bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
John 18
John 18
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
← Chapter 17
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 19 →
1
Yesu atanena zimenezi, adapita ndi ophunzira ake kutsidya kwa kamtsinje ka Kedroni. Kumeneko kunali munda, ndipo adaloŵa m'menemo.
2
Yudasi yemwe, amene adapereka Yesu kwa adani ake, ankaŵadziŵa malowo, pakuti Yesu ankapita kumeneko kaŵirikaŵiri ndi ophunzira ake.
3
Yudasiyo adatenga gulu la asilikali achiroma pamodzi ndi asilikali a ku Nyumba ya Mulungu amene akulu a ansembe ndi Afarisi adaaŵatuma. Iwo adapita kumundako atatenga nyale ndi miyuni ndi zida zankhondo.
4
Yesu adaadziŵiratu zonse zimene zinalikudzamugwera. Nchifukwa chake Iye adaima poyera, naŵafunsa kuti, “Kodi mukufuna yani?”
5
Adamuyankha kuti, “Tikufuna Yesu wa ku Nazarete.” Yesu adati, “Ndine, ndilipo.” Yudasi, wompereka kwa adani ake uja, anali nao pomwepo.
6
Pamene Yesu adaŵayankha kuti, “Ndine, ndilipo,” iwo adabwerera m'mbuyo nagwa pansi.
7
Yesu adaŵafunsanso kuti, “Mukufuna yani kodi?” Iwo aja adati “Tikufuna Yesu wa ku Nazarete.”
8
Yesu adati, “Ndakuuzani kuti ndine, ndilipo. Tsono ngati mukufuna Ine, aŵa alekeni apite.”
9
(Adaatero kuti zipherezere zimene Iye adaanena kale kuti, “Sindidatayepo ndi mmodzi yemwe mwa amene mudandipatsa.”)
10
Simoni Petro anali ndi lupanga. Adalisolola, natema kapolo wa mkulu wa ansembe onse, mpaka kumusenga khutu la ku dzanja lamanja. Kapoloyo dzina lake anali Malkusi.
11
Apo Yesu adauza Petro kuti, “Bwezera lupanga lako m'chimake. Kodi ukuti ndisamwe chikho cha masautso chimene Atate andipatsa?”
12
Gulu la asilikali achiroma lija, pamodzi ndi mtsogoleri wao, ndiponso asilikali achiyuda, adagwira Yesu nammanga.
13
Poyamba adapita naye kwa Anasi, chifukwa anali mpongozi wa Kayafa, amene anali mkulu wa ansembe onse chaka chimenecho.
14
Kayafayo ndi yemwe uja amene adaalangiza anzake kuti nkwabwino koposa kuti munthu mmodzi afe m'malo mwa anthu onse.
15
Simoni Petro ndi wophunzira wina adatsatira Yesu. Wophunzira winayo anali wodziŵika kwa mkulu wa ansembe onse. Tsono iye adaloŵa pamodzi ndi Yesu m'bwalo la nyumba ya mkulu wa ansembeyo.
16
Koma Petro adaima pa khomo kunja. Wophunzira wina uja, amene anali wodziŵikayo, adatuluka nakalankhula ndi mtsikana wolonda pa khomo, nkumuloŵetsa Petroyo.
17
Mtsikanayo adafunsa Petro kuti, “Kodi inu sindinunso mmodzi mwa ophunzira a munthuyu?” Iye adati, “Ineyo? Iyai.”
18
Antchito pamodzi ndi asilikali achiyuda aja adaaimirira pamenepo atasonkha moto nkumaotha, chifukwa kunkazizira. Petro nayenso adaaimirira pomwepo nkumaotha nao motowo.
19
Tsono mkulu wa ansembe onse adafunsa Yesu za ophunzira ake, ndiponso za zimene Iye ankaphunzitsa.
20
Yesu adati, “Ine ndinkalankhula mosabisa pamaso pa anthu onse. Ndinkaphunzitsa m'nyumba zamapemphero ndiponso m'Nyumba ya Mulungu, m'mene anthu onse amasonkhana. Sindidalankhule kanthu mobisa ai.
21
Nanga tsono mukundifunsiranji Ineyo? Funsani amene adamva zomwe ndinkaŵauza. Iwowo akudziŵa zimene ndinkanena.”
22
Atanena zimenezi, mmodzi mwa asilikali oimirira pomwepo adamenya Yesu kumaso, adati, “Ungayankhe choncho kwa mkulu wa ansembe onse?”
23
Yesu adamuyankha kuti, “Ngati ndalankhula moipa, chitchule choipacho. Koma ngati ndalankhula moona, ukundimenyeranji?”
24
Anasi adatumiza Yesu ali chimangire kwa Kayafa, mkulu wa ansembe onse.
25
Simoni Petro anali chililibe akuwotha nao moto. Tsono ena adamufunsa kuti, “Kodi iwenso sindiwe mmodzi mwa ophunzira a munthu uja?” Petro adakana, adati, “Iyai.”
26
Wantchito wina wa mkulu wa ansembe onse, mbale wa munthu uja amene Petro adaamusenga khutu, adamufunsa kuti, “Kodi sindidakuwone m'munda muja uli naye?”
27
Petro adakananso, nthaŵi yomweyo tambala adalira.
28
Adamtenga Yesu kuchokera kwa Kayafa kupita naye ku bwalo la bwanamkubwa. Akuluakulu a Ayuda sadaloŵe nao m'bwalo la bwanamkubwalo, kuwopa kuti angaipitsidwe, pakuti ankafuna kudya phwando la Paska.
29
Motero Pilato adatulukira kwa iwo naŵafunsa kuti, “Mwampeza cholakwa chanji munthuyu?”
30
Iwo adati, “Akadapanda kuchita choipa ameneyu, sibwenzi titadzampereka kwa inu ai.”
31
Choncho Pilato adaŵauza kuti, “Mtengenitu tsono inuyo, mukamuweruze potsata malamulo anu.” Koma Ayudawo adati, “Ife sitiloledwa kupha munthu ai.”
32
(Zidaatero kuti zipherezere zimene Yesu adaanena za imfa yake.)
33
Pilato adaloŵanso m'nyumba yake ija, naitana Yesu. Adamufunsa kuti, “Kodi iwe, ndiwe Mfumu ya Ayuda?”
34
Yesu adati, “Kodi mukunena zimenezi mwa inu nokha, kapena ena adakuuzani za Ine?”
35
Pilato adati, “Ine ndine Myuda kodi? Anthu a mtundu wako womwe ndiponso akulu a ansembe ndiwo akupereka kwa ine. Udachita chiyani?”
36
Yesu adayankha kuti, “Ufumu wanga si wapansipano ai. Ufumu wanga ukadakhala wapansipano, bwenzi anyamata anga atamenya nkhondo kuti ndisaperekedwe kwa akulu a Ayuda. Komatu ai, ufumu wanga si wapansipano.”
37
Pilato adati, “Tsono ndiye kuti ndiwedi mfumu, ati?” Yesu adati, “Mwanena nokha kuti ndine mfumu. Ine ndidabwera pansi pano ndipo ndidabadwa kuti ndidzachitire umboni choona. Aliyense wokonda choona amamva mau anga.”
38
Pilato adamufunsa kuti, “Choona nchiyaninso?” Pilato atanena mau ameneŵa, adatulukiranso kwa Ayuda, naŵauza kuti, “Ine munthuyu sindikumpeza chifukwa chilichonse.
39
Koma potsata chizoloŵezi chanu, pa nthaŵi ya chikondwerero cha Paska ndimakumasulirani mkaidi mmodzi. Tsono kodi mukufuna kuti ndikumasulireni Mfumu ya Ayudayi?”
40
Pamenepo iwo adafuulanso kuti, “Ameneyu ai, koma Barabasi.” (Barabasiyo anali chigaŵenga.)
← Chapter 17
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 19 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21