bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
/
Ezekiel 48
Ezekiel 48
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
← Chapter 47
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 37
Chapter 38
Chapter 39
Chapter 40
Chapter 41
Chapter 42
Chapter 43
Chapter 44
Chapter 45
Chapter 46
Chapter 47
Chapter 48
1
Maina a mafuko tsono ndi awa: Kuyambira nsonga ya kumpoto, ku mbali ya njira ya ku Hetiloni, polowera ku Hamati, Hazara-Enani ku malire a Damasiko kumpoto, ku mbali ya ku Hamati; ndi mbali zake zilinge kum'mawa ndi kumadzulo; Dani akhale nalo gawo limodzi.
2
Ndi m'malire a Dani, kuyambira mbali ya kum'mawa kufikira mbali ya kumadzulo; Asere, limodzi.
3
Ndi m'malire a Asere, kuyambira mbali ya kum'mawa kufikira mbali ya kumadzulo; Nafutali, limodzi.
4
Ndi m'malire a Nafutali, kuyambira mbali ya kum'mawa kufikira mbali ya kumadzulo; Manase, limodzi.
5
Ndi m'malire a Manase, kuyambira mbali ya kum'mawa kufikira mbali ya kumadzulo; Efuremu, limodzi.
6
Ndi m'malire a Efuremu, kuyambira mbali ya kum'mawa kufikira mbali ya kumadzulo; Rubeni, limodzi.
7
Ndi m'malire a Rubeni, kuyambira mbali ya kum'mawa kufikira mbali ya kumadzulo; Yuda, limodzi.
8
Ndi m'malire a Yuda, kuyambira mbali ya kum'mawa kufikira mbali ya kumadzulo, pakhale chopereka muchipereke, mikono zikwi makumi awiri mphambu zisanu kupingasa kwake, ndi m'litali mwake lilingane ndi magawo enawo, kuyambira mbali ya kum'mawa kufikira mbali ya kumadzulo; ndi malo opatulika akhale pakati pake.
9
Chopereka muchipereke kwa Yehova chikhale cha mikono zikwi makumi awiri mphambu zisanu m'litali mwake, ndi zikwi khumi kupingasa kwake.
10
Ndipo m'mwemo mudzakhala chopereka chopatulika cha ansembe kumpoto, mikono zikwi makumi awiri mphambu zisanu m'litali mwake, ndi kumadzulo mikono zikwi khumi kupingasa kwake, ndi kum'mawa mikono zikwi khumi kupingasa kwake, ndi kumwera mikono zikwi makumi awiri mphambu zisanu m'litali mwake; ndi pakati pake pakhale malo opatulika a Yehova.
11
Chidzakhala cha ansembe opatulidwa a ana a Zadoki, amene anasunga udikiro wanga osasokera, muja anasokera ana a Israele, ndi muja anasokera Alevi.
12
Ndi chiperekocho chikhale chao chotapa pa chopereka cha dziko, ndicho chopatulika kwambiri pa malire a Alevi.
13
Ndipo polingana ndi malire a ansembe Alevi akhale nalo gawo la mikono zikwi makumi awiri mphambu zisanu m'litali mwake, ndi mikono zikwi khumi kupingasa kwake; m'litali mwake monse ndimo mikono zikwi makumi awiri mphambu zisanu, ndi kupingasa kwake mikono zikwi khumi.
14
Ndipo asagulitseko, kapena kulisintha, kapena kupitiriza zipatso zoyamba za dziko; pakuti lili lopatulika la Yehova.
15
Ndipo zikwi zisanu zotsalazo m'kupingasa kwake, chakuno cha mikono zikwi makumi awiri mphambu zisanu, zikhale za ntchito wamba za mudzi, za kumangapo zapabusa; ndi mudzi ukhale pakati pake.
16
Ndi miyeso yake ndi iyi: mbali ya kumpoto, mikono zikwi zinai mphambu mazana asanu; ndi mbali ya kumwera, mikono zikwi zinai mphambu mazana asanu; ndi mbali ya kum'mawa, mikono zikwi zinai mphambu mazana asanu; ndi mbali ya kumadzulo, mikono zikwi zinai mphambu mazana asanu.
17
Ndipo mudziwo ukhale ndi busa lake; kumpoto mikono mazana awiri mphambu makumi asanu, kumwera mikono mazana awiri mphambu makumi asanu, ndi kum'mawa mikono mazana awiri mphambu makumi asanu, ndi kumadzulo mikono mazana awiri mphambu makumi asanu.
18
Ndipo madera otsalawo m'litali mwake alingane ndi chopereka chopatulika, ndicho mikono zikwi khumi kum'mawa, ndi mikono zikwi khumi kamadzulo, alingane ndi chopereka chopatulika; ndi zipatso zake zikhale za chakudya cha iwo ogwira ntchito m'mudzi.
19
Iwo ogwira ntchito m'mudzi mwa mafuko onse a Israele alimeko.
20
Chopereka chonse ndicho mikono zikwi makumi awiri mphambu zisanu m'litali mwake, mikono zikwi makumi awiri mphambu zisanu kupingasa kwake; muchipereke chopereka chopatulika chaphwamphwa, pamodzi ndi dziko la mudziwo.
21
Ndipo madera ena otsalawo ndiwo a kalonga, mbali ina ndi ina ya chopereka chopatulika ndi ya dziko la mudzi, kutsogolo kwa mikono zikwi makumi awiri mphambu zisanu za chopereka kumalire a kum'mawa, ndi kumadzulo kutsogolo kwa mikono zikwi makumi awiri mphambu zisanu kumalire a kumadzulo, pandunji pa magawo enawo ndiwo cha kalonga; ndipo chopereka chopatulika ndi malo opatulika a Kachisi zidzakhala pakati pake.
22
Kuyambira tsono dziko la Alevi kufikira dziko la mudzi, ndiwo a pakati pa magawo ake a kalonga, pakati pa malire a Yuda ndi malire a Benjamini, kukhale kwa kalonga.
23
Kunena za mafuko otsala tsono, kuyambira kumbali ya kum'mawa kufikira mbali ya kumadzulo, Benjamini akhale nalo gawo limodzi.
24
Ndi kumalire a Benjamini, kuyambira mbali ya kum'mawa kufikira mbali ya kumadzulo; Simeoni, gawo limodzi.
25
Ndi kumalire a Simeoni kuyambira mbali ya kum'mawa kufikira mbali ya kumadzulo; Isakara, limodzi.
26
Ndi kumalire a Isakara, kuyambira mbali ya kum'mawa kufikira mbali ya kumadzulo; Zebuloni, limodzi.
27
Ndi kumalire a Zebuloni, kuyambira kumbali ya kum'mawa kufikira mbali ya kumadzulo; Gadi, limodzi.
28
Ndi ku malire a Gadi, mbali ya kumwera, kuloza kumwera, malire akhale kuyambira ku Tamara kufikira ku madzi a Meribati-Kadesi, ku mtsinje wa Ejipito, kufikira ku Nyanja Yaikulu.
29
Ili ndi dziko muligawire mafuko a Israele ndi kuchita maere, likhale cholowa chao; ndipo awa ndi magawo ao, ati Ambuye Yehova.
30
Ndipo malekezero a mudzi ndi awa: mbali ya kumpoto ayese mikono zikwi zinai mphambu mazana asanu;
31
ndi zipata za mudzi zidzakhala monga mwa maina a mafuko a Israele; zipata zitatu kumpoto: chipata chimodzi cha Rubeni, chipata chimodzi cha Yuda, chipata chimodzi cha Levi;
32
ndi ku mbali ya kum'mawa zikwi zinai mphambu mazana asanu, ndi zipata zitatu: chipata chimodzi cha Yosefe, chipata chimodzi cha Benjamini, chipata chimodzi cha Dani;
33
ndi kumbali ya kumwera ayese mikono zikwi zinai mphambu mazana asanu, ndi zipata zitatu: chipata chimodzi cha Simeoni, chipata chimodzi cha Isakara, chipata chimodzi cha Zebuloni;
34
kumbali ya kumadzulo mikono zikwi zinai mphambu mazana asanu, ndi zipata zake zitatu: chipata cha Gadi, chipata chimodzi cha Asere, chipata chimodzi cha Nafutali.
35
Pozungulira pake ndipo mikono zikwi khumi mphambu zisanu ndi zitatu, ndi dzina la mudziwo kuyambira tsiku ilo lidzakhala, Yehova ali pomwepo.
← Chapter 47
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 37
Chapter 38
Chapter 39
Chapter 40
Chapter 41
Chapter 42
Chapter 43
Chapter 44
Chapter 45
Chapter 46
Chapter 47
Chapter 48
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24
25
26
27
28
29
30
31
32
33
34
35
36
37
38
39
40
41
42
43
44
45
46
47
48