bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
2 Samuel 8
2 Samuel 8
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
← Chapter 7
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 9 →
1
Pambuyo pake Davide adathira nkhondo Afilisti, naŵagonjetsa, ndipo adaŵalanda mzinda wa Metegama.
2
Kenaka Davide adagonjetsa Amowabu. Adalamula onsewo kuti agone pansi m'mizere itatu pa gulu lililonse. Pagulu lililonse anali kupha anthu amene anali pa mizere iŵiri yoyamba, kusiyapo a mzere wachitatu. Choncho Amowabu adasanduka akapolo a Davide, nayamba kukhoma msonkho kwa iye.
3
Davide adagonjetsanso Hadadezere, mwana wa Rehobu, mfumu ya ku Zoba, pamene Hadadezereyo ankapita kumtunda kwa mtsinje wa Yufurate, kuti akakhazikitsenso ulamuliro wake ku deralo.
4
Davide adagwira ankhondo a Hadadezere. Okwera pa akavalo analipo 1,700, a pansi analipo 20,000. Ndipo adadula mitsempha ya miyendo ya akavalo onse okakoka magaleta, koma adasungako ena a magaleta 100.
5
Pamene Asiriya a ku Damasiko adaabwera kudzathandiza Hadadezere, mfumu ya ku Zoba, Davide adapha anthu a ku Siriyawo okwanira 22,000.
6
Pambuyo pake Davide adaika maboma a ankhondo ku Damasiko, m'dziko la Siriya. Choncho Asiriyawo adasanduka otumikira Davide, nayamba kukhoma msonkho kwa iye. Motero Chauta adampambanitsa Davideyo kulikonse kumene ankapita.
7
Davide adatenga zishango zagolide zimene anyamata a Hadadezere ankanyamula, nabwera nazo ku Yerusalemu.
8
Kuchokera ku Beta ndi ku Berotai, mizinda ya Hadadezere, Mfumu Davide adabwerako ndi mkuŵa wambiri.
9
Pamene Toi mfumu ya ku Hamati adamva kuti Davide wagonjetsa gulu lonse lankhondo la Hadadezere,
10
adatuma mwana wake Yoramu kwa mfumu Davide, kuti akamlonjere. Adaafunanso kukamuyamika chifukwa chakuti adaamenya nkhondo ndi Hadadezere namgonjetsa. Adaatero pakuti Hadadezereyo ankamenyana nkhondo ndi Toi kaŵirikaŵiri. Tsono Yoramuyo adabwera ndi mphatso zopangidwa ndi siliva, golide, ndi mkuŵa.
11
Zimenezonso mfumu Davide adazipereka kwa Chauta pamodzi ndi siliva ndi golide amene adaafunkha kwa anthu a mitundu ina amene adaŵagonjetsa.
12
Anthuwo anali Aedomu, Amowabu, Aamoni, Afilisti ndi Aamaleke. Zina zinali zimene adaafunkha kwa Hadadezere mwana wa Rehobu, mfumu ya ku Zoba.
13
Mbiri ya Davide idamveka ponseponse. Pamene ankabwerera, anali atapha Aedomu 18,000 ku chigwa cha Mchere.
14
Tsono adaika zigono za ankhondo pena ndi pena m'dziko la Edomu. Mu Edomu monse munali timagulu ta ankhondo, choncho Aedomu onse adasanduka otumikira Davide. Motero Chauta adampambanitsa Davide kulikonse kumene ankapita.
15
Motero Davide adalamulira dziko lonse la Israele, ndipo ankayendetsa zonse mwachilungamo ndi mosakondera.
16
Tsono Yowabu, mwana wa Zeruya, anali mtsogoleri wa ankhondo, ndipo Yehosafati, mwana wa Ahiludi, anali mlembi wolemba mbiri.
17
Zadoki, mwana wa Ahitubi, ndiponso Ahimeleki, mwana wa Abiyatara, anali ansembe, ndipo Seraya anali mlembi.
18
Benaya, mwana wa Yehoyada, anali nduna yoyang'anira Akereti ndi Apeleti, ndipo ana a Davide anali ansembe.
← Chapter 7
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 9 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24