bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
/
Ezekiel 28
Ezekiel 28
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
← Chapter 27
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 37
Chapter 38
Chapter 39
Chapter 40
Chapter 41
Chapter 42
Chapter 43
Chapter 44
Chapter 45
Chapter 46
Chapter 47
Chapter 48
Chapter 29 →
1
Ndipo anandidzera mau a Yehova, akuti,
2
Wobadwa ndi munthu iwe, uziti kwa kalonga wa Tiro, Atero Ambuye Yehova, Popeza mtima wako wadzikweza, nuti, Ine ndine Mulungu, ndikhala pa mpando wa Mulungu pakati pa nyanja, ungakhale uli munthu, wosati Mulungu, ungakhale waika mtima wako ngati mtima wa Mulungu,
3
taona, ndiwe wanzeru woposa Daniele, palibe chinsinsi angakubisire;
4
mwa nzeru zako ndi luntha lako wadzionerera chuma, wadzionereranso golide ndi siliva mwa chuma chako;
5
mwa nzeru zako zazikulu ndi kugulana malonda kwako wachulukitsa chuma chako, ndi mtima wako wadzikuza chifukwa cha chuma chako;
6
chifukwa chake atero Ambuye Yehova, Popeza waika mtima wako ngati mtima wa Mulungu;
7
chifukwa chake taona ndidzakufikitsira alendo oopsa a mitundu ya anthu, iwo adzasololera malupanga ao nzeru zako zokongola, nadzaipsa kunyezimira kwako.
8
Adzakutsitsira kumanda, nudzafa mafedwe a ophedwa m'kati mwa nyanja.
9
Kodi udzanena ndithu pamaso pa iye wakupha iwe, Ine ndine Mulungu, pokhala uli munthu, wosati Mulungu, m'dzanja la iye wakupha iwe.
10
Udzafa mafedwe a osadulidwa ndi dzanja la alendo, pakuti ndachinena, ati Ambuye Yehova.
11
Nandidzeranso mau a Yehova, akuti,
12
Wobadwa ndi munthu iwe, kweza nyimbo ya maliro yolirira mfumu ya Tiro, nuziti kwa iye, Atero Ambuye Yehova, Wakomera muyeso ndi chizindikiro, wodzala ndi nzeru wokongola wangwiro.
13
Unali m'Edeni, munda wa Mulungu, mwala uliwonse wa mtengo wake unali chofunda chako, sardiyo, topazi, diamondi, berulo, sohamu, ndi yaspi, safiro, nofeki, bareketi, ndi golide; malingaka ako ndi akazi ako anakutumikira tsiku lolengedwa iwe zinakonzekeratu.
14
Unali kerubi wodzozedwa wakuphimba, ndipo ndinakuika unali pa phiri lopatulika la Mulungu, anayendayenda pakati pa miyala yamoto.
15
Unali wangwiro m'njira zako chilengedwere iwe, mpaka chinapezeka mwa iwe chosalungama.
16
Mwa kuchuluka kwa malonda ako anakudzaza m'kati mwako ndi chiwawa, ndipo unachimwa; chifukwa chake ndinakukankha kukuchotsa pa phiri la Mulungu; ndipo ndinakuononga, kerubi wakuphimba iwe, kukuchotsa pakati pa miyala yamoto.
17
Unadzikuza mtima chifukwa cha kukongola kwako, waipsa nzeru zako; chifukwa cha kuwala kwako ndakugwetsa pansi, ndakuika pamaso pa mafumu, kuti akupenye.
18
Mwa mphulupulu zako zochuluka ndi malonda ako osalungama waipsa malo ako opatulika; chifukwa chake ndatulutsa moto m'kati mwako wakunyeketsa iwe; ndipo ndakusandutsa mapulusa panthaka pamaso pa onse akuona.
19
Onse akudziwa iwe mwa mitundu ya anthu adzadabwa nawe; wasanduka choopsa, ndipo sudzakhalanso konse.
20
Anandidzeranso mau a Yehova, akuti,
21
Wobadwa ndi munthu iwe, lozetsa nkhope yako ku Sidoni, nuunenere;
22
uziti, Atero Ambuye Yehova, Taona, nditsutsana nawe Sidoni, ndipo ndidzalemekezedwa pakati pako; ndipo adzadziwa kuti Ine ndine Yehova pakuchita Ine maweruzo mwa uwu, ndi kuzindikiridwa Woyera mwa uwu.
23
Pakuti ndidzatumiza mliri ndi mwazi ilowe m'makwalala ake, ndi olasidwa adzagwa m'kati mwake ndi lupanga lougwera pozungulira ponse; motero adzadziwa kuti Ine ndine Yehova.
24
Ndipo nyumba ya Israele siidzakhalanso nayo mitungwi yolasa, kapena minga yaululu ya aliyense wakuizinga ndi kuipeputsa; motero adzadziwa kuti Ine ndine Ambuye Yehova.
25
Atero Ambuye Yehova, Pakusonkhanitsa nyumba ya Israele mwa mitundu ya anthu anabalalikamo, ndidzazindikirika Woyera mwaiwowa, pamaso pa amitundu; ndipo adzakhala m'dziko mwaomwao ndinalipereka kwa Yakobo mtumiki wanga.
26
Nadzakhalamo osatekeseka, nadzamanga nyumba, ndi kuoka mpesa m'mindamo, nadzakhalamo mosatekeseka, ndikatha kukwaniritsira maweruzo pa onse akuwapeputsa pozungulira pao; motero adzadziwa kuti Ine ndine Yehova Mulungu wao.
← Chapter 27
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 37
Chapter 38
Chapter 39
Chapter 40
Chapter 41
Chapter 42
Chapter 43
Chapter 44
Chapter 45
Chapter 46
Chapter 47
Chapter 48
Chapter 29 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24
25
26
27
28
29
30
31
32
33
34
35
36
37
38
39
40
41
42
43
44
45
46
47
48