pamenepo Ayuda aja adamuitana kachiŵiri munthu uja kale sankapenyayu, namuuza kuti, “Lemekeza Mulungu, ndipo unene zoona. Ife tikudziŵa kuti munthu amene uja ngwochimwa.”
25
Iye adati, “Zakuti Iye ngwochimwa, ine sindikudziŵa. Chinthu chimodzi chokha ndikudziŵa, kuti kale ndinali wosapenya, koma tsopano ndikupenya.”
26
Iwo adamufunsa kuti, “Kodi anachita chiyani pamene anakupenyetsa?”
27
Iye adati, “Ndakuuzani kale, koma simumasamalako. Nanga chifukwa chiyani mukufuna kuzimvanso? Kapenatu nanunso mukufuna kukhala ophunzira ake eti?”
28
Pamenepo iwo adayamba kumlalatira, adati, “Wophunzira wake ndi iweyo. Ife ndifetu ophunzira a Mose.
29
Tikudziŵa kuti Mulungu adalankhula ndi Mose, koma uyu sitikudziŵa kumene wachokera.”
30
Munthuyo adati, “Pakudabwitsatu mpamenepa: kuti inuyo simukudziŵa kumene Iye wachokera, komabe wandipenyetsa.
31
Timadziŵa kuti Mulungu samvera anthu ochimwa. Koma munthu akasamala za Mulungu, nachita zimene Mulungu afuna, Mulungu amamumvera.
32
Nkale lomwe sikudamveke konse kuti wina adapenyetsa munthu wakhungu.
33
Munthu ameneyu akadapanda kuchokera kwa Mulungu, sakadatha konse kuchita kanthu.”
34
Iwo adati, “Iwe udabadwa m'machimo okhaokha. Ndiye iweyo nkutiphunzitsa ife?” Atatero adamtulutsa nkumudula ku mpingo.
35
Yesu adamva kuti Ayuda amtulutsa ndi kumdula ku mpingo munthu uja. Tsono pamene adampeza, adamufunsa kuti, “Kodi ukukhulupirira Mwana wa Munthu?”
36
Iye adati, “Ambuye, mundiwuzetu ndani Iyeyo, kuti ndimkhulupirire.”
37
Yesu adamuuza kuti, “Wamuwona kale, ndi yemwe akulankhula nawe.”
38
Iye adati, “Ambuye, ndikukhulupirira.” Atatero adamgwadira.
39
Tsono Yesu adati, “Ndidabwera pansi pano kudzaweruza, kuti osapenya apenye, ndipo openya achite khungu.”
40
Afarisi ena amene anali pafupi naye, atamva zimenezi adamufunsa kuti, “Kodi monga ifenso ndife akhungu?”
41
Yesu adati, “Mukadakhala akhungu, bwenzi mulibe mlandu. Koma chifukwa mukuti, ‘Tikupenya,’ ndiye kuti mlandu wanu ulipobe.”
← Chapter 8
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 10 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21