bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
/
Ezekiel 3
Ezekiel 3
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
← Chapter 2
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 37
Chapter 38
Chapter 39
Chapter 40
Chapter 41
Chapter 42
Chapter 43
Chapter 44
Chapter 45
Chapter 46
Chapter 47
Chapter 48
Chapter 4 →
1
Ndipo ananena nane, Wobadwa ndi munthu iwe, Idya chimene wachipeza; idya mpukutu uwu, numuke ndi kunena ndi nyumba ya Israele.
2
Pamenepo ndinatsegula pakamwa panga ndipo anandidyetsa mpukutuwo.
3
Nati kwa ine, Wobadwa ndi munthu iwe, dyetsa m'mimba mwako, nudzaze matumbo ako ndi mpukutu uwu ndakupatsawu. M'mwemo ndinaudya, ndi m'kamwa mwanga munazuna ngati uchi.
4
Ndipo anati kwa ine, Wobadwa ndi munthu iwe, Muka, nufike kwa nyumba ya Israele, nunene nao mau anga.
5
Pakuti sutumizidwa kwa anthu a chinenedwe chosamveka ndi chovuta, koma kwa nyumba ya Israele;
6
si kwa mitundu yambiri ya anthu a chinenedwe chosamveka ndi chovuta, amene sukhoza kudziwitsa chinenedwe chao. Zedi ndikakutumiza kwa iwowa adzamvera iwe.
7
Koma nyumba ya Israele siidzakumvera, pakuti siifuna kundimvera Ine; pakuti nyumba yonse ya Israele ndiyo yolimba mutu ndi youma mtima.
8
Taona ndakhwimitsa nkhope yako itsutsane nazo nkhope zao; ndalimbitsanso mutu wako utsutsane nayo mitu yao.
9
Ndalimbitsa mutu wako woposa mwala wolimbitsitsa, usawaopa kapena kutenga nkhawa pamaso pao; pakuti iwo ndiwo nyumba yopanduka.
10
Ananenanso nane, Wobadwa ndi munthu iwe, mau anga onse ndidzawanena ndi iwe uwalandire m'mtima mwako, utawamva m'makutu mwako.
11
Numuke, nufike kwa andende kwa ana a anthu a mtundu wako, nunene nao ndi kuwauza, Atero Yehova Mulungu, ngakhale akamva kapena akaleka kumva.
12
Pamenepo mzimu unandinyamula, ndipo ndinamva kumbuyo kwanga mau a mkokomo waukulu, ndi kuti, Wodala ulemerero wa Yehova m'malo mwake.
13
Ndipo ndinamva mkokomo wa mapiko a zamoyozo pakukhudzana, ndi mlikiti wa njingazo m'mbali mwa izo, ndilo phokoso la mkokomo waukulu.
14
M'mwemo mzimu unandinyamula ndi kuchoka nane; ndipo ndinamuka wowawidwa, womyuka mtima; koma dzanja la Yehova linandigwirizitsa.
15
Ndipo ndinafika kwa andende ku Telabibu, okhala kumtsinje Kebara, ndiko kwao; ndipo ndinakhalako wodabwa pakati pao masiku asanu ndi awiri.
16
Ndipo kunali atatha masiku asanu ndi awiri, mau a Yehova anandidzera, ndi kuti,
17
Wobadwa ndi munthu iwe, ndakuika ukhale mlonda wa nyumba ya Israele, m'mwemo mvera mau otuluka m'kamwa mwanga, nundichenjezere iwo.
18
Ndikanena kwa woipa, Udzafa ndithu, koma iwe osamchenjeza, wosanena kumchenjeza woipayo aleke njira yake yoipa, kumsunga ndi moyo, woipa yemweyo adzafa mu mphulupulu yake; koma mwazi wake ndidzaufuna pa dzanja lako.
19
Koma ukachenjeza woipa, osabwerera iye kuleka choipa chake kapena njira yake yoipa, adzafa mu mphulupulu yake; koma iwe walanditsa moyo wako.
20
Momwemonso akabwerera wolungama kuleka chilungamo chake, ndi kuchita chosalungama, ndipo ndikamuikira chomkhumudwitsa, adzafa; popeza sunamchenjeza, adzafa m'tchimo lake, ndi zolungama zake adazichita sizidzakumbukika; koma mwazi wake ndidzaufuna pa dzanja lako.
21
Koma ukamchenjeza wolungamayo, kuti asachimwe wolungamayo, ndipo sachimwa, adzakhala ndi moyo ndithu, popeza anachenjezedwa; ndipo iwe walanditsa moyo wako.
22
Ndipo dzanja la Yehova linandikhalira komweko, nati kwa ine, Nyamuka, tuluka kunka kuchidikha, ndipo pomwepo ndidzalankhula ndi iwe.
23
Ndipo ndinauka ndi kutuluka kunka kuchidikha, ndipo taonani, ulemerero wa Yehova unaimako monga ulemerero uja ndinauona kumtsinje Kebara, ndipo ndinagwa nkhope pansi.
24
Pamenepo unandilowa mzimu ndi kundiimika ndikhale chilili; ndipo analankhula ndi ine, nanena nane, Muka, katsekedwe m'nyumba mwako.
25
Koma iwe wobadwa ndi munthu, taona, adzakuikira iwe zingwe zolimba, nadzakumanga nazo, ndipo sudzatuluka pakati pao;
26
ndipo ndidzamamatiritsa lilime lako kumalakalaka ako, kuti ukhale wosanena, wosawakhalira wakuwadzudzula; pakuti iwo ndiwo nyumba yopanduka.
27
Koma pamene ndilankhula nawe ndidzatsegula pakamwa pako, nudzanena nao, Atero Yehova Mulungu. Wakumvera amvere, wosafuna kumvera akhale; pakuti iwo ndiwo nyumba yopanduka.
← Chapter 2
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 37
Chapter 38
Chapter 39
Chapter 40
Chapter 41
Chapter 42
Chapter 43
Chapter 44
Chapter 45
Chapter 46
Chapter 47
Chapter 48
Chapter 4 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24
25
26
27
28
29
30
31
32
33
34
35
36
37
38
39
40
41
42
43
44
45
46
47
48