bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
2 Samuel 1
2 Samuel 1
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 2 →
1
Saulo atamwalira, Davide adabwerako kumene adaakagonjetsa Aamaleke kuja, ndipo adakakhala ku Zikilagi masiku aŵiri.
2
Tsono pa tsiku lachitatu lake, adangoona munthu akuchokera ku zithando zankhondo za Saulo, atavala zovala zong'ambika ndiponso atadzithira dothi kumutu. Munthuyo atafika kwa Davide, adadzigwetsa pansi, namlambira.
3
Davide adamufunsa kuti, “Ukuchokera kuti?” Iye adayankha kuti, “Ndathaŵa ku zithando zankhondo za Aisraele.”
4
Davide adamufunsanso kuti, “Zinthu zidayenda bwanji? Tandiwuza.” Iye adati, “Anthu athaŵa kunkhondoko, ndipo ambirinso aphedwa. Saulo ndi mwana wake Yonatani, nawonso aphedwa.”
5
Apo Davide adamufunsa mnyamatayo kuti, “Iwe wadziŵa bwanji kuti Saulo ndi Yonatani nawonso adafa?”
6
Mnyamata wodzanena uja adati, “Zidangochitika kuti ndinali pa phiri la Gilibowa. Kumeneko ndidaona Saulo atangoti zyoli ku mkondo wake. Nthaŵi imeneyo nkuti magaleta ankhondo, ndiponso adani okwera pa akavalo atamuyandikira Sauloyo.
7
Tsono Saulo atacheuka nandiwona, adandiitana. Ndidavomera kuti, ‘Ŵaŵa.’
8
Adandifunsa kuti, ‘Ndiwe yani?’ Ine ndidati, ‘Ndine Mwamaleke.’
9
Apo adandiwuza kuti, ‘Bwera pafupi, undiphe, chifukwa ndikumva ululu woopsa, komabe ndikali moyo.’
10
Choncho ndidasendera pafupi, nkumupha, poti ndidaadziŵa kuti akagwa, sakhala moyo. Tsono ndidamuvula chisoti chaufumu kumutu kwake ndi chigwinjiri kumkono kwake, ndipo ndabwera nazo kuno kwa inu mbuyanga.”
11
Apo Davide adang'amba zovala zake. Nawonso anthu amene anali naye adachita chimodzimodzi.
12
Ndipo anthuwo adabuma maliro. Adalira ndi kusala zakudya mpaka madzulo chifukwa cha Saulo ndi Yonatani mwana wake. Adaliranso chifukwa cha Aisraele, anthu a Chauta, chifukwa choti anali ataphedwa ku nkhondo.
13
Tsono Davide adafunsa mnyamata wodzanena uja kuti, “Kodi iwe ndiwe wa kuti?” Iye adati, “Munthune ndine mwana wa mlendo, Mwamaleke.”
14
Davide adamufunsanso kuti, “Nanga iwe sudachite mantha bwanji kutambalitsa dzanja lako nkupha wodzozedwa wa Chauta?”
15
Pomwepo Davide adaitana mmodzi mwa ankhondo ake, namuuza kuti, “Mtenge ameneyu, ukamuphe.” Wankhondoyo adamkanthadi naafa.
16
Ndipo Davide adati, “Wadziphetsa wekha, unanena wekha ndi pakamwa pako kuti, ‘Ndidapha wodzozedwa wa Chauta.’ ”
17
Choncho Davide adaimba nyimbo ya madandaulo, kulira Saulo ndi Yonatani mwana wake.
18
Ndipo adalamula kuti mau a madandaulowo aŵaphunzitse kwa anthu a ku Yuda. Mau ake ndi aŵa, monga adalembedwera m'buku la Yasara.
19
“Ulemerero wako wathera zitunda zako zachipembedzo, iwe Israele. Ha! Kani amphamvu agwa motere!
20
Musakanene zimenezi ku Gati, musakalengeze m'miseu ya ku Asikeloni, kuti akazi a Afilisti angasekerere, akazi a anthu osaumbalidwa angakondwe.
21
“Inu mapiri a ku Gilibowa, pa inu pasagwe mame ndi mvula, pa inu pasapezeke minda yobereka dzinthu. Paja kumeneko adani adanyoza chishango cha munthu wamphamvu, chishango cha Saulo, chosapukutidwapo ndi mafuta.
22
“Uta wa Yonatani sudabwereko chabe osakhetsa magazi a anthu osabayako ankhondo amphamvu. Ndipo lupanga la Saulo silidabwereko chabe osapha anthu.
23
“Saulo ndi Yonatani pa moyo wao anali okondedwa ndi okondwetsa, ndipo sadalekane ali moyo ngakhale pa imfa. Anali ndi liŵiro loposa la ziwombankhanga. Anali amphamvu kuposa mikango.
24
“Inu akazi a ku Israele, mlireni Saulo. Chifukwa cha iye uja munkavala zovala zabwino zofiira, ndiponso munkaika zokometsera zagolide pa zovala zanu.
25
“Ha! Kani amphamvu agwa motere! Yonatani ali gone, atafa pa zitunda zako zachipembedzo.
26
“Mbale wanga Yonatani, ndikuvutika mu mtima chifukwa cha iwe, wakhala wapamtima wanga. Chikondi chako pa ine chinali chodabwitsa kwambiri, chinali choposa ngakhale chikondi cha akazi.
27
“Ha! Kani amphamvu agwa motere, zida zao zankhondo nkuwonongeka!”
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 2 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24