bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
/
Ezekiel 12
Ezekiel 12
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
← Chapter 11
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 37
Chapter 38
Chapter 39
Chapter 40
Chapter 41
Chapter 42
Chapter 43
Chapter 44
Chapter 45
Chapter 46
Chapter 47
Chapter 48
Chapter 13 →
1
Mau a Yehova anandidzeranso, ndi kuti,
2
Wobadwa ndi munthu iwe, ukhala pakati pa nyumba yampanduko, yokhala nao maso akuonera, koma osaona; ndi makutu akumvera, koma osamva; pakuti iwo ndiwo nyumba yampanduko.
3
Potero wobadwa ndi munthu iwe, udzikonzeretu akatundu a pa ulendo wa kundende, nuchoke usana pamaso pao, uchoke pokhala iwepo kunka malo ena pamaso pao; kapena adzachizindikira, angakhale ndiwo nyumba yopanduka.
4
Uzitulutsa akatundu ako usana pamaso pao, ngati a pa ulendo wa kundende; ndipo madzulo uzituluka wekha pamaso pao, monga amatuluka olowa kundende.
5
Udziboolere khoma pamaso pao, nuwatulutsire akatundu pamenepo.
6
Pamaso pao uwasenze paphewa pako, ndi kuwatulutsa kuli mdima, nuphimbe nkhope yako kuti usapenye dziko; popeza ndakuika chizindikiro cha nyumba ya Israele.
7
Ndipo ndinachita monga momwe anandilamulira, ndinatulutsa akatundu anga usana, ngati a pa ulendo wa kundende, ndi madzulo ndinaboola pakhoma ndi dzanja langa, ndinawatulutsa pali mdima, ndi kuwasenza paphewa panga pamaso pao.
8
Ndipo m'mawa mau a Yehova anandidzera, ndi kuti,
9
Wobadwa ndi munthu iwe, kodi nyumba ya Israele, nyumba yampanduko, siinati kwa iwe, Uchitanji?
10
Unene nao, Atero Ambuye Yehova, Katundu uyu anena za kalonga wa m'Yerusalemu, ndi nyumba yonse ya Israele yokhala pakati pao.
11
Uziti, Ine ndine chizindikiro chanu, monga ndachita ine momwemo kudzachitidwa nao; adzachotsedwa kunka kundende.
12
Kalongayo ali pakati pao adzasenza paphewa pake mumdima, nadzatuluka; adzaboola palinga, nadzatulutsapo; adzaphimba nkhope yake kuti asapenye dziko ndi maso ake.
13
Ndidzamphimba ndi ukonde wanga, nadzakodwa iye mu msampha wanga; ndipo ndidzafika naye ku Babiloni, ku dziko la Ababiloni; sadzaliona, chinkana adzafako.
14
Ndipo onse omzinga kumthandiza, ndi magulu ake onse, ndidzawamwaza kumphepo zonse, ndidzawasololeranso lupanga lakuwatsata.
15
Motero adzadziwa kuti Ine ndine Yehova, pakuwamwaza Ine mwa amitundu, ndi kuwabalalitsa m'maiko.
16
Koma ndidzawasiya owerengeka apulumuke lupanga, ndi njala, ndi mliri, kuti afotokoze zonyansa zao kwa amitundu kumene afikako; ndipo adzadziwa kuti Ine ndine Yehova.
17
Anandidzeranso mau a Yehova, akuti,
18
Wobadwa ndi munthu iwe, udye mkate wako ndi kunthunthumira, ndi kumwa madzi ako ndi kunjenjemera, ndi kutenga nkhawa;
19
nunene kwa anthu a m'dziko, Atero Yehova Mulungu za iwo okhala m'Yerusalemu, ndi za dziko la Israele, Adzadya mkate wao ndi nkhawa, ndi kumwa madzi ao ndi kusumwa; pakuti dziko lao lidzakhala lachipululu, kuleka kudzala kwake chifukwa cha chiwawa cha onse okhalamo.
20
Ndi midzi yokhalamo anthu idzapasuka, ndi dziko lidzakhala labwinja; ndipo mudzadziwa kuti Ine ndine Yehova.
21
Ndipo anandidzera mau a Yehova, akuti,
22
Wobadwa ndi munthu iwe, ngwotani mwambi umene muli nao m'dziko la Israele, wakuti, Masiku achuluka, ndi masomphenya ali onse apita pachabe?
23
Chifukwa chake unene nao, Atero Yehova Mulungu, Ndidzaleketsa mwambi uwu, ndipo sadzautchulanso mwambi m'Israele; koma unene nao, Masiku ayandikira, nadzachitika masomphenya ali onse.
24
Pakuti sikudzakhalanso masomphenya achabe, kapena ula wosyasyalika m'nyumba ya Israele.
25
Pakuti Ine ndine Yehova, ndidzanena, ndi mau ndidzanenawo adzachitika, osazengerezekanso; pakuti m'masiku anu, nyumba yopanduka inu, ndidzanena mau ndi kuwachita, ati Yehova Mulungu.
26
Anandidzeranso mau a Yehova, akuti,
27
Wobadwa ndi munthu iwe, taona, iwo a nyumba ya Israele akuti, masomphenya awaona ndiwo a masiku ambiri; ndipo anenera za nthawi zili kutali.
28
Chifukwa chake uziti nao, Atero Ambuye Yehova, Palibe amodzi a mau anga adzazengerezekanso; koma mau ndidzanenawo adzachitika, ati Ambuye Yehova.
← Chapter 11
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 37
Chapter 38
Chapter 39
Chapter 40
Chapter 41
Chapter 42
Chapter 43
Chapter 44
Chapter 45
Chapter 46
Chapter 47
Chapter 48
Chapter 13 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24
25
26
27
28
29
30
31
32
33
34
35
36
37
38
39
40
41
42
43
44
45
46
47
48