bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
/
Ezekiel 42
Ezekiel 42
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
← Chapter 41
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 37
Chapter 38
Chapter 39
Chapter 40
Chapter 41
Chapter 42
Chapter 43
Chapter 44
Chapter 45
Chapter 46
Chapter 47
Chapter 48
Chapter 43 →
1
Pamenepo anatuluka nane kunka kubwalo la kunja, njira ya kumpoto; nalowa nane kunyumba yazipinda idali pandunji pa mpatawo, ndi pandunji pa nyumbayo inaloza kumpoto.
2
Chakuno cha m'litali mwake mwa mikono zana limodzi kunali khomo la kumpoto, ndi kupingasa kwake mikono makumi asanu.
3
Pandunji pa mikono makumi awiri a bwalo lam'kati, ndi pandunji pa moyalamo mwa miyala, mwa bwalo lakunja, panali khonde lam'mwamba, lokomana ndi khonde linzake losanjikika pachiwiri.
4
Ndi kukhomo kwa zipinda anakonza poyendapo, kupingasa kwake mikono khumi m'kati mwake, njira ya mikono zana limodzi, ndi makomo ao analoza kumpoto.
5
Ndipo zipinda zapamwamba zinachepa, pakuti makonde am'mwamba analanda pamenepo, chifukwa chake zinachepa koposa zapansi ndi zapakati m'nyumba yazipinda.
6
Pakuti zinasanjikizana pawiri, ndipo zinalibe nsanamira ngati nsanamira za kumabwalo; chifukwa chake zam'mwambazo zinachepa koposa zakunsi ndi pakati kuyambira pansi.
7
Ndipo linga linali kunjalo, lolingana ndi nyumba yazipinda, kuloza kubwalo lakunja, popenyana ndi nyumba yazipinda, m'litali mwake munali mikono makumi asanu.
8
Pakuti kupingasa kwake kwa nyumba yazipinda inali m'bwalo lakunja, kunali mikono makumi asanu; ndipo taonani, kuloza kukhomo la Kachisi inali mikono zana limodzi.
9
Ndipo pansi pa zipinda izi panali polowera mbali ya kum'mawa, poloweramo kuchoka kubwalo lakunja.
10
M'kuchindikira kwa linga la bwalo, kuloza kumwera, chakuno cha mpatawo, chakuno cha nyumba, panali nyumba yazipinda.
11
Ndipo njira ya pakhomo pao inanga maonekedwe njira ya kunyumba yazipinda yoloza kumpoto, inalingana nayo m'litali mwake, momwemonso kupingasa kwake; ndi m'matulukiro mwake monse munali monga mwa machitidwe a inzake, ndi monga mwa makomo a inzake.
12
Ndi monga mwa makomo a zipinda za kumwera panali khomo polekeza njira, ndiyo njira yokhudzana ndi linga la kum'mawa polowamo.
13
Pamenepo anati kwa ine, Zipinda za kumpoto, ndi zipinda za kumwera, zili chakuno cha mpatawo, ndizo zipinda zopatulika, kumene ansembe okhala pafupi pa Yehova azidyera zinthu zopatulika kwambiri; kumeneko aziika zopatulika kwambiri, ndi nsembe yaufa, ndi nsembe yauchimo, ndi nsembe yopalamula; pakuti malowo ndi opatulika.
14
Atalowa ansembe asatulukenso m'malo opatulika kunka kubwalo lakunja, koma komweko aziika zovala zao zimene atumikira nazo; pakuti zili zopatulika; ndipo avale zovala zina, nayandikire zinthu wamba za anthu.
15
Atatha tsono kuyesa nyumba ya m'katimo, anatuluka nane njira ya chipata choloza kum'mawa nayesa bwalo pozungulira pake.
16
Anayesa mbali ya kum'mawa, ndi bango loyesera, mikono mazana asanu, kuyesa ndi bango loyesera.
17
Anayesa mbali ya kumpoto mikono mazana asanu, kuyesa ndi bango loyesera.
18
Anayesa mbali ya kumwera mikono mazana asanu, kuyesa ndi bango loyesera.
19
Anatembenukira kumbali ya kumadzulo, nayesa mikono mazana asanu ndi bango loyesera.
20
Analiyesa mbali zake zinai, linali nalo linga pozungulira pake, utali wake mikono mazana asanu, chitando chake mikono mazana asanu, kusiyanitsa pakati pa zopatulika ndi zinthu wamba.
← Chapter 41
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 37
Chapter 38
Chapter 39
Chapter 40
Chapter 41
Chapter 42
Chapter 43
Chapter 44
Chapter 45
Chapter 46
Chapter 47
Chapter 48
Chapter 43 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24
25
26
27
28
29
30
31
32
33
34
35
36
37
38
39
40
41
42
43
44
45
46
47
48