bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
2 Samuel 5
2 Samuel 5
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
← Chapter 4
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 6 →
1
Pambuyo pake mafuko onse a Aisraele adadzasonkhana kwa Davide ku Hebroni. Adamuuza kuti, “Ifetu ndi inuyo tili magazi amodzi.
2
Kale Saulo adakali mfumu yathu yotilamulira, ndinuyo amene munkatsogolera Aisraele ku nkhondo nkubwera nawonso. Ndipo Chauta adaakuuzani kuti, ‘Udzakhala mbusa wa anthu anga Aisraele, udzakhala mfumu ya Israele.’ ”
3
Choncho atsogoleri onse a Aisraele adadza kwa mfumu ku Hebroni. Tsono mfumu Davide adachita nawo chipangano pamaso pa Chauta ku Hebroniko, ndipo anthuwo adamdzoza Davideyo kuti akhale mfumu ya Aisraele onse.
4
Davide anali wa zaka makumi atatu za kubadwa pamene adaloŵa ufumu. Adakhala mu ufumu zaka makumi anai.
5
Ku Hebroni adalamulira Ayuda zaka zisanu ndi ziŵiri ndi theka. Ndipo ku Yerusalemu adalamulira Israele yense ndi Yuda zaka 33.
6
Mfumu Davide ndi anthu ake adapita ku Yerusalemu kukamenyana ndi Ayebusi. Ayebusiwo anali nzika za dzikolo. Anthuwo adauza Davide kuti, “Sudzaloŵa muno ai. Anthu akhungu ndi anthu opunduka ndiwo adzakupirikitse.”
7
Komabe Davide adalanda linga la Ziyoni, ndiye kuti Mzinda wa Davide.
8
Tsono tsiku limenelo Davide adati, “Aliyense wofuna kuti akakanthe Ayebusi, ayenera kudzera m'ngalande ya madzi, kuti akaphe opunduka ndi akhunguwo amene mtima wanga umadana nawo.” Nchifukwa chake amanena kuti, “Akhungu ndi opunduka sadzaloŵa m'Nyumba ya Chauta.”
9
Tsono Davide adakhala mu mzinda wamalinga uja nautchula dzina lakuti, “Mzinda wa Davide.” Ndipo adamanga mzinda kuzungulira deralo kuyambira ku malo komwe kale kunali chidikha, kuvuma kwa phiri mpaka m'kati mwake.
10
Motero mphamvu za Davide zidanka zikulirakulira, chifukwa Chauta, Mulungu Wamphamvuzonse, anali naye.
11
Hiramu, mfumu ya ku Tiro, adatuma amithenga kwa Davide, pamodzi ndi mitengo ya mkungudza, ndiponso amisiri a matabwa ndi ena odziŵa kumanga ndi miyala. Iwowo adadzamangira Davide nyumba yachifumu.
12
Motero Davide adazindikira kuti Chauta wamkhazikitsa kuti akhale mfumu yolamulira Aisraele, ndiponso kuti wakweza ufumu wake chifukwa cha Aisraele, anthu ake.
13
Tsono Davide atafika ku Yerusalemu kuchokera ku Hebroni, adakwatira akazi ena natenganso azikazi ena kumeneko. Tsono adabereka ana ambiri, aamuna ndi aakazi.
14
Naŵa maina a ana a Davide amene adabadwira ku Yerusalemu: Samuwa, Sobabu, Natani, Solomoni,
15
Ibara, Elisuwa, Nefegi, Yafiya,
16
Elisama, Eliyada ndi Elifeleti.
17
Afilisti atamva kuti Davide wadzozedwa kukhala mfumu yolamulira dziko la Aisraele, adapita kukamfunafuna. Koma Davide atamva zimenezo, adatsikira ku linga.
18
Tsono Afilisti adabwera nakhala momwazikana m'chigwa cha Refaimu.
19
Davide adafunsa kwa Chauta kuti, “Kodi ndipite kukamenyana nawo nkhondo Afilistiwo? Kodi mudzaŵapereka m'manja mwanga?” Chauta adamuuza kuti, “Inde, pita. Ndidzaŵaperekadi Afilistiwo m'manja mwako.”
20
Pamenepo Davide adapita ku Baala-Perazimu, ndipo adagonjetsa Afilistiwo kumeneko. Tsono adati, “Ine ndikufika, Chauta waŵang'amba pakati adani anga ngati madzi a chigumula.” Nchifukwa chake malo amenewo amatchedwa kuti Baala-Perazimu.
21
Afilisti adasiya mafano ao kumeneko, ndipo Davide ndi anthu ake adatenga mafanowo napita nawo kwao.
22
Nthaŵi ina Afilisti adabweranso, nandanda m'chigwa chija cha Refaimu.
23
Davide atafunsa Chauta, adamuyankha kuti, “Usakaŵathire nkhondo kumaso. Uŵadzere cha kumbuyo, uŵathire nkhondo pa malo oyang'anana ndi mitengo ya mkandankhuku ija.
24
Tsono ukakamva phokoso pa nsonga za mitengo ya mkandankhukuyo, pamenepo ukakonzeke, chifukwa ndiye kuti Chauta wakutsogolera kuti ukakanthe gulu lankhondo la Afilistiwo.”
25
Davide adachitadi monga momwe Chauta adaamlamulira, ndipo adagonjetsa Afilistiwo kuyambira ku Geba mpaka ku Gezere.
← Chapter 4
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 6 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24