bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
/
Ezekiel 39
Ezekiel 39
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
← Chapter 38
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 37
Chapter 38
Chapter 39
Chapter 40
Chapter 41
Chapter 42
Chapter 43
Chapter 44
Chapter 45
Chapter 46
Chapter 47
Chapter 48
Chapter 40 →
1
Ndipo iwe, wobadwa ndi munthu, nenera motsutsana naye Gogi, uziti, Atero Ambuye Yehova, Taona, nditsutsana nawe Gogi, iwe mfumu yaikulu ya Meseki ndi Tubala;
2
ndipo ndidzakutembenuza, ndi kukutsogolera, ndi kukweza iwe uchoke ku malekezero a kumpoto; ndipo ndidzadza nawe kumapiri a Israele;
3
ndipo ndidzakantha uta wako kuuchotsa m'dzanja lako lamanzere, ndi kutayitsa mivi yako kudzanja lako lamanja.
4
Udzagwa pa mapiri a Israele, iwe ndi magulu ako onse, ndi mitundu ya anthu okhala ndi iwe; ndidzakupereka kwa mbalame zolusa za mitundu yonse, ndi kwa zilombo za kuthengo, akuyese chakudya.
5
Udzagwa kuthengo, koyera, pakuti ndanena ndine, ati Ambuye Yehova.
6
Ndipo ndidzatumizira moto Magogi, ndi iwo okhala mosatekeseka m'zisumbu; motero adzadziwa kuti Ine ndine Yehova.
7
Ndipo ndidzadziwikitsa dzina langa loyera pakati pa anthu anga Israele, osalola dzina langa loyera aliipsenso; ndipo amitundu adzadziwa kuti Ine ndine Yehova Woyerayo wa Israele.
8
Taonani, chikudza, chidzachitika, ati Ambuye Yehova, ndilo tsiku ndanenalo.
9
Ndipo iwo okhala m'midzi ya Israele adzatuluka, nadzasonkha moto, nadzatentha zida za nkhondo, ndi zikopa zotchinjiriza, mauta, ndi mivi, ndi ndodo, ndi mikondo; ndipo adzasonkha moto nazo zaka zisanu ndi ziwiri;
10
osatenga nkhuni kuthengo, kapena kuzitema kunkhalango; popeza adzasonkha moto ndi zidazo; nadzafunkha iwo amene anawafunkha, ndi kulanda zao za iwo adalanda zaozo, ati Ambuye Yehova.
11
Ndipo kudzachitika tsiku ilo, ndidzapatsa Gogi manda m'Israele, chigwa cha opitawo kum'mawa kwa nyanja; ndipo lidzaletsa opitawo, ndipo adzaika komweko Gogi ndi unyinji wake wonse, nadzachitcha, Chigwa cha unyinji wa Gogi.
12
Ndi a nyumba ya Israele adzapititsa miyezi isanu ndi iwiri alikuwaika, kuti ayeretse dziko.
13
Inde anthu onse a m'dziko adzawaika, nadzamveka nako tsiku lakulemekezedwa Ine, ati Ambuye Yehova.
14
Ndipo adzasankha anthu akupitapitabe m'dziko, ndi pamodzi ndi opitapitawo anthu akuika mafupa otsala pamtunda, kuliyeretsa; pakutha miyezi isanu ndi iwiri adzapwaira.
15
Ndipo opitapitawo adzapitapita m'dziko, ndipo wina akaona fupa la munthu aikepo chizindikiro, mpaka oikawo aliika m'chigwa cha unyinji wa Gogi.
16
Ndipo dzina la mudzi lidzakhala Hamona. Momwemo adzayeretsa dziko.
17
Ndipo iwe, wobadwa ndi munthu, atero Ambuye Yehova, Nena kwa mbalame za mitundu yonse, ndi kwa nyama zonse za kuthengo, Memezanani, idzani, sonkhanani kumbali zonse, kudza kunsembe yanga imene ndikupherani, ndiyo nsembe yaikulu pa mapiri a Israele, kuti mudzadye nyama ndi kumwa mwazi.
18
Mudzadya nyama ya amphamvu, ndi kumwa mwazi wa akalonga a padziko, wa nkhosa zamphongo, wa anaankhosa, ndi wa mbuzi, ndi wa ng'ombe, zonsezi zonenepa za ku Basani.
19
Ndipo mudzadya zonona mpaka mudzakhuta, ndi kumwa mwazi mpaka mudzaledzera za nsembe yanga ndakupherani.
20
Ndipo podyera panga mudzakhuta akavalo, ndi magaleta, ndi anthu amphamvu, ndi anthu onse a nkhondo, ati Ambuye Yehova.
21
Ndipo ndidzaika ulemerero wanga mwa amitundu; ndi amitundu onse adzaona chiweruzo changa ndachichita, ndi dzanja langa limene ndinawaikira.
22
Ndipo nyumba ya Israele idzadziwa kuti Ine ndine Yehova Mulungu wao, kuyambira tsiku ilo ndi m'tsogolomo.
23
Ndipo amitundu adzadziwa kuti nyumba ya Israele idalowa undende chifukwa cha mphulupulu zao, popeza anandilakwira Ine; ndipo ndinawabisira nkhope yanga; m'mwemo ndinawapereka m'dzanja la adani ao, nagwa iwo onse ndi lupanga.
24
Ndinachita nao monga mwa kudetsedwa kwao, ndi monga mwa kulakwa kwao, ndipo ndinawabisira nkhope yanga.
25
Chifukwa chake atero Ambuye Yehova, Tsopano ndidzabweza undende wa Yakobo, ndi kuchitira chifundo nyumba yonse ya Israele, ndipo ndidzachitira dzina langa loyera nsanje.
26
Ndipo adzasenza manyazi ao, ndi zolakwa zao zonse, zimene anandilakwira nazo, pokhala mosatekeseka iwo m'dziko lao, opanda wina wakuwaopsa;
27
nditabwera nao kuchoka kwa mitundu ya anthu, nditawasokolotsa m'maiko a adani ao, ndi kuzindikiridwa Woyera mwa iwo pamaso pa amitundu ambiri.
28
Ndipo adzadziwa kuti Ine ndine Yehova Mulungu wao, popeza ndinalola atengedwe ndende kunka kwa amitundu, koma ndinawasonkhanitsanso akhale m'dziko lao, osasiyakonso mmodzi yense wa iwowa.
29
Ndipo sindidzawabisiranso nkhope yanga, popeza ndatsanulira mzimu wanga pa nyumba ya Israele, ati Ambuye Yehova.
← Chapter 38
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 37
Chapter 38
Chapter 39
Chapter 40
Chapter 41
Chapter 42
Chapter 43
Chapter 44
Chapter 45
Chapter 46
Chapter 47
Chapter 48
Chapter 40 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24
25
26
27
28
29
30
31
32
33
34
35
36
37
38
39
40
41
42
43
44
45
46
47
48