bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
John 2
John 2
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
← Chapter 1
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 3 →
1
Patapita masiku aŵiri, kunali ukwati ku mudzi wa Kana m'dera la Galileya. Amai ake a Yesu anali komweko.
2
Yesu nayenso pamodzi ndi ophunzira ake adaaitanidwa kuukwatiko.
3
Pamene vinyo adatha, amai ake a Yesu adamuuza kuti, “Waŵathera vinyo.”
4
Yesu adayankha kuti, “Mai, kodi mukuti nditani? Nthaŵi yangatu siinafike.”
5
Apo amai ake adauza anyamata amene ankatumikira kuti, “Chilichonse chimene akuuzeni, muchite.”
6
Pamenepo panali mbiya zamwala zisanu ndi imodzi, zimene adaaziikapo chifukwa cha mwambo wa kudziyeretsa wa Ayuda. M'mbiya iliyonse munkaloŵa madzi okwanira malita zana limodzi kapena kupitirirapo.
7
Tsono Yesu adauza anyamata aja kuti, “Dzazani mbiyazi ndi madzi.” Ndipo adazidzaza mpaka m'milomo.
8
Pambuyo pake adaŵauza kuti, “Tsopano tungani, kaperekeni kwa mkulu wa phwando,” Iwowo adakaperekadi.
9
Mkulu wa phwandoyo adalaŵa madzi osanduka vinyowo osadziŵa kumene achokera. (Koma anyamata aja amene adaatunga madziwo ankadziŵa.) Tsono mkulu wa phwandoyo adaitana mkwati,
10
namuuza kuti, “Anzanu amapereka vinyo wabwino kwambiri poyamba, kenaka anthu atakhuta, amaŵapatsa vinyo wokoma pang'ono. Koma inu mwasunga vinyo wabwino kwambiri kufikira tsopano.”
11
Yesu adaonetsa chizindikiro chake choyambachi m'mudzi wa Kana m'dera la Galileya. Pamenepo adaonetsa ulemerero wake, ndipo ophunzira ake adamkhulupirira.
12
Pambuyo pake Yesu adapita ku Kapernao, pamodzi ndi amai ake ndi abale ake ndi ophunzira ake, ndipo adakhala kumeneko masiku oŵerengeka.
13
Itayandikira nthaŵi ya Paska, chikondwerero cha Ayuda, Yesu adanyamuka kupita ku Yerusalemu.
14
Kumeneko adaloŵa m'Nyumba ya Mulungu napezamo anthu akugulitsa ng'ombe, nkhosa ndi nkhunda. Munalinso anthu osinthitsa ndalama.
15
Apo Yesu adapanga mkwapulo wazingwe nayamba kuŵatulutsira onse kunja, pamodzi ndi nkhosa ndi ng'ombe zao zomwe. Adagubudula matebulo a osinthitsa ndalama aja, naŵamwazira ndalama zao.
16
Ndipo adalamula ogulitsa nkhunda aja kuti, “Izi zitulutseni muno. Nyumba ya Atate anga musaisandutse nyumba yochitiramo malonda.”
17
Ophunzira ake adakumbukira Malembo aja akuti, “Changu chomwe ndimachitira nyumba yanu chidzandiphetsa.”
18
Pamenepo akuluakulu a Ayuda adamufunsa kuti, “Kodi mungatiwonetse chizindikiro chotani chakuti muli ndi ulamuliro wochitira zimenezi?”
19
Yesu adaŵayankha kuti, “Gwetsani nyumba ya Mulungu ino, Ine ndidzaimanganso masiku atatu.”
20
Apo iwo adati, “Nyumba ya Mulunguyi idatenga zaka 46 kuti aimange, tsono Inu nkuimanga masiku atatu chabe?”
21
Koma Yesu ankanena za thupi lake mophiphiritsa, pamene adaatchula Nyumba ya Mulungu.
22
Iye atauka kwa akufa, ophunzira ake adadzakumbukira kuti adaanena zimenezi, nakhulupirira Malembo ndiponso mau amene Yesu adaanenawo.
23
Pamene Yesu anali m'Yerusalemu pa chikondwerero cha Paska, anthu ambiri adayamba kuika chikhulupiriro chao pa Iye, poona zozizwitsa zimene ankachita.
24
Koma Yesu sadaikepo chikhulupiriro pa iwowo, popeza kuti Iye ankaŵadziŵa anthu onse.
25
Sankalira kuti wina achite chomuuza za munthu aliyense. Pakuti mwiniwakeyo ankadziŵa za m'mitima mwa anthu.
← Chapter 1
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 3 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21