bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
John 13
John 13
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
← Chapter 12
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 14 →
1
Chikondwerero cha Paska chili pafupi, Yesu adaadziŵiratu kuti nthaŵi yake yafika yakuti achoke pansi pano kupita kwa Atate. Iye ankaŵakonda amene anali ake pansi pano, ndipo adaaŵakonda kotheratu.
2
Tsono Yesu ndi ophunzira ake ankadya chakudya chamadzulo. Satana nkuti ataika kale mumtima mwa Yudasi, mwana wa Simoni Iskariote, maganizo akuti akapereke Yesu kwa adani ake.
3
Yesu ankadziŵa kuti Atate adapereka zinthu zonse m'manja mwake. Ankadziŵanso kuti adachokera kwa Mulungu, ndipo kuti akubwerera kwa Mulungu.
4
Choncho pamene analikudya, Yesu adaimirira, adavula mwinjiro wake, natenga nsalu yopukutira nkuimanga m'chiwuno.
5
Atatero adathira madzi m'beseni, nayamba kutsuka mapazi a ophunzira ake, nkumaŵapukuta ndi nsalu yopukutira ija imene adaaimanga m'chiwuno.
6
Pamene adafika pa Simoni Petro, iyeyo adati, “Ambuye, Inuyo nkundisambitsa ine mapazi?”
7
Yesu adamuyankha kuti, “Zimene ndikuchitazi, sukuzidziŵa tsopano, koma udzazidziŵa m'tsogolo muno.”
8
Petro adati, “Simudzandisambitsa konse mapazi.” Yesu adamuyankha kuti, “Ngati sindikusambitsa, ndiye kuti chako palibe.”
9
Simoni Petro adati, “Ambuye, ngati ndi choncho, mutsuke osati mapazi anga okha, komanso manja anga ndi mutu womwe.”
10
Yesu adamuuza kuti, “Munthu amene wasamba, wayera yense. Palibe chifukwa choti asambenso, koma kungosamba mapazi okha basi. Tsono inu mwayera, koma osati nonsenu ai.”
11
Yesu ankamudziŵa munthu wodzampereka kwa adani ake, nchifukwa chake adaati, “Si nonsenu muli oyera.”
12
Yesu atatsuka mapazi a ophunzira ake, adavalanso mwinjiro wake nakakhalanso podyera paja. Kenaka adaŵafunsa kuti, “Kodi mwazimvetsa zimene ndakuchitiranizi?
13
Paja inu mumanditchula kuti, ‘Aphunzitsi’ ndiponso, ‘Ambuye.’ Apo mumalondola, pakuti ndine amene.
14
Tsono ngati Ine Mbuye wanu ndi Mphunzitsi wanu ndakusambitsani mapazi anu, ndiye kuti inunso muyenera kumasambitsana mapazi.
15
Ndakupatsani chitsanzo, kuti inunso muzichita monga momwe Ine ndakuchitirani inu.
16
Kunena zoona, wantchito saposa mbuye wake, nthumwinso siiposa woituma.
17
Ngati mudziŵa zimenezi, ndinu odala mukamazichita.
18
“Mauŵa sindikunenera nonsenu ai. Ndikuŵadziŵa amene ndaŵasankha. Koma ziyenera kuchitikadi zimene Malembo adanena kuti, ‘Amene ankadya nane pamodzi, yemweyo ndiye adandiwukira.’
19
Ndikukuuziranitu zimenezi tsopano zisanachitike, kuti zikadzachitika, mudzakhulupirire kuti Ine ndinedi Ndilipo.
20
Ndithu ndikunenetsa kuti wolandira aliyense amene ndamtuma, amalandira Ine. Ndipo wondilandira Ine, amalandira Iye amene adandituma.”
21
Yesu atanena zimenezi, adayamba kuvutika mu mtima ndipo adati, “Ndinene poyera pano: mmodzi mwa inu andipereka kwa adani anga.”
22
Ophunzira aja adayamba kupenyetsetsana, osadziŵa konse kuti akunena yani.
23
Wophunzira wina, yemwe Yesu ankamukonda kwambiri, adaakhala pambali pa Yesu.
24
Tsono Simoni Petro adamkodola nati, “Taŵafunsa, kodi akunena yani?”
25
Pamenepo iyeyo adatsamira pachifukwa pa Yesu, namufunsa kuti, “Ambuye, mukunena yani kodi?”
26
Yesu adati, “Yemwe ndimusunsire nkumupatsa mkate umene ndimunyemere ndi ameneyo.” Tsono atasunsa mkate wonyemawo adaupatsa Yudasi, mwana wa Simoni Iskariote.
27
Yudasi atangolandira mkatewo, Satana adaloŵa mwa iye. Yesu adamuuza kuti, “Zimene ufuna kuchita, kachite mwamsanga.”
28
Koma mwa amene ankadyawo panalibe ndi mmodzi yemwe amene adaamvetsa zimene adaamuuzazo.
29
Popeza kuti Yudasi ankasunga thumba la ndalama, anzake ankayesa kuti Yesu akumuuza kuti, “Kagule zofunika paphwando pano,” kapena kuti akapereke kanthu kwa osauka.
30
Yudasi atalandira mkate uja, pompo adatuluka. Nthaŵiyo nkuti kutada kale.
31
Yudasi atatuluka, Yesu adati, “Tsopano Mwana wa Munthu walemekezedwa, ndipo mwa Iyeyu Mulungu walemekezedwa.
32
Ngati Mulungu walemekezedwa mwa Iyeyu, Mulungu Mwini nayenso adzamlemekeza Iye, ndipo achita zimenezi tsopano apa.
33
Ana anga, ndili nanube kanthaŵi pang'ono. Mudzandifunafuna, koma ndikukuuzani tsopano, monga ndidauziranso akulu a Ayuda kuti, ‘Kumene ndikupita Ine, inu simungathe kufikako.’
34
Ndikukupatsani lamulo latsopano, lakuti muzikondana. Monga momwe Ine ndidakukonderani, inunso muzikondana.
35
Mukamakondana, anthu onse adzadziŵa kuti ndinudi ophunzira anga.”
36
Simoni Petro adafunsa Yesu kuti, “Ambuye, mukupita kuti?” Yesu adati, “Kumene ndikupita, sungathe kunditsatira tsopano ai, koma udzanditsatira bwino lino.”
37
Petro adamufunsa kuti, “Ambuye, chifukwa chiyani sindingathe kukutsatirani tsopano? Inetu nditha kutaya ngakhale moyo wanga chifukwa cha Inu.”
38
Apo Yesu adati, “Iweyo kutaya moyo wako chifukwa cha Ine! Ndithu ndikunenetsa kuti tambala asanalire, ukhala utandikana katatu kuti Ine sundidziŵa.”
← Chapter 12
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 14 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21