bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
/
Ezekiel 31
Ezekiel 31
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
← Chapter 30
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 37
Chapter 38
Chapter 39
Chapter 40
Chapter 41
Chapter 42
Chapter 43
Chapter 44
Chapter 45
Chapter 46
Chapter 47
Chapter 48
Chapter 32 →
1
Ndipo kunali chaka chakhumi ndi chimodzi, mwezi wachitatu, tsiku loyamba la mwezi, anandidzera mau a Yehova, akuti,
2
Wobadwa ndi munthu iwe, nena kwa Farao mfumu ya Aejipito ndi aunyinji ake, Ufanana ndi yani m'ukulu wako?
3
Taona, Asiriya anali mkungudza wa ku Lebanoni ndi nthambi zokoma zovalira, wautali msinkhu, kunsonga kwake ndi kumitambo.
4
Madzi anaumeretsa, chigumula chinaukulitsa, mitsinje yake inayenda, nizungulira munda wake, nipititsa michera yake kumitengo yonse ya kuthengoko.
5
Chifukwa chake msinkhu wake unaposa mitengo yonse ya kuthengo, ndi nthambi zake zinachuluka, ndi nthawi zake zinatalika, chifukwa cha madzi ambiri pophuka uwu.
6
Mbalame zonse za m'mlengalenga zinamanga zisa zao pa nthambi zake, ndi pansi pa nthawi zake zinaswana nyama zonse za kuthengo, ndi pa mthunzi wake inakhala mitundu yonse yaikulu ya anthu.
7
M'mwemo unakoma m'ukulu wake, m'kutalika kwa nthawi zake, popeza muzu wake unakhala kumadzi ambiri.
8
Mikungudza ya m'munda wa Mulungu siinathe kuubisa, milombwa siinanga nthambi zake, mifula siinanga nthawi zake; m'munda wa Mulungu munalibe mtengo wofanana nao kukoma kwake.
9
Ndinaupanga wokoma ndi nthawi zake zochuluka; ndi mitengo yonse ya m'Edeni inali m'munda wa Mulungu inachita nao nsanje.
10
Chifukwa chake atero Ambuye Yehova, Popeza mtengowo unakuza msinkhu wake, nufikitsa nsonga yake kumitambo, nukwezeka mtima wake m'kukula kwake,
11
ndidzaupereka m'dzanja la wamphamvu wa amitundu; iye adzachita naotu, Ine ndautaya mwa choipa chake.
12
Ndipo alendo oopsawo a amitundu anaulikhatu, nausiya; nthawi zake zidagwa pamapiri ndi m'zigwa zonse, ndi nthambi zake zinathyokera ku timitsinje tonse ta m'dziko; ndi mitundu yonse ya anthu a pa dziko lapansi inatsika kumthunzi wake, niusiya.
13
Pogwera pake padzakhala mbalame zonse za m'mlengalenga, ndi nyama zonse za kuthengo zidzakhala pa nthambi zake;
14
kuti mitengo iliyonse ya kumadzi isadzikuze chifukwa cha msinkhu wao, kapena kufikitsa nsonga zao pakati pa mitambo, ndi kuti amphamvu ao asaime m'kukula kwao, ndiwo onse akumwa madzi; pakuti onsewo aperekedwa kuimfa munsi mwake mwa dziko, pakati pa ana a anthu, pamodzi ndi iwo otsikira kumanda.
15
Atero Ambuye Yehova, Tsiku lija anatsikira kumanda ndinachititsa maliro, ndinamphimbira nyanja, ndinachepsa mitsinje yake, ndi madzi aakulu analetseka; ndipo ndinamdetsera Lebanoni, ndi mitengo yonse ya kuthengo inafota chifukwa cha uwo.
16
Ndinagwedeza amitundu ndi phokoso la kugwa kwake, muja ndinagwetsera kumanda, pamodzi ndi iwo otsikira kumanda; ndi mitengo yonse ya ku Edeni yosankhika, ndi yokometsetsa ya ku Lebanoni, yonse yakumwa madzi, inasangalala munsi mwake mwa dziko lapansi.
17
Iwonso anatsika naye kumanda kwa iwo ophedwa ndi lupanga, ndiwo amene adakhala dzanja lake okhala mumthunzi mwake pakati pa amitundu.
18
Momwemo ufanana ndi yani m'ulemerero ndi ukulu pakati pa mitengo ya Edeni? Koma udzatsitsidwa pamodzi ndi mitengo ya Edeni munsi mwake mwa dziko lapansi, udzagona pakati pa osadulidwa, pamodzi ndi iwo ophedwa ndi lupanga. Uwu ndi Farao ndi aunyinji ake onse, ati Ambuye Yehova.
← Chapter 30
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 37
Chapter 38
Chapter 39
Chapter 40
Chapter 41
Chapter 42
Chapter 43
Chapter 44
Chapter 45
Chapter 46
Chapter 47
Chapter 48
Chapter 32 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24
25
26
27
28
29
30
31
32
33
34
35
36
37
38
39
40
41
42
43
44
45
46
47
48