bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
/
Ezekiel 27
Ezekiel 27
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
← Chapter 26
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 37
Chapter 38
Chapter 39
Chapter 40
Chapter 41
Chapter 42
Chapter 43
Chapter 44
Chapter 45
Chapter 46
Chapter 47
Chapter 48
Chapter 28 →
1
Anandidzeranso mau a Yehova, akuti,
2
Ndipo iwe wobadwa ndi munthu, Takwezera Tiro nyimbo ya maliro;
3
nuti kwa Tiro, Iwe wakukhala polowera m'nyanja, wakuchita malonda ndi mitundu ya anthu m'zisumbu zambiri, atero Ambuye Yehova, Iwe, Tiro, wati, Ine ndine wokongola wangwiro.
4
M'mphepete mwako muli m'kati mwa nyanja, iwo anakumanga iwe anakonza kukongola kwako kukhale kwangwiro.
5
Anacheka matabwa ako onse amlombwa wa ku Seniri, anatenga mikungudza ya ku Lebanoni kukupangira milongoti.
6
Anasema nkhafi zako za thundu wa ku Basani, anapanga mipando yako yamnyanga, woika mu mtengo wanaphini wochokera ku zisumbu za Kitimu.
7
Thanga lako ndi labafuta wopikapika wa ku Ejipito, likhale ngati mbendera yako; chophimba chako ndicho nsalu yamadzi ndi yofiirira zochokera ku zisumbu za Elisa.
8
Okhala m'Sidoni ndi Arivadi ndiwo opalasa ako; anzeru ako, Tiro, okhala mwa iwe, ndiwo oongolera ako.
9
Akulu a ku Gebala ndi eni luso ake anali mwa iwe kukonza ziboo zako; zombo zonse za kunyanja pamodzi ndi amalinyero ao anali mwa iwe kusinthana nawe malonda.
10
Apersiya, Aludi, Aputi, anali m'khamu lako; anthu ako a nkhondo anapachika chikopa ndi chisoti mwa iwe, anamveketsa kukoma kwako.
11
Anthu a Arivadi pamodzi ndi ankhondo ako anali pa malinga ako pozungulira, ndi Agamadi anali mu nsanja zako; anapachika zikopa zao pa makoma ako pozungulira, anakwaniritsa kukoma kwako.
12
Tarisisi anagulana nawe malonda m'kuchuluka kwa chuma chilichonse; anagula malonda ako ndi siliva ndi chitsulo, seta ndi ntovu.
13
Yavani, Tubala, Meseki, anagulana nawe malonda; ndi anthu amoyo ndi zotengera zamkuwa anagulana nawe malonda.
14
Iwo a nyumba ya Togarima anagula malonda ako ndi akavalo, ndi akavalo a nkhondo, ndi nyuru.
15
Anthu a ku Dedani anakutsatsa malonda, zisumbu zambiri zinazolowerana nawe malonda ako, anabwera nazo minyanga ndi phingo kugulana nawe malonda.
16
Aramu anachita nawe malonda chifukwa cha zambirizo udazipanga, anagula malonda ako ndi smaragido, nsalu yofiirira, ndi yopikapika, ndi bafuta, ndi korale, ndi ngale.
17
Yuda ndi dziko la Israele anagulana nawe malonda, anagula malonda ako ndi tirigu wa ku Miniti, ndi zozuna, ndi uchi, ndi mafuta, ndi mafuta amankhwala.
18
Damasiko anagulana nawe malonda chifukwa cha zambirizo udazipanga, chifukwa cha kuchuluka kwa chuma chilichonse, ndi vinyo wa ku Heliboni, ndi ubweya wa nkhosa woyera.
19
Vedani ndi Yavani anagula malonda ako ndi thonje, unagulana nao chitsulo chosalala, ngaho, ndi nzimbe.
20
Dedani anagulana nawe malonda ndi nsalu za mtengo wake zoyenda nazo pa kavalo.
21
Arabiya ndi akalonga onse a ku Kedara anazolowerana nao malonda ako; anaankhosa, nkhosa zamphongo, ndi mbuzi, izi anagulana nawe.
22
Amalonda a ku Sheba ndi a ku Raama anagulana nawe malonda; anagula malonda ako ndi zonunkhira zoposa zilizonse, ndi miyala iliyonse ya mtengo wake, ndi golide.
23
Harani ndi Kane ndi Edeni, amalonda a ku Sheba Asiriya ndi Kilimadi, anagulana nawe malonda.
24
Awa anagulana nawe malonda ndi zovala zosankhika, ndi mitumba ya nsalu zofiirira ndi zopikapika, ndi chuma cha thonje lopotapota, ndi zingwe zopota zolimba za malonda ako.
25
Zombo za ku Tarisisi ndizo amtengatenga a malonda ako; ndipo unadzadzidwa ndi chuma ndi ulemu waukulu pakati pa nyanja.
26
Opalasa ako anakufikitsa kumadzi aakulu; mphepo ya kum'mawa inakuthyola m'kati mwa nyanja.
27
Chuma chako, zako zogulana nazo malonda ako, amalinyero ako, ndi oongolera ako, amisiri ako, ndi ogulitsa malonda ako, ndi ankhondo ako onse okhala mwa iwe, pamodzi ndi msonkhano wonse uli pakati pa iwe, adzagwa m'kati mwa nyanja tsiku la kugwa kwako.
28
Pakumveka mfuu wa oongolera ako mabwalo ako adzagwedezeka.
29
Ndi onse ogwira nkhafi, amalinyero, ndi oongolera onse a kunyanja, adzatsika kuzombo zao, nadzaima pamtunda,
30
nadzamveketsa mau ao pa iwe, nadzalira mowawa mtima, nadzathira fumbi pamitu pao, nadzakunkhulira m'maphulusa,
31
nadzameta mpala chifukwa cha iwe, nadzadzimangira ziguduli m'chuuno, nadzakulirira ndi mtima wowawa maliro owawa.
32
Ndipo pakulira adzakukwezera nyimbo ya maliro, ndi kukulirira, ndi kuti, Wakunga Tiro ndani, wakunga uyu waonongeka pakati pa nyanja?
33
Pakutuluka malonda ako m'nyanja unadzaza mitundu yambiri ya anthu, unalemeretsa mafumu a pa dziko lapansi ndi chuma chako chochuluka ndi malonda ako.
34
Muja unathyoka ndi nyanja m'madzi akuya malonda ako ndi msonkhano wako wonse adagwa pakati pako.
35
Onse okhala pa zisumbu adagwa nawe, ndi mafumu ao aopsedwa kwambiri, zikhululuka nkhope zao.
36
Amalonda mwa mitundu ya anthu akunyodola, wakhala choopsetsa iwe, ndipo sudzakhalanso konse.
← Chapter 26
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 37
Chapter 38
Chapter 39
Chapter 40
Chapter 41
Chapter 42
Chapter 43
Chapter 44
Chapter 45
Chapter 46
Chapter 47
Chapter 48
Chapter 28 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24
25
26
27
28
29
30
31
32
33
34
35
36
37
38
39
40
41
42
43
44
45
46
47
48