bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
/
Ezekiel 1
Ezekiel 1
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 37
Chapter 38
Chapter 39
Chapter 40
Chapter 41
Chapter 42
Chapter 43
Chapter 44
Chapter 45
Chapter 46
Chapter 47
Chapter 48
Chapter 2 →
1
Ndipo kunali chaka cha makumi atatu, mwezi wachinai, tsiku lachisanu la mwezi, pokhala ine pakati pa andende kumtsinje Kebara, kunatseguka kumwamba, ndipo ndinaona masomphenya a Mulungu.
2
Tsiku lachisanu la mwezi, ndicho chaka chachisanu cha kutengedwa ndende mfumu Yehoyakini,
3
anadzadi mau a Yehova kwa Ezekiele wansembe, mwana wa Buzi, m'dziko la Ababiloni kumtsinje Kebara; ndi pomwepo dzanja la Yehova lidamkhalira.
4
Ndinapenya, ndipo taonani, mkuntho wa mphepo wochokera kumpoto, mtambo waukulu ndi moto wofukusika m'mwemo, ndi pozungulira pake padachita cheza, ndi m'kati mwake mudaoneka ngati chitsulo chakupsa m'kati mwa moto.
5
Ndi m'kati mwake mudaoneka mafaniziro a zamoyo zinai. Ndipo maonekedwe ao ndiwo anafanana ndi munthu,
6
ndi yense anali nazo nkhope zinai, ndi yense wa iwo anali nao mapiko anai.
7
Ndi mapazi ao anali mapazi oongoka, ndi kumapazi ao kunanga kuphazi kwa mwanawang'ombe; ndipo ananyezimira ngati mawalidwe a mkuwa wowalitsidwa.
8
Zinali naonso manja a munthu pansi pa mapiko ao pa mbali zao zinai; ndipo zinaizi zinali nazo nkhope zao ndi mapiko ao.
9
Mapiko ao analumikizana; sizinatembenuka poyenda; chilichonse chinayenda ndi kulunjika kutsogoloko.
10
Mafaniziro a nkhope zao zinali nayo nkhope ya munthu; ndi izi zinai zinali nayo nkhope ya mkango pa mbali ya kudzanja lamanja; ndi izi zinai zinali nayo nkhope ya ng'ombe pa mbali ya kudzanja lamanzere; izi zinai zinali nayonso nkhope ya chiombankhanga.
11
Ndi nkhope zao ndi mapiko ao zinagawikana kumutu; chilichonse chinali nao mapiko awiri olumikizana, ndi awiri anaphimba thupi.
12
Ndipo zinayenda, chilichonse chinalunjika kutsogolo kwake uko mzimu unafuna kumukako zinamuka, sizinatembenuka poyenda.
13
Kunena za mafaniziro a zamoyozo, maonekedwe ao ananga makala amoto, monga maonekedwe a miyuni; motowo unayendayenda pakati pa zamoyozo, ndi motowo unachita cheza, ndi m'motomo mudatuluka mphezi.
14
Ndipo zamoyozo zinathamanga ndi kubwerera, ngati maonekedwe a mphezi yong'anima.
15
Ndipo pakupenyerera ine zamoyozo, taonani, njinga imodziimodzi yoponda pansi pafupi ndi zamoyozo pa nkhope zao zinai.
16
Maonekedwe a njingazi ndi mapangidwe ao ananga mawalidwe a berulo; ndi izi zinai zinafanana mafaniziro ao; ndi maonekedwe ao ndi mapangidwe ao anali ngati njinga ziwiri zopingasitsana.
17
Poyenda zinayenda kumbali zao zinai, zosatembenuka poyenda.
18
Ndi mikombero yake inali yokuzika ndi yoopsa; ndi izi zinai zinali ndi mikombero yao yodzala ndi maso pozungulira pao.
19
Ndipo poyenda zamoyozo, njingazi zinayenda pambali pao; ndipo ponyamuka pansi zamoyozo, njinga zinanyamuka.
20
Kuli konse mzimu ukuti umuke, zinamuka komwe mzimu ukuti umuke; ndi njingazi zinanyamuka pambali pa izi; pakuti mzimu wa zamoyozo unali m'njingazo.
21
Poyenda zija zinayenda izi, poima zija zinaima izo; ndipo ponyamuka pansi zija njingazi zinanyamuka pambali pa izi; pakuti mzimu wa zamoyozo unali mu njingazi.
22
Ndi pa mitu ya zamoyozi panali chifaniziro cha thambo, monga mawalidwe a krustalo woopsa, loyalika pamwamba pamitu pao.
23
Ndi pansi pa thambolo mapiko ao analunjikana, lina kulunjika kulinzake; chilichonse chinali nao mapiko awiri akuphimba matupi ao, chakuno ndi chauko.
24
Ndipo pakuyenda izi ndinamva mkokomo wa mapiko ao, ngati mkokomo wa madzi aakulu, ngati mau a Wamphamvuyonse, phokoso lakusokosera ngati phokoso la ankhondo; pakuima zinagwetsa mapiko ao.
25
Ndipo panamveka mau pamwamba pa thambolo linali pamwamba pa mitu yao; pakuima izi zinagwetsa mapiko ao.
26
Ndi pamwamba pa thambolo linali pamitu pao panali chifaniziro cha mpando wachifumu, maonekedwe ake ngati mwala wa safiro; ndipo pa chifaniziro cha mpando wachifumu panali chifaniziro ngati maonekedwe ake a munthu wokhala pamwamba pake.
27
Ndipo ndinapenya ngati chitsulo chakupsa, ngati maonekedwe ake a moto m'kati mwake pozungulira pake, kuyambira maonekedwe a m'chuuno mwake ndi kumwamba kwake; ndipo kuyambira maonekedwe a m'chuuno mwake ndi kunsi kwake ndinaona ngati maonekedwe ake a moto; ndi kunyezimira kudamzinga.
28
Ngati maonekedwe a utawaleza uli m'mtambo tsiku la mvula, momwemo maonekedwe a kunyezimira kwake pozungulira pake. Ndiwo maonekedwe a chifaniziro cha ulemerero wa Yehova. Ndipo pakuchipenya ndinagwa nkhope pansi, ndipo ndinamva mau a wina wakunena.
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 37
Chapter 38
Chapter 39
Chapter 40
Chapter 41
Chapter 42
Chapter 43
Chapter 44
Chapter 45
Chapter 46
Chapter 47
Chapter 48
Chapter 2 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24
25
26
27
28
29
30
31
32
33
34
35
36
37
38
39
40
41
42
43
44
45
46
47
48