bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
/
Ezekiel 4
Ezekiel 4
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
← Chapter 3
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 37
Chapter 38
Chapter 39
Chapter 40
Chapter 41
Chapter 42
Chapter 43
Chapter 44
Chapter 45
Chapter 46
Chapter 47
Chapter 48
Chapter 5 →
1
Ndipo iwe wobadwa ndi munthu, dzitengere njerwa, nuiike pamaso pako, nulembepo mudzi, ndiwo Yerusalemu;
2
nuuzinge, nuumangire nsanja zouzinga, nuundire nthumbira, ndi kuumangira misasa, nuuikire zogumulira pozungulira pake.
3
Nudzitengere chiwaya chachitsulo, ndi kuchiika ngati khoma lachitsulo pakati pa iwe ndi mudziwo; nuulozetsere nkhope yako kuti umangidwire misasa, ndipo udzamangira misasa. Ichi chikhale chizindikiro cha nyumba ya Israele.
4
Ndipo iwe ugonere pansi mbali yako ya kumanzere, nuikepo mphulupulu ya nyumba ya Israele; monga mwa kuwerenga kwa masiku amene udzagonapo udzasenza mphulupulu yao.
5
Ndipo Ine ndakuikira zaka za mphulupulu yao ngati masiku, ndiwo masiku mazana atatu mphambu makumi asanu ndi anai, kuti usenze mphulupulu ya nyumba ya Israele.
6
Ndipo utatsiriza awa, ugonerenso mbali yako ya kumanja, ndi kusenza mphulupulu ya nyumba ya Yuda; ndakuikira masiku makumi anai, kuliyesa tsiku limodzi ngati chaka chimodzi.
7
Ndipo ulozetse nkhope yako kuzingidwa kwake kwa Yerusalemu, ndi dzanja lako losafundika, nuunenere.
8
Ndipo taona ndidzakumanga ndi zingwe zolimba kuti usakunkhulire, mpaka watsiriza masiku a kuzingidwa kwako.
9
Udzitengerenso tirigu, ndi barele, ndi nyemba, ndi mphodza, ndi mapira, ndi mawere, nuziike m'mbale imodzi, ndi kudzipangira mkate nazo; uzidyako monga mwa kuwerenga kwa masiku udzagonawo pambali pako, ndiwo masiku mazana atatu mphambu makumi asanu ndi anai,
10
Ndipo chakudya chako uzichidya chiyesedwe masekeli makumi awiri tsiku limodzi; uzidyako tsiku ndi tsiku pa nthawi yake.
11
Uzimwanso madzi monga mwa muyeso, limodzi la magawo asanu ndi limodzi la hini; uzimwako tsiku ndi tsiku pa nthawi yake.
12
Ndipo uzichidya ngati timikate ta barele, ndi kutiocha pamaso pao ndi zonyansa za munthu.
13
Ndipo Yehova anati, Motero ana a Israele adzadya chakudya chao chodetsedwa, mwa amitundu kumene ndidzawaingitsirako.
14
Pamenepo ndinati, Ha, Ambuye Yehova! Taonani, moyo wanga sunadetsedwa, pakuti chiyambire ubwana wanga mpaka tsopano sindinadye chinthu chakufa chokha, kapena chogwidwa ndi chilombo; simunalowanso m'kamwa mwanga nyama yonyansa.
15
Ndipo anati kwa ine, Taona ndakuninkha ndowe ya ng'ombe m'malo mwa zonyansa za munthu, uotche mkate wako pamenepo.
16
Nanenanso nane, Wobadwa ndi munthu iwe, taona, ndidzathyola mchirikizo, ndiwo chakudya, m'Yerusalemu; ndipo adzadya chakudyacho monga mwa muyeso, ndi mosamalira, nadzamwa madzi monga mwa muyeso, ndi kudabwa;
17
kuti asowe chakudya ndi madzi, nasumwesumwe, naondetse mu mphulupulu zao.
← Chapter 3
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 37
Chapter 38
Chapter 39
Chapter 40
Chapter 41
Chapter 42
Chapter 43
Chapter 44
Chapter 45
Chapter 46
Chapter 47
Chapter 48
Chapter 5 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24
25
26
27
28
29
30
31
32
33
34
35
36
37
38
39
40
41
42
43
44
45
46
47
48