bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
2 Samuel 3
2 Samuel 3
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
← Chapter 2
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 4 →
1
Kunali nkhondo nthaŵi yaitali pakati pa anthu a Saulo ndi anthu a Davide. Davide mphamvu zake zinkakulirakulira pamene anthu a Saulo ankafookerafookera.
2
Davide adabereka ana aamuna ku Hebroni. Mwana wake woyamba anali Aminoni, wobadwa kwa Ahinowamu wa ku Yezireele.
3
Wachiŵiri anali Kiliyabu, wobadwa kwa Abigaile, mkazi wamasiye wa Nabala, wa ku Karimele. Wachitatu anali Abisalomu, wobadwa kwa Maaka, mwana wa Talimai, mfumu ya ku Gesuri.
4
Wachinai anali Adoniya, wobadwa kwa Hagiti. Wachisanu anali Sefatiya wobadwa kwa Abitala.
5
Ndipo mwana wachisanu ndi chimodzi anali Itireamu, wobadwa kwa Egila. Ameneŵa ndiwo ana a Davide amene adabadwira ku Hebroni.
6
Pamene kunali nkhondo pakati pa anthu a Saulo ndi anthu a Davide, Abinere adayamba kudzipatsa mphamvu pa anthu a Saulo.
7
Saulo anali ndi mzikazi dzina lake Rizipa, mwana wa Aya. Tsono Isiboseti adafunsa Abinere kuti, “Chifukwa chiyani wakaloŵa kwa mzikazi wa bambo wanga?”
8
Abinere adapsa nawo mtima kwambiri mau a Isiboseti, ndipo adati, “Kodi ukundiyesa ine galu wa Ayuda, adani athu? Kuyambira poyamba pomwe ndakhala wokhulupirika kwa Saulo bambo wako, abale ake, ndi abwenzi ake, ndipo sindidakupereke m'manja mwa Davide. Ndiye lero, iwe ukundiimba mlandu woti ndachimwa ndi mkazi!
9
Nchifukwa chake Mulungu andilange, ngakhale kundipha kumene, ngati sindimchitira Davide zimene Chauta adamlonjeza.
10
Ndidzachotsa ufumu pa banja la Saulo ndi kuupereka kwa Davide, kuti alamulire Israele ndi Yuda kuyambira ku Dani mpaka ku Beereseba.”
11
Pamenepo Isiboseti adangoti kukamwa yasa, osatha kumuyankha Abinere mau ndi amodzi omwe, chifukwa ankamuwopa kwambiri.
12
Tsono Abinere adatuma amithenga kwa Davide ku Hebroni kukamufunsa kuti, “Kodi dzikoli nlayani? Tipangane, ine ndidzakuthandizani kuti dziko la Israele likhale lanu.”
13
Apo Davide adati, “Chabwino, tipangana. Koma ndikukupempha chinthu chimodzi: sudzandiwona ukapanda kubwera ndi Mikala, mwana wamkazi wa Saulo.”
14
Tsono Davide adatuma amithenga kwa Isiboseti, mwana wa Saulo, kukanena kuti, “Undipatse mkazi wanga, Mikala, amene ndidamukwatira polipira timakungu 100 ta nsonga za mavalo a Afilisti.”
15
Pamenepo Isiboseti adatuma anthu kuti akamtenge Mikalayo kwa mwamuna wake Palatiele, mwana wa Laisi.
16
Koma mwamuna wakeyo adamtsatira mkaziyo. Mwamunayo ankapita nalira njira yonse mpaka ku Bahurimu. Abinere adamuuza kuti, “Iwe, bwerera.” Iye uja nkubwereradi.
17
Pambuyo pake Abinere pokambirana ndi atsogoleri a Aisraele, adaŵauza kuti, “Nthaŵi yapitayi mwakhala mukufuna Davide kuti akhale mfumu yanu yokulamulani.
18
Ndiye zimenezi muchitedi. Paja Chauta adalonjeza Davide kuti, ‘Ndidzapulumutsa anthu anga Aisraele kwa Afilisti kudzera mwa iwe mtumiki wanga, ndipo ndidzaŵapulumutsa kwa adani ao onse.’ ”
19
Abinere adalankhulanso ndi anthu a fuko la Benjamini. Kenaka adakauzanso Davide ku Hebroni zonse zimene Abenjamini ndi Aisraele adavomerezana kuti achite.
20
Pambuyo pake Abinere adabwera ndi anthu makumi aŵiri kwa Davide ku Hebroni. Davideyo adakonzera madyerero Abinere ndi anthu makumi aŵiri amene anali nawowo.
21
Tsono Abinere adauza Davide kuti, “Loleni ndikasonkhanitse Aisraele onse kuti abwere kwa inu kuno, mbuyanga mfumu, kuti adzachite nanu chipangano, ndipo kuti muzilamulira kulikonse kumene mtima wanu ufuna.” Choncho Davide adamlola Abinere kuti apite. Ndipo iye adapita mwamtendere.
22
Nthaŵi yomweyo ankhondo a Davide adafika ndi Yowabu kuchokera kumene adaakamenya nkhondo, atatenga zofunkha zambiri. Koma Abinere sanali ndi Davide ku Hebroni, popeza kuti anali atamlola kuti apite, ndipo iye anali atapitadi mwamtendere.
23
Pamene Yowabu ndi ankhondo onse amene anali nawo adabwera, ena adauza Yowabuyo kuti, “Abinere mwana wa Nere adaabwera kwa amfumu, ndipo amfumuwo adamlola kuti apite, mwakuti wapitadi mwamtendere.”
24
Atamva zimenezo Yowabu adapita kwa mfumu nakafunsa kuti, “Inu amfumu, kodi akuti mwachita zotani? Abinere wobwera bwinobwino kuno, nanga bwanjinso inu mwamlola kuti apite? Moti wapitadi?
25
Inu amfumu, monga Abinere, mwana wa Nere, simumdziŵa? Amene ujatu adaabwera kudzangokumyatani m'maso. Adaafuna kudzangokutambwani, kuti adziŵe zonse zimene mukuchita.”
26
Yowabu atachokako kwa Davide kuja, adatuma amithenga kuti amlondole Abinere. Iwowo adakampezadi ku chitsime cha Sira, nambweza, Davide osadziŵa kanthu.
27
Pamene Abinere ankabwerera ku Hebroni, Yowabu adamtengera pambali, pafupi ndi chipata, nakhala ngati afuna kulankhula naye poduka mphepo. Pomwepo Yowabu adabaya Abinere m'mimba, nkuferatu. Yowabu adachita zimenezi chifukwa choti Abinere anali atamuphera mbale wake Asahele.
28
Pambuyo pake Davide atamva, adati, “Ine pamodzi ndi anthu a mu ufumu wanga tilibe ndi mlandu womwe pamaso pa Chauta pa imfa ya Abinere, mwana wa Nere.
29
Mlandu umenewu ugwere Yowabu ndi onse a pa banja la bambo wake. Ndipo Mulungu amlange Yowabuyu kuti pabanja pake pasadzakhale popanda munthu wa nthenda ya chidzonono, kapena wakhate, kapena wolumala, kapena wophedwa ku nkhondo kapenanso wosoŵa chakudya.”
30
Choncho Yowabu ndi mbale wake Abisai adapha Abinere chifukwa choti Abinereyo anali ataŵaphera mbale wao Asahele pa nkhondo ya ku Gibiyoni.
31
Tsono Davide adauza Yowabu ndi anthu onse amene anali naye kuti, “Ng'ambani zovala zanu, muvale ziguduli, kuti mulire maliro a Abinere.” Ndipo mfumu Davide mwiniwake ankatsatira onyamula mtembowo.
32
Adakamuika Abinere ku Hebroni. Ndiye mfumu idalira mokweza mau ku manda a Abinere. Nawonso anthu onse adalira kwambiri.
33
Polira maliro a Abinere mfumu Davide ankati, “Abinere nkufa motere, monga m'mene chimafera chitsiru?
34
Manja ako anali osamanga, mapazi ako anali osakulunga. Komabe wafa monga m'mene amafera munthu m'manja mwa anthu oipa mtima.” Anthu onse adaliranso, kumlira Abinere.
35
Kenaka anthuwo adadza kudzapempha mfumu kuti adye chakudya kudakali koyera. Koma Davide adalumbira kuti, “Mulungu andilange kwabasi, ngati ndidya chakudya kapena kanthu kena kalikonse dzuŵa lisanaloŵe.”
36
Anthu onse adamvera zimenezo, ndipo zidaŵakomera. Zonse zimene ankachita mfumu zinkaŵakondwetsa anthu onse.
37
Choncho onse amene ankakhala ndi mfumu pamodzi ndi Aisraele onse adamvetsa tsiku limenelo kuti sikunali kufuna kwa mfumu kuti Abinere mwana wa Nere aphedwe.
38
Ndipo mfumu Davide adafunsa ankhondo ake kuti, “Kodi simukudziŵa kuti lero m'dziko la Israele mwagwa kalonga amene ali munthu wamkulu?
39
Tsono ine lero ndafooka kwambiri, ngakhale kuti ndine mfumu yodzozedwa. Ndithu anthu ameneŵa, ana aamuna a Zeruya, akundivutitsa kwambiri. Chauta abwezere munthu wochita zoipa molingana ndi kuipa kwake.”
← Chapter 2
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 4 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24