bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
/
Ezekiel 43
Ezekiel 43
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
← Chapter 42
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 37
Chapter 38
Chapter 39
Chapter 40
Chapter 41
Chapter 42
Chapter 43
Chapter 44
Chapter 45
Chapter 46
Chapter 47
Chapter 48
Chapter 44 →
1
Pamenepo anamuka nane kuchipata choloza kum'mawa,
2
ndipo taonani, ulemerero wa Mulungu wa Israele unadzera njira ya kum'mawa, ndi mau ake ananga mkokomo wa madzi ambiri, ndi dziko linanyezimira ndi ulemerero wake.
3
Ndipo maonekedwe a masomphenya ndinawaona anali monga masomphenya aja ndinawaona pakudza ine kupasula mudzi; ndi masomphenyawa anali ngati masomphenya aja ndinawaona kumtsinje wa Kebara; ndipo ndinagwa nkhope pansi.
4
Ndipo ulemerero wa Yehova unalowa m'Kachisi kudzera njira ya chipata choloza kum'mawa.
5
Ndipo mzimu unandinyamula numuka nane kubwalo la m'kati; ndipo taonani, ulemerero wa Yehova unadzaza Kachisi.
6
Ndipo ndinamva wina alikulankhula nane ali m'Kachisi, naima nane munthu.
7
Ndipo anati kwa ine, Wobadwa ndi munthu iwe, pano mpokhala mpando wachifumu wanga, mpoponda kumapazi anga, pomwe ndidzakhala pakati pa ana a Israele kosatha; ndi nyumba ya Israele siidzadetsanso dzina langa loyera, ngakhale iwo kapena mafumu ao, mwa chigololo chao, ndi mitembo ya mafumu ao pa misanje yao,
8
ndi kuika chiundo chao pafupi pa chiundo changa, ndi mphuthu yao pa mbali ya mphuthu yanga, ndipo panali khoma lokha pakati pa iwo ndi Ine, nadetsa dzina langa loyera ndi zonyansa zao anazichita; chifukwa chake ndinawatha mu mkwiyo wanga.
9
Ataye tsono chigololo chao ndi mitembo ya mafumu ao kutali kwa Ine, ndipo ndidzakhala pakati pao kosatha.
10
Wabadwa ndi munthu iwe, onetsa nyumba ya Israele Kachisiyu, kuti achite manyazi ndi mphulupulu zao; ndipo ayese muyeso wake.
11
Ndipo ngati akachita manyazi nazo zonse anazichita, uwadziwitse maonekedwe a Kachisiyu, ndi muyeso wake, ndi potulukira pake, ndi polowera pake, ndi malongosoledwe ake onse, ndi malemba ake onse, ngakhale maonekedwe ake onse, ndi malamulo ake onse; nuwalembere pamaso pao, kuti asunge maonekedwe ake onse, ndi malemba ake onse, nawachite.
12
Lamulo la Kachisi ndi ili: pamwamba pa phiri malire ake onse pozungulira pake azikhala opatulika kwambiri. Taonani, limeneli ndi lamulo la Kachisi.
13
Ndipo miyeso ya guwa la nsembe, kuyesa mikono ndi iyi: (mkonowo ndiwo mkono ndi chikhato), tsinde lake likhale mkono, ndi kupingasa kwake dzanja limodzi, ndi mkuzi wake m'mphepete mwake pozungulira pake kuyesa zala; ili ndi tsinde la guwali.
14
Ndi kuyambira kunsi kwake kunthaka, kufikira phaka lamunsi, mikono iwiri; ndi kupingasa kwake mkono umodzi; ndi kuyambira phaka laling'ono kufikira phaka lalikulu mikono inai; ndi kupingasa kwake mkono.
15
Ndi guwa lapamwamba mikono inai; ndi pamoto pa guwa padzatuluka nyanga zinai.
16
Ndi pamoto pa guwa, m'litali mwake mikono khumi ndi iwiri, ndi kupingasa kwake khumi ndi iwiri, laphwamphwa mbali zake zinai.
17
Ndi phaka, m'litali mwake mikono khumi ndi inai, ndi kupingasa kwake mikono khumi ndi inai kumbali zake zinai; ndi mkuzi wake pozungulira pake mkono wa nusu, ndi tsinde lake mkono pozungulira pake, ndi makwerero ake aloza kum'mawa.
18
Ndipo anati kwa ine, Wobadwa ndi munthu iwe, atero Ambuye Yehova, Malemba a guwa la nsembe, tsiku lakulimanga, kuperekapo nsembe zopsereza, ndi kuwazapo mwazi, ndi awa;
19
Upatse ansembe Alevi, a mbeu za Zadoki, okhala pafupi ndi Ine, kunditumikira Ine, ati Ambuye Yehova, mwanawang'ombe, akhale wa nsembe yauchimo.
20
Nutengeko mwazi wake, ndi kupaka pa nyanga zinai za guwa, ndi pangodya zinai za phaka, ndi pa mkuzi wake pozungulira; motero uliyeretse ndi kulichitira chotetezera.
21
Utengenso ng'ombe ya nsembe yauchimo, aipsereze pa malo oikika a Kachisi kunja kwa malo opatulika.
22
Ndipo tsiku lachiwiri upereke tonde wopanda chilema, akhale nsembe yauchimo; ndipo ayeretse guwa la nsembe monga umo analiyeretsera ndi ng'ombeyo.
23
Utatha kuliyeretsa upereke mwanawang'ombe wopanda chilema, ndi nkhosa yamphongo ya zoweta yopanda chilema.
24
Ndipo ubwere nazo kwa Yehova, ndi ansembe athirepo mchere, ndi kuzipereka nsembe yopsereza ya Yehova.
25
Masiku asanu ndi awiri uzikonzera mbuzi tsiku ndi tsiku, ikhale nsembe yauchimo; akonzerenso mwanawang'ombe, ndi nkhosa yamphongo ya zoweta zopanda chilema.
26
Masiku asanu ndi awiri achite chotetezera guwali ndi kuliyeretsa, momwemo alipatule.
27
Ndipo atatsiriza masiku, kudzachitika tsiku lachisanu ndi chitatu ndi m'tsogolo, ansembe azichita nsembe zanu zopsereza, ndi nsembe zanu zoyamika pa guwalo; ndipo ndidzakulandirani, ati Ambuye Yehova.
← Chapter 42
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 37
Chapter 38
Chapter 39
Chapter 40
Chapter 41
Chapter 42
Chapter 43
Chapter 44
Chapter 45
Chapter 46
Chapter 47
Chapter 48
Chapter 44 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24
25
26
27
28
29
30
31
32
33
34
35
36
37
38
39
40
41
42
43
44
45
46
47
48