bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
2 Samuel 18
2 Samuel 18
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
← Chapter 17
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 19 →
1
Pambuyo pake Davide adasonkhanitsa anthu amene anali naye kuti aŵagaŵe m'magulu, ndipo adaŵaikira atsogoleri, ena olamulira anthu zikwi, ena olamulira anthu mazana.
2
Ndipo Davide adatumiza gulu lankhondo ataligaŵa patatu, chigawo chimodzi cholamulidwa ndi Yowabu, china cholamulidwa ndi Abisai, mwana wa Zeruya, mng'ono wake wa Yowabu, china cholamulidwa ndi Itai Mgiti. Tsono mfumu idauza anthuwo kuti, “Inenso ndipita nao.”
3
Koma anthuwo adati, “Inuyo simupita nao, chifukwa ife tikathaŵa, adani sadzatisamala. Ngati theka la ife lifa, iwo sadzasamalako za ife. Koma inu mukuposa anthu 10,000 mwa ife. Nchifukwa chake nkwabwino kwambiri kuti inu muzingotitumizira chithandizo kuchokera kumzindako.”
4
Mfumu idaŵauza kuti, “Chilichonse chimene chikukomereni, ndidzachita.” Choncho mfumuyo idakaimirira pambali pa chipata nthaŵi imene gulu lonse lankhondo linkatuluka mazanamazana, ndiponso zikwizikwi.
5
Ndipo mfumu idalamula Yowabu, Abisai ndi Itai kuti, “Mumlezere mtima mwanayo Abisalomu chifukwa cha ine.” Anthu onse adamva pamene mfumu inkalamula atsogoleri a ankhondo kunena za Abisalomu.
6
Tsono ankhondo adatuluka kunka ku thengo kukamenyana ndi Aisraele. Ndipo nkhondo idachitikira ku nkhalango ya Efuremu.
7
Aisraele adagonjetsedwa kumeneko ndi ankhondo a Davide. Motero tsiku limenelo adaphedwa anthu ambiri okwanira 20,000 onse pamodzi.
8
Nkhondo idafalikira m'dziko lonselo, ndipo zoopsa zam'nkhalango zidapha anthu ambiri kuposa anthu ophedwa ndi lupanga.
9
Mwadzidzidzi Abisalomu adakumana ndi ankhondo a Davide. Abisalomuyo anali atakwera pa bulu wake, ndipo buluyo adaloŵa kunsi kwa nthambi zochindikira za mtengo wa thundu. Pamenepo Abisalomu adatsalira ali lendee, mutu wake utapanika pa nthambiyo, pamene bulu ankakwerayo adapitirira.
10
Munthu wina ataona zimenezo, adauza Yowabu kuti, “Ndamuwona Abisalomu ali lendee mu mtengo wa thundu.”
11
Yowabu adafunsa munthuyo kuti, “Nanga bwanji sudamphere pomwepo? Ndikadakondwa ndipo ndikadakupatsa ndalama zasiliva khumi ndiponso lamba.”
12
Koma munthuyo adauza Yowabu kuti, “Ngakhale ndikadalandira m'manja mwangamu ndalama zasiliva zokwanira 1,000, sindikadasamula dzanja langa kuti ndiphe mwana wa mfumu. Paja mfumu idakulamulani inu ndi Abisai ndi Itai, ife tilikumva, kuti, ‘Mumtchinjirize mwanayo Abisalomu chifukwa cha ine.’
13
Bwenzi nditanyoza mau a mfumuwo, pomupha mwana wake, ndipo zikadadziŵika, poti palibe kanthu kobisika pamaso pa mfumu, ndipo inu nomwe simukadanditeteza.”
14
Apo Yowabu adati, “Ukunditayitsa nthaŵi!” Ndipo adatenga mikondo itatu m'manja mwake, nakabaya Abisalomu m'chifuŵa asanafe, akali lendee mu mtengo wa thunduwo.
15
Pomwepo ankhondo khumi onyamula zida zankhondo za Yowabu, adazinga Abisalomu, namkantha mpaka kumupha.
16
Pambuyo pake Yowabu adaliza lipenga loletsa nkhondo, ndipo ankhondo ake adabwerako kumene ankalondola Aisraele kuja.
17
Ndipo ankhondowo adatenga mtembo wa Abisalomu, nakautaya m'chidzenje chachikulu m'nkhalango, naunjika mulu wa miyala padzenjepo. Aisraele onse adathaŵa, aliyense kuthaŵira kwao.
18
Abisalomu akadali moyo, adaadzimangira chipilala m'chigwa cha mfumu, poti ankati, “Ine ndilibe mwana wamwamuna woti adzakhale chikumbutso cha dzina langa.” Adaatchula chipilalacho dzina lake lomwe, ndipo mpaka pano chikutchulidwa kuti chikumbutso cha Abisalomu.
19
Tsono Ahimaazi, mwana wa Zadoki, adati, “Imani ndithamange ndikauze mfumu nkhani yokondwetsayi yakuti Chauta waipulumutsa mfumuyo kwa adani ake.”
20
Yowabu adauza Ahimaaziyo kuti, “Iwe usakanene zimenezi lero. Ukanene zimenezi tsiku lina, koma lero usakanene mbiri iliyonse, chifukwa mwana wa mfumu waphedwa.”
21
Pambuyo pake Yowabu adauza Mkusi kuti, “Pita, ukauze mfumu zimene waziwonazi.” Mkusiyo adaŵeramira Yowabu mwaulemu, nayamba kuthamanga.
22
Zitatero, Ahimaazi uja, mwana wa Zadoki, adauzanso Yowabu kuti, “Zitanizitani, mundilole kuti inenso ndimthamangire Mkusi uja.” Yowabu adamufunsa kuti, “Mwana wanga, chifukwa chiyani ukuti uthamange, pamene sudzalandirapo mphotho chifukwa cha uthenga umenewo?”
23
Ahimaazi adati, “Zitanizitani, ine ndithamanga ndithu.” Apo Yowabu adamuuza kuti, “Chabwino, pita.” Choncho Ahimaazi adathamanga, kudzera njira yakuchigwa, nkumubzola Mkusi uja.
24
Nthaŵi imeneyo nkuti Davide atakhala pakati pa zipata ziŵiri, chakubwalo ndi cham'kati. Mlonda adakwera pa khoma nakaimirira pa denga la chipata. Adati atayang'ana, adaona munthu akuthamanga yekhayekha.
25
Ndipo mlondayo adafuula nauza mfumu. Mfumuyo idati, “Ngati ali yekhayekha, ndiye kuti ali ndi nkhani yabwino.” Tsono munthu uja adafika ndithu, nayandikira pafupi.
26
Mlondayo adaona munthu winanso akuthamanga. Ndipo adafuulira munthu wapachipata nati, “Onani, pali munthu winanso akuthamanga yekhayekha.” Apo mfumu idati, “Iyeyonso akubwera ndi nkhani yabwino.”
27
Mlonda uja adati, “Munthu akuthamanga patsogoloyo, kathamangidwe kake kakufanafana ndi m'mene amathamangira Ahimaazi, mwana wa Zadoki.” Mfumu idati, “Ameneyo ndi munthu wabwino, ndipo akubwera ndi nkhani yabwino.”
28
Tsono Ahimaazi adafuula kwa mfumu, kuti, “Nkwabwino!” Atatero adadzigwetsa pansi pamaso pa mfumu, nati, “Atamandike Chauta, Mulungu wanu, amene wapereka m'manja mwanu anthu amene adaaukira inu mbuyanga mfumu.”
29
Mfumu idamufunsa kuti, “Kodi mwana uja Abisalomu, zinthu zamuyendera bwino?” Ahimaazi adauza mfumu kuti, “Pamene Yowabu amandituma ine, kapolo wanu, ndinaona chipiringu chachikulu cha anthu, sindikudziŵa kaya kwagwa zotani.”
30
Pompo mfumu idati, “Patuka, kaime apo.” Iye adapatuka nakaima potero.
31
Mkusi uja nayenso adafika, ndipo adati, “Ndakutengerani uthenga wabwino, mbuyanga mfumu. Lero lino Chauta wakupulumutsani ku mphamvu za anthu onse amene ankakuukirani.”
32
Tsono mfumuyo idafunsa Mkusi uja kuti, “Kodi mwana uja Abisalomu zinthu zamuyendera bwino?” Mkusiyo adayankha kuti, “Adani anu mbuyanga mfumu, pamodzi ndi anthu onse amene amakuukirani, ziŵaonekere zomwe zamuwonekera mwanayo.”
33
Pamenepo mfumu idagwidwa ndi chisoni chachikulu, nikwera ku chipinda cham'mwamba pa chipata kukalira. Tsono popita inkati, “Iwe mwana wanga Abisalomu, mwana wanga Abisalomu. Kalanga ine, achikhala ndidaafa ndine m'malo mwako! Iwe Abisalomu mwana wanga, mwana wanga!”
← Chapter 17
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 19 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24