bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
2 Samuel 2
2 Samuel 2
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
← Chapter 1
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 3 →
1
Pambuyo pake, Davide adafunsa Chauta kuti, “Kodi ndipite kukakhazikika ku mzinda wina uliwonse wa ku Yuda?” Chauta adamuuza kuti, “Inde, pita.” Apo Davide adafunsa kuti, “Tsono ndipite kuti?” Chauta adati, “Pita ku Hebroni.”
2
Motero Davide adapita kumeneko pamodzi ndi akazi ake aŵiri aja, Ahinowamu wa ku Yezireele, ndi Abigaile mkazi wamasiye uja wa Nabala wa ku Karimele.
3
Ndipo Davide adabwera ndi anthu ake aja amene anali nawo, aliyense ndi banja lake. Adakhala m'midzi ya ku Hebroni.
4
Tsono anthu a ku Yuda adafika, ndipo kumeneko adadzoza Davide kuti akhale mfumu yao. Davide atamva kuti ndi anthu a ku Yabesi-Giliyadi amene adaika Saulo m'manda,
5
adatuma amithenga kwa anthuwo kukaŵauza kuti, “Chauta akudalitseni, poti mudaonetsa kukhulupirika kwanu pomuika Saulo mbuyanu.
6
Tsopano Chauta akuwonetseni chikondi chake chosasinthika, ndiponso kukhulupirika kwake kwa inu. Ndipotu inenso ndidzakuchitirani zabwino chifukwa cha zimene mwachitazi.
7
Nchifukwa chake tsono mulimbe mtima, ndipo muchite chamuna. Paja mbuyanu Saulo adamwalira, ndipo anthu a mtundu wa Yuda andidzoza ine kuti ndikhale mfumu yao.”
8
Abinere mwana wa Nere, amene ankalamula ankhondo a Saulo, anali atatenga Isiboseti mwana wa Saulo, kupita naye kutsidya, ku Mahanaimu.
9
Tsono adamlonga ufumu kuti akhale mfumu ya Giliyadi, Asere, Yezireele, Efuremu ndi Benjamini, kungoti Israele yense.
10
Isiboseti, mwana wa Saulo, anali wa zaka 40 pamene adayamba kulamulira Israele, ndipo ufumu wake udakhala zaka ziŵiri. Koma fuko la Yuda lidatsata Davide.
11
Ndipo Davide adakhala mfumu ya fuko la Yuda ku Hebroni zaka zisanu ndi ziŵiri ndi theka.
12
Tsono Abinere mwana wa Nere pamodzi ndi ankhondo a Isiboseti mwana wa Saulo adapita ku Gibiyoni kuchokera ku Mahanaimu.
13
Yowabu mwana wa Zeruya pamodzi ndi ankhondo a Davide adapita kukakumana nawo ku dziŵe la Gibiyoni. Adakhala pansi, ena tsidya lina la dziŵelo, enanso tsidya lina.
14
Abinere adauza Yowabu kuti, “Anyamata anu ndi athu abwere, amenyane tiwone.” Yowabu adati, “Chabwino, namenyane.”
15
Anyamatawo adabweradi naŵaŵerenga. A fuko la Benjamini, anyamata a Isiboseti, mwana wa Saulo, analipo khumi ndi aŵiri, anyamata a Davide analinso khumi ndi aŵiri.
16
Tsono aliyense adagwira mutu wa mnzake nabaya mnzakeyo m'nthitimu ndi lupanga. Choncho onse 24 adafera limodzi. Nchifukwa chake malo amenewo adaŵatchula kuti Helikati-Hazurimu, ndipo ali ku Gibiyoni.
17
Tsono panali nkhondo yoopsa tsiku limenelo. Abinere pamodzi ndi anthu a ku Israele adagonjetsedwa ndi ankhondo a Davide.
18
Yowabu, Abisai ndi Asahele, ana atatu aja a Zeruya, anali komweko. Asahele anali waliŵiro ngati insa.
19
Iyeyo adathamangitsa Abinere. Pothamangapo sankayang'ana uku ndi uku, maso anali pa Abinere basi.
20
Tsono Abinere adacheuka nati, “Kodi ndiwe, Asahele?” Iye adayankha kuti, “Ndine amene.”
21
Abinere adamuuza kuti, “Patukira mbali ina iliyonse, ukagwire mmodzi mwa ankhondowo, umlande zake.” Koma Asahele sadafune kuti aleke kuthamangitsa Abinere.
22
Tsono Abinere adauzanso Asahele kuti, “Iwe leke, usandithamangitse, bwanji ukundikakamiza kuti ndikuphe? Nanga ndikakupha, mbale wako Yowabu ndikaonana naye bwanji?”
23
Koma Asahele sadafune kumleka. Choncho Abinere adabaya Asaheleyo m'mimba ndi luti la mkondo wake, mkondowo nkutulukira kumsana. Asahele adagwa pansi, kufa nkukhala komweko. Anthu onse amene adafika pamalo pomwe padafera Asahele, adangoima kungoti kakasi.
24
Koma Yowabu ndi Abisai adayamba kuthamangitsa Abinere. Ndipo pamene dzuŵa linkaloŵa, adakafika ku phiri la Ama limene lili cha kuno kwa Giya, pa njira yopita ku chipululu cha Gibiyoni.
25
Abenjamini adasonkhana pamodzi kuthandiza Abinere, ndipo adapanga gulu limodzi lankhondo, nakaima pamwamba pa phiri.
26
Tsono Abinere adafuulira Yowabu namufunsa kuti, “Kodi tipitirirebe kumenyana mpakampaka? Monga sukudziŵa kuti mathero ake adzakhala oŵaŵa? Kodi udzaŵaletsa liti anthu ako kutithamangitsa ife abale ao?”
27
Yowabu adayankha kuti, “Ndithudi, ndikulumbira, pali Mulungu wamoyo, ukadapanda kulankhula, ankhondo angaŵa sakadaleka kuŵathamangitsa abale aowo mpaka maŵa m'maŵa.”
28
Choncho Yowabu adaliza lipenga, ndipo anthu onse adaleka, osathamangitsanso Aisraele, ndipo sadamenyane nawonso.
29
Choncho Abinere ndi anthu ake adayenda usiku wonse, nabzola chidikha cha Araba. Adaoloka mtsinje wa Yordani, ndipo adayenda m'maŵa monse, nakafika ku Mahanaimu.
30
Yowabu adabwerako kumene adaakathamangitsa Abinere kuja. Atasonkhanitsa anthu onse pamodzi, kudapezeka kuti padasoŵa ankhondo a Davide okwanira 19, pamodzi ndi Asahele.
31
Koma ankhondo a Davidewo anali atapha anthu 360 a Abinere, a fuko la Benjamini.
32
Tsono adatenga mtembo wa Asahele, nakauika m'manda a bambo wake, amene anali ku Betelehemu. Yowabu ndi anthu ake adayenda usiku wonse, ndipo kudaŵachera ali ku Hebroni.
← Chapter 1
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 3 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24