bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
/
Ezekiel 11
Ezekiel 11
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
← Chapter 10
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 37
Chapter 38
Chapter 39
Chapter 40
Chapter 41
Chapter 42
Chapter 43
Chapter 44
Chapter 45
Chapter 46
Chapter 47
Chapter 48
Chapter 12 →
1
Pamenepo unandikweza mzimu, nudza nane kuchipata cha kum'mawa cha nyumba ya Yehova choloza kum'mawa; ndipo taonani, pa chitseko cha chipata amuna makumi awiri mphambu asanu; ndipo ndinaona pakati pao Yazaniya mwana wa Azuri ndi Pelatiya mwana wa Benaya, akalonga a anthu.
2
Ndipo anati kwa ine, Wobadwa ndi munthu iwe, awa ndi anthu olingirira za mphulupulu, ndi kupangira uphungu woipa m'mudzi muno;
3
ndiwo akuti, siinafike nyengo yakumanga nyumba; mudzi uwu ndi mphika, ife ndife nyama.
4
Chifukwa chake uwanenere, neneratu, wobadwa ndi munthu iwe.
5
Pamenepo mzimu wa Yehova unandigwera, ndipo anati kwa ine, Nena, Atero Yehova, Mwatero nyumba ya Israele, pakuti ndidziwa zimene zimalowa m'mtima mwanu.
6
Mwachulukitsa ophedwa anu m'mudzi muno, mwadzazanso makwalala ake ndi ophedwawo.
7
Chifukwa chake atero Yehova Mulungu, Ophedwa anu munawaika m'kati mwake, iwo ndiwo nyama imene, ndi mudzi uwu ndiwo mphika; koma inu mudzatulutsidwa m'kati mwake.
8
Mwaopa lupanga, tsono ndidzakufikitsirani lupanga, ati Yehova Mulungu.
9
Ndipo ndidzakutulutsani m'kati mwake, ndi kukuperekani m'manja a alendo, ndi kuchita maweruzo pakati panu.
10
Mudzagwa ndi lupanga, ndidzakuweruzirani kumalire a Israele; ndipo mudzadziwa kuti Ine ndine Yehova.
11
Mudzi uno sudzakhala mphika wanu, ndi inu simudzakhala nyama m'kati mwake, ndidzakuweruzirani kumalire a Israele;
12
ndipo mudzadziwa kuti Ine ndine Yehova, pakuti simunayenda m'malemba anga, kapena kuchita maweruzo anga, koma mwachita monga mwa maweruzo a amitundu okhala pozungulira panu.
13
Ndipo kunali, pakunenera ine, anamwalira Pelatiya mwana wa Benaya. Pamenepo ndinagwa nkhope yanga pansi, ndi kufuula ndi mau akulu, ndi kuti, Kalanga ine, Yehova Mulungu? Mudzatsiriza kodi otsala a Israele?
14
Ndipo mau a Yehova anandidzera kuti,
15
Wobadwa ndi munthu iwe, abale ako, inde abale ako amuna a chibale chako, ndi nyumba yonse ya Israele, yonseyi ndiwo amene okhala m'Yerusalemu ananena nao, Muzikhala kutali kwa Yehova; dziko ili lapatsidwa kwa ife, likhale cholowa chathu;
16
chifukwa chake uziti, Atero Yehova Mulungu, Ngakhale ndawachotsa kutali mwa amitundu, ngakhalenso ndawabalalikitsa m'maiko, koma ndidzawakhalira malo opatulika kanthawi kumaiko adafikako.
17
Chifukwa chake uziti, Atero Yehova Mulungu, Ndidzakumemezani kumitundu ya anthu, ndi kukusonkhanitsani muchoke m'maiko m'mene munabalalikiramo, ndipo ndidzakuninkhani dziko la Israele.
18
Ndipo adzafikako, nadzachotsako zonyansa zake zonse, ndi zake zonse zakuipitsamo.
19
Ndipo ndidzawapatsa mtima umodzi, ndi kuika mzimu watsopano m'kati mwao; ndipo ndidzawachotsera mtima wamwala m'thupi mwao, ndi kuwapatsa mtima wamnofu;
20
kuti ayende m'malemba anga, ndi kusunga maweruzo anga, ndi kuwachita; ndipo adzakhala anthu anga, ndi Ine ndidzakhala Mulungu wao.
21
Koma iwo amene mtima wao unatsata mtima wa zonyansa zao, ndi zoipitsitsa zao, ndidzawabwezera njira yao pamtu pao, ati Yehova Mulungu.
22
Pamenepo akerubi anatambasula mapiko ao, ndi njinga zinali pa mbali pao; ndi ulemerero wa Mulungu wa Israele unali pamwamba pao.
23
Ndipo ulemerero wa Yehova unakwera kuchoka pakati pa mudzi, nuima pa phiri la kum'mawa kwa mudzi.
24
Ndipo mzimu unandikweza, nufika nane m'masomphenya mwa mzimu wa Mulungu kudziko la Ababiloni, kwa andendewo. M'mwemo masomphenya ndidawaona anandichokera, nakwera.
25
Pamenepo ndinanena ndi andendewo zonse zija adandionetsa Yehova.
← Chapter 10
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 37
Chapter 38
Chapter 39
Chapter 40
Chapter 41
Chapter 42
Chapter 43
Chapter 44
Chapter 45
Chapter 46
Chapter 47
Chapter 48
Chapter 12 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24
25
26
27
28
29
30
31
32
33
34
35
36
37
38
39
40
41
42
43
44
45
46
47
48