bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
/
Ezekiel 13
Ezekiel 13
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
← Chapter 12
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 37
Chapter 38
Chapter 39
Chapter 40
Chapter 41
Chapter 42
Chapter 43
Chapter 44
Chapter 45
Chapter 46
Chapter 47
Chapter 48
Chapter 14 →
1
Ndipo mau a Yehova anandidzera ine, akuti,
2
Wobadwa ndi munthu iwe, Unenere za aneneri a Israele onenerawo, nuziti nao onenera za m'mtima mwaomwao, Tamverani mau a Yehova.
3
Atero Ambuye Yehova, Tsoka aneneri opusawo akutsata mzimu waowao, chinkana sanaone kanthu.
4
Aneneri ako, Israele, akhala ngati nkhandwe m'mapululu.
5
Simunakwera kuima mopasuka, kapena kumanganso linga la nyumba ya Israele, kuima kunkhondo tsiku la Yehova.
6
Iwo aona zopanda pake, ndi phenda labodza amene anena, Atero Yehova; koma Yehova sanawatume, nayembekezetsa anthu kuti mauwo adzakhazikika.
7
Simunaona masomphenya opanda pake kodi? Simunanena ula wabodza kodi? Pakunena inu, Atero Yehova; chinkana sindinanena?
8
Chifukwa chake atero Ambuye Yehova, Popeza mwanena zopanda pake, ndi kuona mabodza, chifukwa chake taonani, ndikhala Ine wotsutsana nanu, ati Ambuye Yehova.
9
Ndi dzanja langa lidzakhala lotsutsana nao aneneri akuona zopanda pake, ndi kupenda za bodza; sadzakhala mu msonkhano wa anthu anga, kapena kulembedwa m'buku lolembedwamo nyumba ya Israele; ndipo mudzadziwa kuti Ine ndine Ambuye Yehova.
10
Popeza, inde popeza asokeretsa anthu anga, ndi kuti, Mtendere, pokhala palibe mtendere; ndipo anthu akamanga linga, aneneriwo alimata ndi dothi losapondeka;
11
uziti nao olimata ndi dothi losapondeka, kuti lidzagwa, lidzavumbidwa ndi mvula yaikulu; ndi inu, matalala akulu, mudzagwa; ndi mkuntho udzalithithimula.
12
Ndipo taonani, litagwa linga, sadzanena nanu kodi, Lili kuti dothi munalimata nalo?
13
Chifukwa chake atero Ambuye Yehova, Ndidzalithithimula ndi mkuntho m'ukali wanga; ndipo lidzavumbidwa ndi mvula yaikulu mu mkwiyo wanga, ndi matalala akulu adzalitha m'ukali wanga.
14
M'mwemo ndidzagumula linga munalimata ndi dothi losapondeka, ndi kuligwetsa pansi; kuti maziko ake agadabuke, ndipo lidzagwa; ndi inu mudzathedwa pakati pake; ndipo mudzadziwa kuti Ine ndine Yehova.
15
M'mwemo ndidzakwaniritsa ukali wanga pa lingalo, ndi pa iwo analimata ndi dothi losapondeka, ndipo ndidzati kwa inu, Lingalo palibe, ndi olimata palibe,
16
ndiwo aneneri a Israele akunenera za Yerusalemu, nauonera masomphenya a mtendere, pamene palibe mtendere, ati Ambuye Yehova.
17
Ndipo iwe wobadwa ndi munthu, uziika nkhope yako itsutsane nao ana akazi a anthu ako, akunenera za m'mtima mwao, nunenere chowatsutsa,
18
nuziti, Atero Ambuye Yehova, Tsoka akazi osoka zophimbira mfundo zonse za dzanja, ndi iwo okonza zokuta mitu za misinkhu iliyonse, kuti asake miyoyo! Kodi musaka miyoyo ya anthu anga ndi kudzisungira miyoyo yanu?
19
Ndipo mundidetsa mwa anthu anga kulandirapo barele wodzala manja, ndi zidutsu za mkate, kuipha miyoyo yosayenera kufa, ndi kusunga miyoyo yosayenera kukhala ndi moyo, ndi kunena mabodza kwa anthu anga omvera bodza.
20
Chifukwa chake atero Ambuye Yehova, Taonani, nditsutsana nazo zophimbira zanu, zimene musaka nazo miyoyo komweko, kuiuluza; ndipo ndidzazikwatula m'manja mwanu, ndi kuimasula, ndiyo miyoyo muisaka kuiuluza.
21
Zokuta mitu zanu zomwe ndidzazing'amba, ndi kulanditsa anthu anga m'manja mwanu; ndipo sadzakhalanso m'mphamvu mwanu kusakidwa; ndipo mudzadziwa kuti Ine ndine Yehova.
22
Popeza mwamvetsa chisoni ndi mabodza mtima wa wolungama, amene sindinamvetsa chisoni Ine, ndi kumlimbitsa manja woipa, kuti asabwerere kuleka njira yake yoipa, ndi kusungidwa wamoyo;
23
chifukwa chake simudzaonanso zopanda pake, kapena kupenda; koma ndidzalanditsa anthu anga m'manja mwanu; ndipo mudzadziwa kuti Ine ndine Yehova.
← Chapter 12
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 37
Chapter 38
Chapter 39
Chapter 40
Chapter 41
Chapter 42
Chapter 43
Chapter 44
Chapter 45
Chapter 46
Chapter 47
Chapter 48
Chapter 14 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24
25
26
27
28
29
30
31
32
33
34
35
36
37
38
39
40
41
42
43
44
45
46
47
48