bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
2 Samuel 23
2 Samuel 23
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
← Chapter 22
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 24 →
1
Naŵa mau otsiriza a Davide: Nayi nyimbo ya Davide, mwana wa Yese, mau a munthu amene Mulungu adamkweza pamwamba, amene Mulungu wa Yakobe adamdzoza kuti akhale mfumu, munthu wokonda kuimba nyimbo zokoma za Israele:
2
“Mzimu wa Chauta ukulankhula mwa ine, mau ake ali pakamwa panga.
3
Mulungu wa Israele walankhula, Thanthwe la Israele landiwuza kuti, ‘Munthu amene amalamulira anthu mwachilungamo, kuŵalamulira molemekeza Mulungu,
4
amaŵafikira ngati kuŵala kwam'maŵa amaŵaŵalira ngati dzuŵa lam'maŵa pa tsiku lamitambo. Alinso ngati mvula imene imameretsa udzu pa nthaka.’
5
Motero Mulungu adzadalitsa zidzukulu zanga chifukwa Iye adachita nane chipangano chosatha, chipangano cholongosoka bwino ndi chosasinthika. Izi nzimene ndikulakalaka, ndiponso zimene zidzandipulumutsa. Ndi Mulungu amene adzachita zonsezi.
6
Koma anthu oipa onse amachotsedwa ngati minga. Anthu satha kuigwira ndi manja.
7
Koma amaidula ndi chigwandali nakaitentha pa moto.”
8
Naŵa maina a ankhondo amphamvu a Davide: Yosebu-Basebeti, wa ku Takemoni, mkulu wa atsogoleri ankhondo atatu. Iye adaamenyana nkhondo ndi anthu 800, naŵapha onsewo ndi mkondo wake.
9
Mnzake wotsatana naye mwa anthu atatu amphamvu aja anali Eleazara, mwana wa Dodo, mwana wa Aho. Iyeyo anali pamodzi ndi Davide pamene ankaputa Afilisti omwe adaasonkhana kuti amenyane naye nkhondo ku Pasi-Damimu. Aisraele anali atathaŵa.
10
Koma iyeyo adatsalira, nakantha Afilisti mpaka dzanja lake kuchita kutopa, komabe osataya lupanga. Tsiku limenelo Chauta adampambanitsa. Aisraelewo adabwerera pambuyo pake kudzangofunkha za ophedwawo.
11
Wotsatana ndi ameneyo anali Sama, mwana wa Age Muharari. Nthaŵi ina Afilisti adasonkhana ku Lehi kumene kunali munda wa mphodza. Aisraele nkuthaŵa Afilisti aja.
12
Koma iyeyo adaima pakatimpakati pa mundawo nautchinjiriza, ndipo adapha Afilistiwo, chifukwa Chauta adampambanitsa kwambiri.
13
Nthaŵi yokolola, atatu mwa ankhondo otchuka makumi atatu aja, adapita kwa Davide ku phanga la Adulamu, pamene gulu lankhondo la Afilisti linkamanga zithando zankhondo ku chigwa cha Refaimu.
14
Pamenepo nkuti Davide ali m'phanga muja, ndipo kagulu kankhondo ka Afilisti kali ku Betelehemu.
15
Tsono Davide adalankhula molakalaka kuti, “Ha, wina akadandipatsa madzi akumwa a m'chitsime chimene chili ku chipata ku Betelehemu kuti ndimwe!”
16
Pamenepo anthu atatu amphamvu aja adapita, nabzola zithando za Afilisti, nkutunga madzi m'chitsime cha ku Betelehemu, chimene chinali pafupi ndi chipata. Adatenga madziwo, nabwera nawo kwa Davide. Koma Davideyo sadafune kumwako madziwo adangoŵathira pansi, kuŵapereka kwa Chauta,
17
nati, “Ndithudi pali Chauta, sindingachite chinthu chotere, chifukwa kukhala ngati kumwa magazi a anthuŵa amene adaika moyo wao paminga.” Motero adakana kumwa madziwo. Zimenezi ndizo adachita anthu atatu amphamvu aja.
18
Tsono Abisai, mbale wa Yowabu, mwana wa Zeruya, ndiye anali mtsogoleri wa anthu makumi atatu aja. Ndiye adapha anthu 300 ndi mkondo wake, nakhala wotchuka ngati anthu atatu ena aja.
19
Iyeyo anali womveka kwambiri mwa atsogoleri makumi atatu aja, ndipo adasanduka mkulu wao. Komabe sadafikepo pa anthu atatu aja.
20
Benaya mwana wa Yehoyada, wa ku Kabizeele, anali munthu wolimba mtima amene ankachita ntchito zamphamvu. Iyeyo adapha ankhondo aŵiri otchuka a ku Mowabu. Tsiku lina chisanu cha mbee chitagwa, adatsikira m'chitsime, naphamo mkango.
21
Adaphanso Mwejipito wina, wa maonekedwe okongola. Mwejipitoyo adaali ndi mkondo m'manja, koma Benaya adapita kwa iyeyo ndi ndodo chabe. Adalanda mkondowo ku manja mwa Mwejipito uja, namupha ndi mkondo wake womwewo.
22
Zimenezi ndi ntchito zimene adatchuka nazo Benaya mwana wa Yehoyada, yemwe anali m'modzi wa anthu makumi atatu amphamvu aja.
23
Iyeyo anali womveka pakati pa atsogoleri makumi atatu aja, komabe sadafikepo pa anthu atatu aja. Davide adamuika kuti azilamulira asilikali ake omuteteza.
24
M'gulu la anthu makumi atatu aja munalinso aŵa: Asahele, mbale wa Yowabu, Elihanani, mwana wa Dodo, wa ku Betelehemu,
25
Sama wa ku Harodi, Elika wa ku Harodi
26
Helezi Mpeleti, Ira mwana wa Ikesi wa ku Tekowa,
27
Abiyezere wa ku Anatoti, Mebunai Muhusa,
28
Zalimoni Mwahohi, Maharai wa ku Netofa,
29
Helebi mwana wa Baana wa ku Netofa, Itai mwana wa Ribai wa ku Gibea, Mbenjamini.
30
Panalinso Benaya wa ku Piratoni, Hidai wa ku mitsinje ya ku Gaasi,
31
Abiyaliboni Mwaraba, Azimaveti wa ku Bahurimu,
32
Eliyaba wa ku Saaliboni, ana a Yaseni, Yonatani,
33
Sama Muharari, Ahiyamu mwana wa Sarara Muharari,
34
Elipeleti mwana wa Ahasibai wa ku Maaka, Eliyamu mwana wa Ahitofele wa ku Gilo,
35
Heziro wa ku Karimele, Paarai Mwaraba,
36
Igala mwana wa Natani wa ku Zoba, Bani Mgadi,
37
Zeleki Mwamoni, Naharai wa ku Beeroti, wonyamula zida za Yowabu, mwana wa Zeruya,
38
Ira Mwitiri ndi Garebu Mwitiri ndi
39
Uriya Muhiti uja. Onse pamodzi anali anthu 37.
← Chapter 22
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 24 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24