bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
/
Ezekiel 34
Ezekiel 34
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
← Chapter 33
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 37
Chapter 38
Chapter 39
Chapter 40
Chapter 41
Chapter 42
Chapter 43
Chapter 44
Chapter 45
Chapter 46
Chapter 47
Chapter 48
Chapter 35 →
1
Ndipo mau a Yehova anandidzera, akuti,
2
Wobadwa ndi munthu iwe, Nenera motsutsa abusa a Israele; nenera, nuti nao abusawo, Atero Ambuye Yehova, Tsoka abusa a Israele odzidyetsa okha; kodi abusa sayenera kudyetsa nkhosa?
3
Mukudya mafuta, muvala ubweya, mukupha zonenepa; koma simudyetsa nkhosa.
4
Zofooka simunazilimbitsa; yodwala simunaichiritsa, yothyoka simunailukira chika, yopirikitsidwa simunaibweza, yotayika simunaifuna; koma munazilamulira mwamphamvu ndi moopsa.
5
M'mwemo zinamwazika posowa mbusa, nizinakhala chakudya cha zilombo zilizonse za kuthengo, popeza zinamwazika.
6
Nkhosa zanga zinasokera kumapiri ali onse, ndi pa chitunda chilichonse chachitali; inde nkhosa zanga zinabalalika pa dziko lonse lapansi, ndipo panalibe wakuzipwaira kapena kuzifunafuna.
7
Chifukwa chake abusa inu, imvani mau a Yehova:
8
Pali Ine, ati Ambuye Yehova, zedi, popeza nkhosa zanga zinakhala nyama, ndi nkhosa zanga zinakhala chakudya cha zilombo zonse za kuthengo, chifukwa kunalibe mbusa, ndi abusa anga sanafunafune nkhosa zanga, koma abusawo anadzidyetsa okha, osadyetsa nkhosa zanga;
9
chifukwa chake, abusa inu, imvani mau a Yehova:
10
Atero Ambuye Yehova, Taonani, Ine ndiipidwa nao abusa, ndidzafunsa nkhosa zanga pa dzanja lao, ndi kuwaletsa asadyetsenso nkhosazo, ngakhale kudzidyetsa okha sadzachitanso; ndipo ndidzalanditsa nkhosa zanga pakamwa pao, zisakhale chakudya chao.
11
Pakuti atero Ambuye Yehova, Taonani, Ine, Inedi ndidzapwaira nkhosa zanga ndi kuzifunafuna.
12
Monga mbusa afunafuna nkhosa zake tsiku lokhala iye pakati pa nkhosa zake zobalalika, momwemo ndidzafunafuna nkhosa zanga; ndipo ndidzawalanditsa m'malo monse anabalalikamo tsiku la mitambo ndi la mdima.
13
Ndipo ndidzazitulutsa mwa mitundu ya anthu, ndi kuzisonkhanitsa m'maiko, ndi kulowa nazo m'dziko lao; ndipo ndidzazidyetsa pa mapiri a Israele, patimitsinje, ndi ponse pokhala anthu m'dziko.
14
Ndidzazidyetsa podyetsa pabwino; ndi pa mapiri atali a Israele padzakhala kholo lao, apo adzagona m'khola mwabwino, nadzadya podyetsa pokometsera pa mapiri a Israele.
15
Ine ndekha ndidzadyetsa nkhosa zanga, ndi kuzigonetsa, ati Ambuye Yehova.
16
Ndidzafuna yotayika, ndi kubweza yopirikitsidwa, ndi kulukira chika yothyoka mwendo, ndikulimbitsa yodwalayo; koma yonenepa ndi yolimba ndidzaziononga, ndidzazidyetsa ndi chiweruzo.
17
Ndipo inu, gulu langa, atero Ambuye Yehova, ndiweruza pakati pa zoweta ndi zoweta, nkhosa zamphongo ndi atonde.
18
Kodi chikucheperani, kuti mwadya podyetsa pabwino? Muyenera kodi kupondereza ndi mapazi anu podyera panu potsala? Muyenera kumwa madzi odikha, ndi kuvundulira otsalawo ndi mapazi anu?
19
Ndi nkhosa zanga zidye kodi zoponderezeka ndi mapazi anu, ndi kumwa zovunduliridwa ndi mapazi anu?
20
Chifukwa chake atero nao Ambuye Yehova, Taonani, Ine, Inedi ndidzaweruza pakati pa zoweta zonenepa, ndi zoweta zoonda.
21
Popeza mukankha ndi nthiti ndi phewa, nimugunda zodwala zonse ndi nyanga zanu, mpaka mwazibalalitsa kubwalo,
22
chifukwa chake ndidzapulumutsa gulu langa lisakhalenso chakudya; ndipo ndidzaweruza pakati pa zoweta ndi zoweta.
23
Ndipo ndidzaziutsira mbusa mmodzi; iye adzazidyetsa, ndiye mtumiki wanga Davide, iye adzazidyetsa, nadzakhala mbusa wao.
24
Ndipo Ine Yehova ndidzakhala Mulungu wao, ndi mtumiki wanga Davide kalonga pakati pao; Ine Yehova ndanena.
25
Ndipo ndidzapangana nazo pangano la mtendere, ndi kuleketsa zilombo zoipa m'dzikomo; ndipo zidzakhala mosatekeseka m'chipululu, ndi kugona kunkhalango.
26
Pakuti ndidzaika izi ndi milaga yozungulira chitunda changa, zikhale mdalitso; ndipo ndidzavumbitsa mivumbi m'nyengo yake, padzakhala mivumbi ya madalitso.
27
Ndi mitengo ya kuthengo idzapereka zobala zao, ndi nthaka idzapereka zipatso zake, ndipo adzakhazikika m'dziko mwao; ndipo adzadziwa kuti Ine ndine Yehova, nditadula zomangira goli lao, ndi kuwalanditsa m'manja mwa iwo akuwatumikiritsa.
28
Ndipo sadzakhalanso chakudya cha amitundu, ndi chilombo cha kuthengo sichidzawadyanso; koma adzakhala osatekeseka, opanda wina wakuwaopsa.
29
Ndipo ndidzawautsira mbeu yomveka, ndipo sadzachotsedwanso ndi njala m'dzikomo, kapena kusenzanso manyazi a amitundu.
30
Ndipo adzadziwa kuti Ine Yehova Mulungu wao ndili nao, ndi kuti iwo, nyumba ya Israele, ndiwo anthu anga, ati Ambuye Yehova.
31
Ndipo inu nkhosa zanga, nkhosa zapabusa panga, ndinu anthu, ndi Ine ndine Mulungu wanu, ati Ambuye Yehova.
← Chapter 33
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 37
Chapter 38
Chapter 39
Chapter 40
Chapter 41
Chapter 42
Chapter 43
Chapter 44
Chapter 45
Chapter 46
Chapter 47
Chapter 48
Chapter 35 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24
25
26
27
28
29
30
31
32
33
34
35
36
37
38
39
40
41
42
43
44
45
46
47
48