bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
2 Samuel 11
2 Samuel 11
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
← Chapter 10
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 12 →
1
Pa nyengo yophukira mitengo, nthaŵi imene mafumu ankakonda kukamenya nkhondo, Davide adatuma Yowabu ndi atsogoleri ake ndi ankhondo a Aisraele onse. Adaononga Aamoni, nazinga mzinda wa Raba ndi zithando zankhondo. Koma Davide adatsalira ku Yerusalemu.
2
Zidangochitika kuti tsiku lina chakumadzulo, Davide adadzuka pabedi pake, namayenda pamwamba pa denga la nyumba yake yaufumu. Ali padengapo, adaona mkazi wina akusamba. Mkaziyo anali wokongola kwabasi.
3
Pomwepo Davide adatuma munthu kuti akafunsitse za mkaziyo. Ndipo munthuyo adamuuza kuti, “Mkazi ujatu ndi Bateseba, mwana wa Eliyamu, mwamuna wake ndi Uriya Muhiti.”
4
Apo Davide adatuma amithenga kuti akamtenge mkaziyo. Iwo adabwera naye kwa Davide, ndipo Davideyo adagona naye. Nthaŵi imeneyo nkuti mkaziyo atangomaliza kusamba. Pambuyo pake mkazi uja adabwerera kunyumba kwake.
5
Kenaka ataona kuti waima, adatumiza mau kwa Davide kukamuuza kuti, “Inetu ndi mommuja, sindili bwino!”
6
Atamva zimenezi Davide adatumiza mau kwa Yowabu kuti, “Umtumize Uriya, Muhiti uja, abwere kuno.” Yowabu adatumizadi Uriya kwa Davide.
7
Uriya atabwera, Davide adamufunsa m'mene analiri Yowabu kunkhondoko, ndiponso m'mene analiri anthu, ndi m'menenso nkhondo inkayendera.
8
Kenaka Davide adauza Uriya kuti, “Pita kunyumba kwako, ukapumuleko.” Uriya adatuluka ku nyumba ya mfumu, ndipo mfumu idatumiza mphatso kukapereka kwa Uriya.
9
Koma Uriya adagona pakhomo pa nyumba ya mfumu pamodzi ndi antchito onse a mbuye wake, sadapite kunyumba kwake.
10
Tsono anthu adamuuza Davide kuti, “Uriyatu sadapite kunyumba kwake.” Davideyo adafunsa Uriya kuti, “Kodi suja iwe wachokera ku ulendo? Nanga bwanji sudapite kunyumba kwako?”
11
Uriya adauza Davide kuti, “Bokosi lachipangano likukhala m'zithando, kudzanso Aisraele ndi Ayuda. Ndipo mbuyanga Yowabu pamodzi ndi ankhondo a mfumu akugona panja pamtetete. Ndiye ine ndingapite kunyumba kwanga kuti ndizikadya ndi kumwa, ndi kumakakhala ndi mkazi wanga? Pali inu amene, ine sindingachite zimenezo.”
12
Apo Davide adauza Uriya kuti, “Utandale pompano lero, maŵa ndikulola kuti uzipita.” Choncho Uriya adatandala ku Yerusalemu tsiku limenelo mpaka m'maŵa mwake.
13
Davide adaitana Uriya, nadya naye ndipo adamwa kwambiri, kotero kuti Davide adamledzeretsa. Komabe madzulo Uriya adapita kukagona pogona pake, pamodzi ndi antchito a mfumu, osapita kunyumba kwake.
14
M'maŵa mwake Davide adalembera Yowabu kalata, napatsira Uriya yemweyo kalatayo kuti akapereke.
15
M'kalatamo adalembamo kuti, “Uriyayo umuike patsogolo penipeni pamene pakulimba nkhondo, ndipo umlekerere yekha kuti alasidwe ndi kuphedwa.”
16
Choncho pamene Yowabu ankazinga mzindawo, adaika Uriya pamalo pamene ankaŵadziŵa kuti pali ankhondo amphamvu.
17
Tsono ankhondo amumzindamo adatuluka nadzamenyana ndi Yowabu. Ndipo ena mwa ankhondo a Davide adaphedwa. Uriya, Muhiti uja, nayenso adaphedwa.
18
Zitatero, Yowabu adatuma wamthenga kwa Davide kukamuuza zonse zimene zidachitika kunkhondoko.
19
Adauza wamthengayo kuti, “Utatha kumuuza mfumu mbiri yonse ya nkhondo,
20
tsono ngati mfumu ikapse mtima, nikakufunsa kuti, ‘Chifukwa chiyani mudapita kufupi ndi mzinda kuti mukamenye nkhondo? Kodi simunkadziŵa kuti adzakulasani kuchokera m'kati mwa linga?
21
Kodi Abimeleki mwana wa Gideoni adamupha ndani? Kodi adamupha si mkazi, pomkunkhunizira mwalawamphero kuchokera pa linga, kotero kuti adafera ku Tebezi? Chifukwa chiyani mudakafika pafupi ndi khoma?’ Pamenepo iweyo ukanene kuti, ‘Wankhondo wanu, Uriya Muhiti uja, nayenso adaphedwa.’ ”
22
Wamthenga uja adapita, nakafika kwa Davide, nakamuuza zonse zimene Yowabu adamuuza kuti akanene.
23
Adauza Davide kuti, “Adani athu adaatipambana, ndipo adaatuluka kukalimbana nafe ku thengo. Koma ife tidaŵabweza mpaka ku khomo lakuchipata.
24
Tsono anthu oponya mivi ankalasa ankhondo anu kuchokera m'linga. Ndipo ankhondo ena mwa ankhondo a inu mfumu adaphedwa. Wankhondo wanu uja, Uriya Muhiti, nayenso adaphedwa.”
25
Apo Davide adauza wamthenga uja kuti, “Kamuuze Yowabu kuti, ‘Zimenezi usavutike nazo, poti wakufa sadziŵika. Ulimbike polimbana ndi mzindawo, ndi kuugonjetsa.’ Choncho ukamlimbitse mtima Yowabuyo.”
26
Pamene mkazi wa Uriya adamva kuti mwamuna wake Uriya adaphedwa, adalira, kulira mwamuna wake.
27
Mkaziyo atatha kulira malirowo, Davide adatuma munthu nakamtenga, nkubwera naye kunyumba kwa mfumu, ndipo Davide adamukwatira. Mkaziyo adambalira mwana wamwamuna. Koma zimene adachita Davidezi zidaipira Chauta.
← Chapter 10
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 12 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24