bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
2 Samuel 22
2 Samuel 22
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
← Chapter 21
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 23 →
1
Tsiku limene Chauta adaapulumutsa Davide kwa adani ake onse ndiponso kwa Saulo,
2
Davideyo adaimbira Chauta nyimbo iyi yakuti, “Chauta ndiye thanthwe langa, linga langa ndi mpulumutsi wanga.
3
Ndiye Mulungu wanga ndi thanthwe langa limene ndimathaŵirako. Ndiye chishango changa, ndiye mtetezi wanga ndi mpulumutsi wanga. Ndiye linga langa ndi mpulumutsi wanga. Ndinu amene mumandiwombola pa nkhondo.
4
Ndimaitana Chauta, amene ayenera kumtamanda, ndipo amandipulumutsa kwa adani anga.
5
“Zoŵaŵa za imfa zidandizinga, mitsinje ya ku malo a anthu akufa idandisefukira.
6
Nthambo zakumanda zidandizeŵeza, misampha ya imfa idandikola.
7
“Ndidaitana Chauta m'zovuta zanga, ndidafuulira Mulungu wanga kuti andithandize. Iye ali m'Nyumba mwake adamva liwu langa, kulira kwanga kofuna chithandizo kudamveka kwa iye.
8
“Pamenepo dziko lapansi lidanjenjemera ndi kuchita chivomezi. Maziko akumwamba adagwedezeka ndi kulilima chifukwa Chauta adaakalipa.
9
M'mphuno mwake munkafuka utsi, m'kamwa mwake munkatuluka moto woononga, makala amoto anali laŵilaŵi kuchokera m'kamwa momwemo.
10
Adang'amba thambo natsika pansi, mdima wabii unali ku mapazi ake.
11
Adakwera pa mkerubi nauluka, adayenda mwaliŵiro ndi mphepo.
12
Mdima adausandutsa chofunda chake, mitambo yakuda yamvula adaisandutsa mwafuli wake.
13
M'kuŵala kumene kunali pamaso pake munkafumira makala amoto alaŵilaŵi.
14
Kumwamba Chauta adagunda ngati bingu, Wopambanazonse liwu lake lidamveka.
15
Adaponya mivi yake, nabalalitsa adani ake. Adachititsa zing'aning'ani, naŵapirikitsa.
16
Ngalande zozama zam'nyanja zidaonekera, maziko a dziko lapansi adakhala poyera, pamene Chauta adakhuluma mokalipa, pamene adatulutsa mpweya wamphamvu m'mphuno mwake.
17
“Ali kumwamba Chauta adatambalitsa dzanja nandigwira, ndi kundivuula m'madzi ozama.
18
Adandipulumutsa kwa adani anga amphamvu, kwa onse amene ankadana nane; pakuti iwo anali amphamvu kwambiri kupambana ine.
19
Adaniwo adandithira nkhondo pamene ndinali m'mavuto, koma Chauta adandichirikiza.
20
Adakandifikitsa ku malo amtendere, adandipulumutsa chifukwa adakondwera nane.
21
“Chauta adandipatsa mphotho molingana ndi kulungama kwanga, adandifupa molingana ndi ungwiro wanga.
22
Ine ndidatsata njira za Chauta sindidachite zoipa ndi kumsiya Mulungu wanga.
23
Ndidamvera malangizo ake onse, ndipo malamulo ake sindidaŵataye.
24
Ndinalibe mlandu pamaso pake, ndinkalewa zoipa m'moyo wanga.
25
Nchifukwa chake Chauta wandipatsa mphotho molingana ndi kulungama kwanga, monga momwe akuwonera kuti ndilibe mlandu.
26
“Kwa anthu okhulupirika, Inu Mulungu mumadziwonetsa okhulupirika, kwa anthu aungwiro mumadziwonetsa abwino kotheratu.
27
Kwa anthu oyera mtima mumadziwonetsa okoma mtima, koma kwa anthu oipa mtima mumadziwonetsa ochenjera koposa.
28
Paja anthu odzichepetsa Inu mumaŵapulumutsa, koma anthu odzikuza mumaŵatsitsa.
29
Ndithu Inu Chauta, ndinu nyale yanga, Inu Mulungu, mumandiwunikira mu mdima.
30
Ndi chithandizo chanu ndingathe kugonjetsa gulu la ankhondo. Ndi chithangato chanu, Inu Mulungu, ndingathe kupambana.
31
Mulungu wathuyo zochita zake nzangwiro, mau a Chauta ndi oona. Iye ndiye chishango choteteza onse othaŵira kwa Iye.
32
“Palibe Mulungu wina koma Chauta yekha. Palibe thanthwe lina lothaŵirapo koma Mulungu wathu yekha?
33
Mulungu wathu ndiye linga langa lolimba, wandichotsera zoopsa m'njira zanga.
34
Amalimbitsa mapazi anga ngati a mbaŵala, ndipo amandisunga bwino ku mapiri.
35
Amaphunzitsa manja anga kamenyedwe ka nkhondo, kotero kuti ndingathe kupinda uta wachitsulo.
36
Inu mwanditeteza ndi chishango chanu chachipulumutso. Mwandikweza ndi chithandizo chanu.
37
Mwalimbitsa miyendo yanga kuti ndiyende bwino, choncho mapazi anga sadaterereke.
38
Ndidalondola adani anga ndi kuŵapeza, sindidabwerere mpaka nditaŵagonjetsa.
39
Ndidaŵakantha, ndidaŵagwetsa pansi, kotero kuti sadadzukenso, ndidaŵapondereza ndi mapazi anga.
40
Paja ndinu mudandipatsa mphamvu zomenyera nkhondo, ndinu mudandigonjetsera anthu ondiwukira.
41
Inu mudapirikitsa adani anga kuti andithaŵe, amene ankadana nane ndidaŵaononga.
42
Adakuwa, koma panalibe ndi mmodzi yemwe woŵapulumutsa. Adalirira Chauta, koma sadaŵayankhe.
43
Ndidaŵaperapera ngati fumbi, ndidaŵaphwanya ndi kuŵapondereza ngati matope amumseu.
44
“Mudandipulumutsa kwa anthu anga ondiwukira. Mudandisunga kuti ndikhale wolamulira mitundu yonse. Choncho anthu osaŵadziŵa adayamba kunditumikira.
45
Anthu a maiko ena adabwera kwa ine kudzapemba; atangomva mau anga oyamba adandimvera.
46
Anthu a mitundu ina adataya mtima, adatuluka m'malinga mwao ali njenjenje.
47
“Chauta ndiwamoyo. Litamandike thanthwe langa, alemekezeke Mulungu wanga, thanthwe londipulumutsa.
48
Mulungu ndiye adandithandiza kuti ndilipsire, ndi kugonjetsa anthu a mitundu ina kuti akhale mu ulamuliro wanga.
49
Ndinu amene mudandipulumutsa kwa adani anga. Mudandikweza pamwamba pa ondiwukira, mudandilanditsa kwa anthu ankhanza.
50
“Chifukwa cha zimenezi ndidzakuyamikani Inu Chauta, pakati pa mitundu ya anthu, ndidzaimba nyimbo zotamanda dzina lanu.
51
Mulungu amathandiza mfumu yake kuti izipambana nthaŵi ndi nthaŵi. Amaonetsa chikondi chake chosasinthika kwa wodzozedwa wake, ndiye kuti kwa Davide ndi kwa zidzukulu zake mpaka muyaya.”
← Chapter 21
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 23 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24