bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
/
Ezekiel 32
Ezekiel 32
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
← Chapter 31
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 37
Chapter 38
Chapter 39
Chapter 40
Chapter 41
Chapter 42
Chapter 43
Chapter 44
Chapter 45
Chapter 46
Chapter 47
Chapter 48
Chapter 33 →
1
Ndipo kunali chaka chakhumi ndi chiwiri, mwezi wakhumi ndi chiwiri, tsiku loyamba la mwezi, anandidzera mau a Yehova, akuti,
2
Wobadwa ndi munthu iwe, takwezera Farao mfumu ya Aejipito nyimbo yamaliro; uziti naye, Unafanana nao msona wa mkango wa amitundu, unanga ng'ona ya m'nyanja, unabuka m'mitsinje mwako, nuvundulira madzi ndi mapazi ako, ndi kudetsa mitsinje yao.
3
Atero Ambuye Yehova, Ndidzakuponyera khoka langa mwa msonkhano wa mitundu yambiri ya anthu, nadzakuvuulira m'khoka mwanga.
4
Ndipo ndidzakusiya pamtunda, ndidzakuponya kuthengo koyera, ndi kuteretsa pa iwe mbalame zonse za m'mlengalenga, ndi kukhutitsa zilombo za dziko lonse lapansi ndi iwe.
5
Ndipo ndidzaika nyama yako pamapiri, ndi kudzaza zigwa ndi msinkhu wako.
6
Ndipo ndidzamwetsa dziko losambiramo iwe ndi mwazi wako, kufikira kumapiri; ndi mitsinje idzadzala nawe.
7
Ndipo pakukuzima iwe ndidzaphimba thambo, ndi kudetsa nyenyezi zake; ndidzaphimba dzuwa ndi mtambo, ndi mwezi sudzaonetsa kuwala kwake.
8
Ndidzakudetsera miyuni yonse yakuunikira kuthambo, ndi kuchititsa mdima pa dziko lako, ati Ambuye Yehova.
9
Ndidzavutanso mitima ya mitundu yambiri ya anthu, pakufikitsa Ine chionongeko chako mwa amitundu, m'maiko amene sunawadziwa.
10
Ndipo ndidzasumwitsa nawe mitundu yambiri ya anthu, ndi mafumu ao adzachita malunga chifukwa cha iwe, pakung'animitsa Ine lupanga langa pamaso pao; ndipo adzanjenjemera mphindi zonse, yense chifukwa cha moyo wake tsiku lakugwa iwe.
11
Pakuti atero Ambuye Yehova, Lupanga la mfumu ya ku Babiloni lidzakudzera.
12
Ndidzagwetsa aunyinji ako ndi malupanga a eni mphamvu, ndiwo onse oopsetsa a amitundu; ndipo adzaipsa kudzikuza kwa Ejipito, ndi aunyinji ake onse adzaonongeka.
13
Ndidzaononganso nyama zake zonse za kumadzi ambiri; ndi phazi la munthu silidzavundulira, ndi ziboda za nyama zosawavundulira.
14
Pamenepo ndidzadikhitsa madzi ake, ndi kuyendetsa madzi a m'mitsinje mwao ngati mafuta, ati Ambuye Yehova.
15
Pakusanduliza Ine dziko la Ejipito likhale lopasuka ndi labwinja, dziko losowa zodzaza zake, pakukantha Ine onse okhala m'mwemo, pamenepo adzadziwa kuti Ine ndine Yehova.
16
Iyi ndi nyimbo ya maliro adzalira nayo, ana akazi a amitundu adzachita nayo maliro; adzalirira nayo Ejipito ndi aunyinji ake onse, ati Ambuye Yehova.
17
Kunalinso chaka chakhumi ndi chiwiri, tsiku lakhumi ndi chisanu la mwezi, anandidzera mau a Yehova, ndi kuti,
18
Wobadwa ndi munthu iwe, lirira aunyinji a Ejipito, nuwagwetsere iye ndi ana akazi a amitundu omveka kunsi kwa dziko, pamodzi ndi iwo akutsikira kudzenje.
19
Uposa yani m'kukoma kwako? Tsika, nuikidwe ndi osadulidwa.
20
Adzagwa pakati pa iwo ophedwa ndi lupanga, operekedwa kwa lupanga, mkokereko ndi aunyinji ake onse.
21
Amphamvu oposa ali m'kati mwa manda adzanena naye, pamodzi ndi othandiza ake, Anatsikira, agonako osadulidwawo, ophedwa ndi lupanga.
22
Asiriya ali komwe ndi msonkhano wake wonse, manda ake amzinga; ophedwa onsewo, adagwa ndi lupanga;
23
manda ao aikidwa ku malekezero a dzenje, ndi gulu lake lizinga manda ake; ophedwa onsewo adagwa ndi lupanga, amene anopsetsa m'dziko la amoyo.
24
Elamu ali komwe ndi gulu lake lonse lozinga manda ake; ophedwa onsewo, adagwa ndi lupanga; amene anatsikira osadulidwa kunsi kwake kwa dziko, amene anaopsetsa m'dziko la amoyo, nasenza manyazi ao, pamodzi ndi iwo akutsikira kudzenje.
25
Pakati pa ophedwa anamuikira kama, iye ndi aunyinji ake onse, manda ake amzinga, onsewo osadulidwa, ophedwa ndi lupanga, pakuti anaopsetsa la amoyo, nasenza manyazi ao, pamodzi ndi iwo akutsikira kudzenje, aikidwa pakati pa ophedwa.
26
Meseki, Tubala, ndi aunyinji ake onse ali komweko, manda ake amzinga; onsewo osadulidwa, ophedwa ndi lupanga; pakuti anaopsetsa m'dziko la amoyo.
27
Koma sagona pamodzi ndi amphamvu osadulidwa adagwawo amene anatsikira kumanda ndi zida zao za nkhondo, amene anawatsamiritsa malupanga ao; ndi mphulupulu zao zili pa mafupa ao; pakuti anaopsetsa amphamvu m'dziko la amoyo.
28
Ndipo udzathyoledwa pakati pa osadulidwa, nudzagona pamodzi ndi iwo ophedwa ndi lupanga.
29
Edomu ali komwe, mafumu ake ndi akalonga ake onse, amene anaikidwa mu mphamvu yao, pamodzi ndi iwo ophedwa ndi lupanga; agona pamodzi ndi osadulidwa, ndi iwo akutsikira kudzenje.
30
Akalonga a kumpoto ali komwe onsewo, ndi Asidoni onse, amene anatsikira pamodzi ndi ophedwa, nachita manyazi chifukwa cha kuopsetsa anachititsaku ndi mphamvu yao, nagona osadulidwa pamodzi ndi iwo ophedwa ndi lupanga, nasenza manyazi ao pamodzi ndi iwo otsikira kudzenje.
31
Farao adzawaona, nadzasangalala nao aunyinji ake onse, Farao ndi ankhondo ake onse ophedwa ndi lupanga, ati Ambuye Yehova.
32
Pakuti ndinaika kuopsa kwake m'dziko la amoyo; ndipo adzaikidwa pakati pa osadulidwa, pamodzi ndi iwo ophedwa ndi lupanga, ndiye Farao ndi aunyinji ake onse, ati Ambuye Yehova.
← Chapter 31
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 37
Chapter 38
Chapter 39
Chapter 40
Chapter 41
Chapter 42
Chapter 43
Chapter 44
Chapter 45
Chapter 46
Chapter 47
Chapter 48
Chapter 33 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24
25
26
27
28
29
30
31
32
33
34
35
36
37
38
39
40
41
42
43
44
45
46
47
48