bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
John 4
John 4
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
← Chapter 3
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 5 →
1
Afarisi adamva kuti Yesu akukopa ndi kubatiza ophunzira ambiri koposa Yohane.
2
(Komabe amene ankabatiza si Yesuyo, koma ophunzira ake).
3
Pamene Yesu adadziŵa kuti Afarisi azimva zimenezi, adachokako ku Yudeya napitanso ku Galileya.
4
Pa ulendowo ankayenera kudzera m'dziko la Samariya.
5
Tsono adafika ku mudzi wina wa ku Samariya, dzina lake Sikari, pafupi ndi kadziko kamene Yakobe adaapatsa Yosefe, mwana wake.
6
Kumeneko kunali chitsime cha Yakobe. Yesu adakhala pansi pambali pa chitsimecho, chifukwa anali atatopa ndi ulendo. Nthaŵi inali ngati 12 koloko masana.
7
Tsono padafika mai wina wachisamariya kudzatunga madzi. Yesu nkunena mopempha kuti, “Zikomo mundipatseko madzi akumwa.”
8
Nthaŵiyo nkuti ophunzira ake aja atakagula chakudya mu mzinda.
9
Mai wachisamariya uja adayankha nati, “Inu amene muli Myuda, bwanji mukupempha madzi kwa ine, mai wachisamariya?” (Pakutitu Ayuda sayenderana ndi Asamariya.)
10
Yesu adati, “Mukadadziŵa mphatso ya Mulungu, mukadadziŵanso amene akupempha madzi akumwayu, bwenzi mutampempha ndi inuyo mai, Iye nakupatsani madzi opatsa moyo.”
11
Maiyo adati, “Bambo, mulibe nchotungira chomwe, ndipo chitsimechi nchozama. Nanga madzi opatsa moyowo muŵatenga kuti?
12
Yakobe, kholo lathu ndiye adatipatsa chitsimechi, chimene mwiniwakeyo ankamwapo pamodzi ndi ana ake, ndiponso zoŵeta zake. Kodi Inu mungapambane iyeyo?”
13
Yesu adati, “Munthu aliyense womwako madzi aŵa, adzamvanso ludzu.
14
Koma aliyense wodzamwa madzi amene Ine ndidzampatse, sadzamvanso ludzu konse mpaka muyaya. Madzi amene ndidzampatsewo azidzatumphukira mwa iye ngati kasupe wa madzi opatsa moyo, nkumupatsa moyo wosatha.”
15
Maiyo adati, “Bambo, patsaniko ineyo madzi amenewo kuti ndisamamvenso ludzu kapena kumadzatunganso madzi kuno.”
16
Yesu adati, “Pitani mukaitane amuna anu, nkukabweranso kuno.”
17
Maiyo adati, “Ndilibe mwamuna.” Yesu adati, “Mwanenetsa kuti mulibe mwamuna.
18
Paja mwakwatiwapo kale ndi amuna asanu, ndipo mwamuna amene muli naye tsopano si wanunso. Mwanenazi nzoona.”
19
Maiyo adati, “Bambo, ndadziŵa tsopano kuti ndinu mneneri.
20
Makolo athu ankapembedza Mulungu pa phiri ili, koma inu Ayuda mumati ndi ku Yerusalemu kumene anthu ayenera kumakapembedzerako.”
21
Yesu adamuuza kuti, “Mai, ndithu ikudza nthaŵi pamene mudzapembedza Atate, osati pa phiri ili kapenanso ku Yerusalemu ai.
22
Asamariyanu mumapembedza chimene simuchidziŵa. Ayudafe timapembedza chimene timachidziŵa, pakuti chipulumutso nchochokera mwa Ayuda.
23
Koma ikudza nthaŵi, ndipo yafika kale, pamene anthu opembedza kwenikweni adzapembedza Atate mwauzimu ndi moona. Atate amafuna anthu otere kuti ndiwo azimpembedza.
24
Mulungu ndi mzimu, ndipo ompembedza Iye ayenera kumpembedza mwauzimu ndi moona.”
25
Maiyo adati, “Ndikudziŵa kuti akudza Mpulumutsi wolonjezedwa uja. Iyeyo akadzafika, adzatifotokozera zonse.”
26
Yesu adamuuza kuti, “Ndine amene, Ineyo amene ndikulankhula nanu, mai.”
27
Nthaŵi yomweyo ophunzira ake a Yesu adafika, ndipo ankadabwa kuti Iye akucheza ndi mkazi. Komabe panalibe amene adamufunsa kuti, “Zakhala bwanji?” Kapena kuti, “Bwanji mukulankhula naye?”
28
Maiyo adasiya mtsuko wake napita ku mudzi nkukauza anthu kuti,
29
“Tiyeni, mukaone munthu amene wandiwuza zonse zimene ine ndidachita. Kodi ameneyu sangakhale Mpulumutsi wolonjezedwa uja kapena?”
30
Apo anthuwo adatuluka m'mudzimo kubwera kwa Yesu,
31
Nthaŵi imeneyo ophunzira ake a Yesu ankamupempha kuti, “Aphunzitsi, idyani.”
32
Koma Iye adati, “Ine ndili nacho chakudya chimene inu simukuchidziŵa.”
33
Pamenepo ophunzirawo adayamba kufunsana kuti, “Kodi kapena wina wadzaŵapatsa kale chakudya?”
34
Koma Yesu adati, “Chakudya changa nkuchita zimene afuna Atate amene adandituma, kuti nditsirize ntchito imene Iwo adandipatsa.
35
Paja anthu amati, ‘Ikapita miyezi inai, ndiye kuti yafika nyengo yokolola.’ Koma ndithu, taonani m'mindamu, kodi simukuwona kuti mbeu zacha kale kudikira kholola?
36
Okolola ayamba kale kulandira malipiro, ndipo akututira mbeu ku moyo wosatha, kuti obzala ndi okolola akondwere pamodzi.
37
Paja amanenadi zoona aja amati, ‘Wobzala ndi wina, wokolola ndi winanso.’
38
Ine ndidakutumani kukakolola mbeu zimene simudagwirirepo ntchito. Anthu ena ndiwo adagwira ntchito, inu mwangolandirapo phindu la ntchito yaoyo.”
39
Asamariya ambiri a m'mudzi muja adakhulupirira Yesu chifukwa cha umboni wa mai uja, wakuti, “Iye wandiwuza zonse zimene ndidachita.”
40
Tsono pamene Asamariyawo adafika kwa Yesu, adampempha kuti akhale nao kwaoko. Ndipo adakhaladi komweko masiku aŵiri.
41
Pamenepo anthu enanso ambiri adakhulupirira chifukwa cha mau a Yesu.
42
Mwakuti adauza mai uja kuti, “Takhulupirira tsopano, osati chifukwa cha mau ako, koma chifukwa tadzimvera tokha. Tadziŵa kuti ameneyu ndi Mpulumutsidi wa anthu a pa dziko lonse lapansi.”
43
Atapita masiku aŵiriwo, Yesu adachoka napita ku Galileya.
44
Mwiniwakeyo anali atanena kuti, “Mneneri, anthu akwao samchitira ulemu.”
45
Komabe pamene adafika ku Galileya, Agalileya adamlandira popeza kuti eniakewo nawonso adaapita ku Yerusalemu ku chikondwerero cha Paska, ndipo adaaona zonse zimene Yesu adaachita pachikondwereropo.
46
Yesu adapitanso ku mudzi wa Kana ku Galileya, kumene Iye adaasandutsa madzi vinyo kuja. Panali Nduna ina ya mfumu imene mwana wake ankadwala ku Kapernao.
47
Pamene adamva kuti Yesu wafika ku Galileya kuchokera ku Yudeya, adadza kwa Iye nampempha kuti apite naye ku Kapernao, kuti akachiritse mwana wake amene anali pafupi kufa.
48
Yesu adamuuza kuti, “Mukapanda kuwona zizindikiro ndi zozizwitsa, simukhulupirira ai.”
49
Ndunayo idati, “Ndapota nanu Ambuye, tiyeni mwana wanga asanafe.”
50
Yesu adamuuza kuti, “Pitani! Mwana wanu wachira.” Munthuyo adakhulupiriradi mau a Yesuwo, ndipo adapita kwao.
51
Pa njira adakumana ndi antchito ake, ndipo iwo adamuuza kuti, “Mwana wanu wachira.”
52
Adaŵafunsa za nthaŵi imene adachira mwanayo, iwo nkunena kuti, “Malungo ake adamleka dzulo nthaŵi ya 1 koloko masana.”
53
Bamboyo adazindikira kuti inali nthaŵi yomwe Yesu adaamuuza kuti, “Mwana wanu wachira.” Tsono iye adakhulupirira pamodzi ndi onse a m'banja mwake.
54
Ichi chinali chizindikiro chachiŵiri chimene Yesu adaonetsa atafika ku Galileya kuchokera ku Yudeya.
← Chapter 3
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 5 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21