bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
2 Samuel 6
2 Samuel 6
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
← Chapter 5
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 7 →
1
Davide adasonkhanitsanso ankhondo okwanira 30,000, amene adaŵasankha pakati pa Aisraele.
2
Adanyamuka, napita pamodzi ndi ankhondo onse amene anali naye kuchokera ku Baala wa ku Yuda kuti akatenge Bokosi lachipangano la Chauta. Bokosilo limadziwika ndi dzina la Chauta Wamphamvuzonse, amene amakhala pa akerubi ngati pa mpando waufumu.
3
Anthuwo adatulutsa Bokosi lachipanganolo m'nyumba ya Abinadabu, imene inali pa phiri, nalinyamula pa ngolo yatsopano. Tsono Uza ndi Ahiyo, ana a Abinadabu, ndiwo ankayendetsa ngolo yatsopanoyo
4
imene idaanyamula Bokosi lachipanganolo kuchoka nalo ku nyumba ya Abinadabu ija ku phiri. Ahiyo ankayenda patsogolo pa Bokosi.
5
Tsono Davide pamodzi ndi Aisraele onse ankakondwerera kwambiri kulemekeza Chauta poimba ndi mphamvu zao zonse nyimbo ndi azeze, apangwe, tizing'wenyeng'wenye, maseche ndi ziwaya zamalipenga.
6
Ndipo atafika pa malo opunthirapo tirigu ku Nakoni, ng'ombe zidaafuna kugwa, ndiye Uza nkutambalitsa dzanja kuti agwirire Bokosi la Mulungu lija, naligwiradi.
7
Pamenepo Chauta adampsera mtima Uzayo, chifukwa sadasunge mwambo, ndipo Mulungu adamkantha, nafera pomwepo pafupi ndi Bokosi la Mulungulo.
8
Tsono Davide adakhumudwa chifukwa chakuti Chauta adaakantha Uza. Ndipo mpaka pano malo amenewo amaŵatchula kuti Pereziuza.
9
Davide adachita mantha ndi Chauta tsiku limenelo, ndipo adafunsa kuti, “Kodi Bokosi la Chautali lingafike bwanji kwathu?”
10
Motero Davide sadafunenso kuti abwere nalo Bokosi la Chautalo kwao ku mzinda wake wa Davide, koma adalipatutsira ku nyumba ya Obededomu Mgiti.
11
Choncho Bokosi lachipanganolo lidakhala miyezi itatu m'nyumba ya Obededomu wa ku Gati. Ndipo Chauta adadalitsa Obededomu ndi banja lake lonse.
12
Tsono Davide adamva kuti Chauta wadalitsa banja la Obededomu ndi zinthu zonse zimene anali nazo, chifukwa cha Bokosi lachipangano. Choncho iye adapita kukatenga Bokosi lachipanganolo, kulichotsa m'nyumba ya Obededomu, napita nalo ku mzinda wake, akukondwera.
13
Ndipo anthu amene ankanyamula Bokosi lachipanganolo ankati akayenda mapazi asanu ndi limodzi, Davide ankapereka nsembe ya ng'ombe yamphongo ndi mwanawang'ombe wonenepa.
14
Davide atavala efodi yabafuta ankavina molemekeza Chauta ndi mphamvu zake zonse.
15
Choncho iye pamodzi ndi Aisraele onse adabwera ndi Bokosi lachipangano akufuula ndi kuliza mbetete.
16
Pamene Bokosi lachipangano linkaloŵa mu mzinda wa Davide, Mikala mwana wamkazi wa Saulo adasuzumira pa windo, naona mfumu Davide akulumphalumpha ndi kuvina molemekeza Chauta. Pamenepo mkaziyo adayamba kunyoza Davide mumtima mwake.
17
Anthu adaloŵa nalo Bokosi lachipangano lija, nakalikhazika pamalo pake m'kati mwa hema limene Davide adaamangira Bokosilo. Tsono Davide adapereka nsembe zopsereza ndi nsembe zachiyanjano kwa Chauta.
18
Atatsiriza kupereka nsembe zopsereza ndi nsembe zachiyanjanozo, adadalitsa anthu m'dzina la Chauta Wamphamvuzonse.
19
Kenaka adagaŵira Aisraele onsewo, amuna ndi akazi, aliyense mtanda wa buledi, nthuli yanyama, ndiponso keke ya mphesa zouma. Tsono anthu onse adachokapo, napita aliyense kunyumba kwake.
20
Pamene Davide adabwerera kuti akadalitse banja lake, Mikala, mwana wa Saulo, adadzamchingamira nati, “Nkutero mfumu ya Aisraele kudzilemekeza kwake lero! Mpaka kuchita kudzivula pamaso pa adzakazi a antchito ake, monga m'mene amachitira munthu wamisala, opanda ndi manyazi omwe!”
21
Davide adamuyankha kuti, “Ndachita zimenezi molemekeza Chauta, amene adandisankhula ine kupambana bambo wako, ndiponso kupambana banja lonse la bambo wako. Ndipo adandiika kuti ndikhale mfumu ya Aisraele, anthu a Chauta. Choncho ndidzasangalalabe ndi kulemekeza Chauta.
22
Ndidzadzinyoza ndithu kupambana pamenepa. Kapena ndidzakhala wonyozeka m'maso mwako, koma m'maso mwa adzakazi amene ukunenawo, ndidzakhala wolemekezeka.”
23
Tsono Mikala, mwana wa Saulo, adaferamo osamuwona mwana.
← Chapter 5
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 7 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24