bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
2 Samuel 20
2 Samuel 20
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
← Chapter 19
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 21 →
1
Zidangochitika kuti kumeneko kunali munthu wina wachabechabe dzina lake Sheba, mwana wa Bikiri wa fuko la Benjamini. Iyeyo tsiku lina adaliza lipenga, nati, “Ife tilibe chathu mu ufumu wa Davide, tilibe choloŵa mwa mwana wa Yese! Inu Aisraele, aliyense apite kunyumba kwake!”
2
Choncho Aisraele onse adaleka kumtsata Davide, nayamba kutsata Sheba, mwana wa Bikiri. Koma anthu a ku Yuda adakhalabe nganganga pambuyo pa mfumu yao, kuyambira ku Yordani mpaka ku Yerusalemu.
3
Davide atafika ku nyumba yake ku Yerusalemu, adatenga azikazi ake khumi amene adaaŵasiya kuti azisunga mudzi, naŵatsekera m'nyumba m'mene adaaikamo mlonda woŵalonda. Ankaŵapatsa chakudya, koma Davide sankaloŵa m'nyumbamo kwa akaziwo. Adaŵatsekera m'nyumba choncho mpaka tsiku la kufa kwao, ndipo ankakhala ngati akazi amasiye.
4
Tsono mfumu idauza Amasa kuti, “Itanire anthu onse a ku Yuda, abwere kuno pasanapite masiku atatu, ndipo iweyo udzakhalepo.”
5
Motero Amasa adakaitana Ayuda. Koma adachedwa, napitiriza nthaŵi imene adaamuikira.
6
Pamenepo Davide adauza Abisai kuti, “Sheba, mwana wa Bikiri, adzativuta kwambiri kupambana Abisalomu. Tenga ankhondo anga mulondole Shebayo kuti angadzipezere mizinda yamalinga namativutitsa.”
7
Choncho Abisai uja, pamodzi ndi ankhondo a Yowabu, ndi Akereti, ndi Apeleti, ndi anyonga onse, adatuluka ku Yerusalemu kumalondola Sheba, mwana wa Bikiri.
8
Nthaŵi imene adafika ku mwala waukulu umene uli ku Gibiyoni, Amasa adabwera kudzakumana nawo. Tsono Yowabu adaavala malaya ankhondo, ndipo pamwamba pa malayawo m'chiwuno mwake, panali lamba womangirirapo lupanga lam'chimake. Pamene ankayenda, lidasololoka.
9
Tsono Yowabu adafunsa Amasa kuti, “Kodi nkwabwino mbale wanga?” Pamenepo Yowabuyo adamgwira ndevu Amasa uja ndi dzanja lake lamanja kuti amumpsompsone.
10
Koma Amasa sadaachenjera nalo lupanga limene linali m'dzanja lina la Yowabu. Pomwepo Yowabuyo adamubaya nalo lupangalo m'mimba kamodzi kokha, mpaka matumbo ake kukhuthuka, naafa pomwepo. Tsono Yowabu ndi Abisai mbale wake adalondola Sheba mwana wa Bikiri.
11
Wina mwa ankhondo a Yowabu adakaimirira pambali pa mtembo wa Amasa, nati, “Aliyense wokhumba Yowabu ndi Davide, mlekeni atsate Yowabuyo.”
12
Monsemo nkuti Amasa atagona pa mseu ndi kuvimvinizika m'magazi ake. Ndipo aliyense amene ankabwera, ankati akamuona, nkuima. Tsono munthu wa Yowabu uja ataona kuti anthu akuima, adanyamula Amasa uja, kumchotsa mumseumo, nakamuika ku thengo, nkumfunditsa chovala.
13
Amasayo atachotsedwa pamseupo, anthu onse adatsatira Yowabu, kuti alondole Sheba mwana wa Bikiri.
14
Sheba adapita ndithu kubzola mafuko onse a Aisraele mpaka kukafika ku Abele wa ku Betemaki. Abikiri onse adasonkhana, naloŵa naye mumzindamo.
15
Ndipo anthu onse amene anali ndi Yowabu adabwera, nadzamzinga ndi zithando zankhondo Shebayo ku Abele wa ku Betemaki. Tsono adauundira mitumbira yankhondo mzindawo, nikagunda ku linga. Choncho ankagumula khoma kuti aligwetse.
16
Ndiye mkazi wina wanzeru adayamba kuitana mumzindamo kuti, “Tamverani! Tamverani! Tauzani aYowabu abwere kuno kuti ndilankhule nawo.”
17
Yowabuyo adadza pafupi ndi mkaziyo, ndipo mkazi uja adamufunsa kuti, “Kodi inu ndinu aYowabu?” Yowabu adayankha kuti, “Ndine amene.” Mkaziyo adamuuza kuti, “Pepani bambo, mumvere mau anga.” Apo Yowabu adayankha kuti, “Inde, ndilikumva!”
18
Apo mkazi uja adati, “Paja anthu kale ankati, ‘Kapempheni nzeru ku Abele.’ Nkhani zao ankazitha motero.
19
Ife ndife anthu amtendere ndi okhulupirika m'dziko la Israele. Inu mukufuna kuwononga mzinda umene uli ngati mai m'dziko la Israele. Chifukwa chiyani mukuti mufafanize choloŵa cha Chauta?”
20
Yowabu adayankha kuti, “Iyai, ine sindikufuna konse kuwononga mzinda uno.
21
Cholinga si chimenechi. Koma munthu wina wa ku dziko la mapiri la Efuremu, dzina lake Sheba, mwana wa Bikiri, adaukira mfumu Davide. Mumpereke yekhayo, ndipo mzindawu ndiwuleka.” Mkazi uja adauza Yowabu kuti, “Tikuponyerani mutu wake pa khoma.”
22
Kenaka mkaziyo mwa nzeru zake adapita kwa anthu, naŵasimbira nkhaniyi. Choncho anthuwo adadula mutu wa Sheba, mwana wa Bikiri, namponyera Yowabu. Pamenepo Yowabu adaliza lipenga, ndipo ankhondo ake adachoka kumzindako, aliyense kupita kwao, ndipo Yowabu adabwerera ku Yerusalemu kwa mfumu.
23
Yowabu ankalamulira gulu lonse lankhondo la Aisraele. Ndipo Benaya, mwana wa Yehoyada, ankalamulira Akereti ndi Apeleti.
24
Adoniramu anali mkulu woyang'anira za thangata. Yehosafati, mwana wa Ahiludi, anali mlembi wolemba mbiri ya dziko.
25
Seva anali mlembi wa mfumu. Zadoki ndi Abiyatara anali ansembe.
26
Ndipo Ira Myairi nayenso anali wansembe wa Davide.
← Chapter 19
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 21 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24