bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
/
Ezekiel 20
Ezekiel 20
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
← Chapter 19
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 37
Chapter 38
Chapter 39
Chapter 40
Chapter 41
Chapter 42
Chapter 43
Chapter 44
Chapter 45
Chapter 46
Chapter 47
Chapter 48
Chapter 21 →
1
Ndipo kunali chaka chachisanu ndi chiwiri, mwezi wachisanu, tsiku lakhumi la mwezi, anadza akulu ena a Israele kufunsira kwa Yehova, nakhala pansi iwowa pamaso panga.
2
Ndipo anandidzera mau a Yehova, akuti,
3
Wobadwa ndi munthu iwe lankhula ndi akulu a Israele, nunene nao, Atero Ambuye Yehova, Mwadza kodi kufunsira kwa Ine? Pali Ine, sindidzafunsidwa ndi inu, ati Ambuye Yehova.
4
Udzawaweruza kodi, wobadwa ndi munthu iwe? Udzawaweruza? Uwadziwitse zonyansa za makolo ao,
5
nunene nao, Atero Ambuye Yehova, Tsiku lija ndinamsankha Israele, ndi kukwezera mbeu ya nyumba ya Yakobo dzanja langa, ndi kudzidziwitsa kwa iwo m'dziko la Ejipito, pakuwakwezera dzanja langa, ndi kuti, Ine ndine Yehova Mulungu wanu;
6
tsiku lomwelo ndinawakwezera dzanja langa kuwatulutsa m'dziko la Ejipito, kunka nao kudziko ndinawazondera, moyenda mkaka ndi uchi, ndilo lokometsetsa mwa maiko onse;
7
ndipo ndinanena nao, Aliyense ataye zonyansa za pamaso pake, nimusadzidetsa ndi mafano a Ejipito; Ine ndine Yehova Mulungu wanu.
8
Koma anapandukira Ine, osafuna kundimvera Ine, sanataye yense zonyansa pamaso pake, sanaleke mafano a Ejipito; pamenepo ndidati ndiwatsanulire ukali wanga, kuwakwaniritsira mkwiyo wanga m'dziko la Ejipito.
9
Koma ndinachichita chifukwa cha dzina langa, kuti lisadetsedwe pamaso pa amitundu amene anakhala pakati pao, amene pamaso pao ndinadzidziwitsa kwa iwo, pakuwatulutsa m'dziko la Ejipito.
10
Momwemo ndinatuluka nao m'dziko la Ejipito, ndi kulowa nao kuchipululu.
11
Ndinawapatsanso malemba anga, ndi kuwadziwitsa maweruzo anga, ndiwo munthu akawachita adzakhala nao ndi moyo.
12
Ndipo ndinawapatsanso masabata anga akhale chizindikiro pakati pa Ine ndi iwo, kuti adziwe kuti Ine ndine Yehova wakuwapatula.
13
Koma nyumba ya Israele inapandukira Ine m'chipululu, sanayende m'malemba anga, nanyoza maweruzo anga, amene munthu akawachita adzakhala nao ndi moyo; ndi masabata anga anawaipsa kwambiri; pamenepo ndidati ndiwatsanulire ukali wanga m'chipululu kuwatha.
14
Koma ndinachichita chifukwa cha dzina langa, kuti lisaipsidwe pamaso pa amitundu amene ndinawatulutsa pamaso pao.
15
Ndipo ndinawakwezeranso dzanja langa m'chipululu, kusawalowetsa m'dzikolo ndidawapatsa, moyenda mkaka ndi uchi, ndilo lokometsetsa mwa maiko onse;
16
popeza ananyoza maweruzo anga, osayenda m'malemba anga, naipsa masabata anga; pakuti mitima yao inatsata mafano ao.
17
Koma diso langa lidawaleka osawaononga, sindinawatha onse m'chipululu.
18
Ndipo ndinati kwa ana ao m'chipululu, Musamayenda m'malemba a atate anu, musawasunga maweruzo ao, kapena kudzidetsa ndi mafano ao;
19
Ine ndine Yehova Mulungu wanu, muziyenda m'malemba anga, ndi kusunga maweruzo anga, ndi kuwachita;
20
muzipatulanso masabata anga, ndipo adzakhala chizindikiro pakati pa Ine ndi inu, kuti mudziwe kuti Ine ndine Yehova Mulungu wanu.
21
Koma anawo anapandukira Ine, sanayende m'malemba anga, kapena kusunga maweruzo anga kuwachita, amene munthu akawachita adzakhala nao ndi moyo; anaipsa masabata anga; pamenepo ndinati ndidzawatsanulira ukali wanga, kuwakwaniritsira mkwiyo wanga m'chipululu.
22
Koma ndinabweza dzanja langa ndi kuchichita, chifukwa cha dzina langa; kuti lisaipsidwe pamaso pa amitundu, amene ndinawatulutsa pamaso pao.
23
Ndinawakwezeranso dzanja langa m'chipululu, kuti ndidzawabalalitsa mwa amitundu, ndi kuwamwaza m'maiko;
24
popeza sanachite maweruzo anga, koma ananyoza malemba anga, naipsa masabata anga, ndi maso ao anatsata mafano a atate ao.
25
Momwemonso ndinawapatsa malemba amene sanali abwino, ndi maweruzo osakhala nao ndi moyo;
26
ndinawadetsanso m'zopereka zao; pakuti anapititsa pamoto onse oyamba kubadwa kuti ndiwapasule; kuti adziwe kuti Ine ndine Yehova.
27
Chifukwa chake wobadwa ndi munthu iwe, lankhula ndi nyumba ya Israele, nunene nao, Atero Ambuye Yehova, Mwa ichinso atate anu anandichitira mwano pakundilakwira Ine.
28
Nditafika nao m'dzikolo ndinawakwezera dzanja langa kuwapatsa ilo, anapenya chitunda chilichonse chachitali, ndi mtengo uliwonse wagudugudu, naphera pomwepo nsembe zao, naperekapo nsembe zao zondiputa, aponso anachita fungo lao lokoma, nathiraponso nsembe zao zothira.
29
Pamenepo ndinanena nao, Msanje wotani uwu mumapitako? Momwemo dzina lake litchedwa Msanje, mpaka lero lino.
30
Chifukwa chake uziti kwa nyumba ya Israele, Atero Ambuye Yehova, Mudzidetsa kodi monga umo anachitira makolo anu? Muchita chigololo kodi kutsata zonyansa zao?
31
Ndipo popereka zopereka zanu popititsa ana anu pamoto, mudzidetsa kodi ndi mafano anu onse mpaka lero lino? Ndipo kodi ndidzafunsidwa ndi inu, nyumba ya Israele? Pali Ine, ati Ambuye Yehova, sindidzafunsidwa ndi inu;
32
ndi ichi chimauka mumtima mwanu sichidzachitika, umo mukuti, Tidzakhala ngati amitundu, ngati mabanja a m'maiko, kutumikira mtengo ndi mwala.
33
Pali Ine, ati Ambuye Yehova, zedi ndi dzanja lamphamvu, ndi mkono wotambasuka, ndi ukali wotsanulidwa, ndidzakhala mfumu yanu.
34
Ndipo ndidzakutulutsani mwa mitundu ya anthu, ndi kukusonkhanitsani m'maiko munabalalikamo ndi dzanja lamphamvu, ndi mkono wotambasuka, ndi ukali wotsanulidwa.
35
Ndipo ndidzalowa nanu m'chipululu cha mitundu ya anthu, ndi kukuweruzani komweko popenyana maso.
36
Monga ndinaweruza makolo anu m'chipululu cha dziko la Ejipito, momwemo ndidzaweruza inu, ati Ambuye Yehova.
37
Ndipo ndidzakupititsani pansi pa ndodo ya mbusa ndi kukulowetsani m'chimango cha chipangano;
38
ndipo ndidzasankhula mwa inu opanduka ndi ondilakwira, ndidzawatulutsa m'dziko logoneramo iwo; koma sadzalowa m'dziko la Israele; motero mudzadziwa kuti Ine ndine Yehova.
39
Ndipo inu, nyumba ya Israele, atero Ambuye Yehova, mukani, tumikirani yense mafano ake, ndi m'tsogolo momwe, popeza simundimvera Ine; koma musaipsanso dzina langa lopatulika ndi zopereka zanu ndi mafano anu.
40
Pakuti pa phiri langa lopatulika, pa phiri lothuvuka la Israele, ati Ambuye Yehova, pomwepo onse a nyumba ya Israele, onsewo adzanditumikira Ine m'dzikomo; pomwepo ndidzawalandira, ndi pomwepo ndidzafuna nsembe zanu zokweza, ndi zoyamba za msonkho wanu, pamodzi ndi zopatulika zanu zonse.
41
Ngati fungo lokoma ndidzakulandirani pakukutulutsani mwa mitundu ya anthu, ndipo ndidzakusonkhanitsani kukuchotsani m'maiko munabalalikiramo, ndipo ndidzazindikirika Woyera mwa inu pamaso pa amitundu.
42
Ndipo mudzadziwa kuti Ine ndine Yehova, pakukulowetsani Ine m'dziko la Israele, m'dzikoli ndinalikwezera dzanja langa kulipereka kwa makolo anu.
43
Ndi pomwepo mudzakumbukira njira zanu, ndi zonse mudazichita ndi kudzidetsa nazo, ndipo mudzakhala onyansa pamaso pa inu nokha, chifukwa cha zoipa zanu zonse mudazichita.
44
M'mwemo mudzadziwa kuti Ine ndine Yehova nditachita nanu chifukwa cha dzina langa, si monga mwa njira zanu zoipa, kapena monga mwa machitidwe anu ovunda, nyumba ya Israele inu, ati Ambuye Yehova.
45
Ndipo anandidzera mau a Yehova, akuti,
46
Wobadwa ndi munthu iwe, lozetsa nkhope yako njira ya kumwera, nubenthulire mau kumwera, nunenere nkhalango ya kuthengo la kumwera kwa Yuda;
47
nuziti kwa nkhalango ya kumwera kwa Yuda, Tamvera mau a Yehova, Atero Ambuye Yehova, Taona ndidzayatsa moto mwa iwe, udzanyeketsa mtengo uliwonse wauwisi mwa iwe, ndi mtengo uliwonse wouma; malawi amoto sadzazimika, ndi nkhope zonse kuyambira kumwera kufikira kumpoto zidzapsa nao.
48
Ndi anthu onse adzaona kuti Ine Yehova ndinauyatsa, sudzazimika.
49
Pamenepo ndinati, Ha, Ambuye Yehova! Anandinena, Wonena mafanizo uyu.
← Chapter 19
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 37
Chapter 38
Chapter 39
Chapter 40
Chapter 41
Chapter 42
Chapter 43
Chapter 44
Chapter 45
Chapter 46
Chapter 47
Chapter 48
Chapter 21 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24
25
26
27
28
29
30
31
32
33
34
35
36
37
38
39
40
41
42
43
44
45
46
47
48