bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
2 Samuel 12
2 Samuel 12
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
← Chapter 11
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 13 →
1
Pambuyo pake Chauta adatuma mneneri Natani kwa Davide. Natani atafika kwa Davide, adamphera fanizo lakuti, “Mu mzinda wina munali anthu aŵiri, wina wolemera, wina wosauka.
2
Wolemerayo anali ndi nkhosa zambiri ndi ng'ombenso zambiri.
3
Koma wosauka uja analibe nkanthu komwe kupatula kankhosa kakakazi kamodzi, kamene adaagula. Ndipo adakaŵeta kankhosako, mpaka kukula kali ndi iyeyo pamodzi ndi ana ake. Kankadyako chakudya chake cha munthuyo, mpaka kumamwera m'chikho chake. Kankagona pakhundu pake pa munthuyo, ndipo kankakhala ngati mwana wake wamkazi.
4
Tsiku lina kunyumba kwa munthu wolemera uja kudafika mlendo. Munthu uja sadafune kutengako imodzi mwa nkhosa zake kapena imodzi mwa ng'ombe zake, kuti aphere mlendo wakeyo. M'malo mwake adakatenga nkhosa ya munthu wosauka uja, naphera mlendo amene adaadzamuchezera uja.” Atamva za munthuyo, Davide adapsa mtima kwambiri.
5
Adauza Natani kuti, “Pali Chauta wamoyo, munthu amene adachita zimeneziyu, ayenera kuphedwa basi.
6
Ndipo pa mwanawankhosayo abwezere ena anai, chifukwa chochita zotere, ndiponso popeza kuti analibe chifundo.”
7
Apo Natani adauza Davide kuti, “Munthuyotu ndinu amene. Chauta, Mulungu wa Israele, akunena kuti, ‘Ine ndidakudzoza kuti ukhale mfumu ya Aisraele, ndipo ndidakupulumutsa kwa Saulo.
8
Ndidakupatsa banja la mbuyako, kudzanso akazi a mbuyako kuti akhale m'manja mwako, ndipo ndidakupatsanso mtundu wa Israele pamodzi ndi fuko la Yuda. Tsono zimenezi zikadakuchepera, ndikadakuwonjezera zina zambiri.
9
Chifukwa chiyani tsono wanyoza mau a Chauta, nuchita choipa pamaso pake? Wapha Uriya Muhiti ndi lupanga, ndipo wakwatira mkazi wake. Wamuphetsa Uriyayo kudzera mwa Aamoni.
10
Nchifukwa chake tsono nkhondo siidzachoka pabanja pako chifukwa wandinyoza Ine, ndipo wakwatira mkazi wa Uriya Muhiti.
11
Tsono Ine Chauta ndikuti, ndithu ndidzakugwetsera tsoka pabanja pako pomwepo. Ndidzakuchotsera akazi ako, iweyo ukupenya, ndi kuŵapereka kwa mnzako wina, ndipo adzagona nawo akazi ako dzuŵa likuwomba mtengo.
12
Iwe unkachita zimenezo m'seri, koma Ine ndidzazichita pamaso pa Aisraele onse, masana ndithu.’ ” Apo Davide adauza Natani kuti,
13
“Ndidachimwira Chauta.” Natani adati, “Chauta wakukhululukirani machimo anu, simufa.
14
Komabe, popeza kuti pochita zimenezi mwanyoza Chauta kotheratu, mwana amene akubalireniyo adzafa.”
15
Pompo Natani adabwerera kunyumba kwake. Motero Chauta adalanga mwana amene mkazi wa Uriya adabalira Davide, ndipo adadwala kwambiri.
16
Nchifukwa chake Davide adapempherera mwanayo kwa Mulungu. Adaleka kudya, nakaloŵa m'nyumba, nkukagona pansi usiku wonse.
17
Akuluakulu a ku nyumba ya mfumu adadzaima pambali pake kuti amuutse. Koma iye adakana kuuka, ndipo sadadye nawo chakudya anthuwo.
18
Pa tsiku lachisanu ndi chiŵiri, mwanayo adamwalira. Atumiki a Davide adaopa kukamuuza kuti mwanayo wafa. Adati, “Pamene mwanayo anali moyo, tinkalankhula naye Davide, koma sankatimvera. Tsono tingathe kukamuuza bwanji lero kuti mwana wafa? Mwina nkudzipweteka.”
19
Koma pamene Davide adaona kuti atumiki ake akunong'onezana, adadziŵa kuti mwana uja wafa. Choncho adafunsa atumiki ake aja kuti, “Kodi mwana uja watisiya?” Atumikiwo adati, “Inde, watisiyadi.”
20
Apo Davide adadzuka pansi paja, ndipo adakasamba, nadzola mafuta, nkusintha zovala zake. Tsono adakaloŵa m'nyumba ya Chauta, nakapembedza. Pambuyo pake adapita kunyumba kwake, naitanitsa chakudya. Ndipo anthu atabwera nacho, iye adadya.
21
Tsono atumiki ake aja adamufunsa kuti, “Tatifotokozerani, kodi zimene mwachitazi nzotani? Pamene mwana uja anali moyo, inu munkakana kudya. Koma pamene adamwalira, inu mudadzuka, nkuyamba kudya.”
22
Davide adati, “Pamene mwanayo anali moyo, ndinkakana zakudya ndipo ndinkalira, poti ndinkati, ‘Sizidziŵika, mwina kapena Chauta nkundikomera mtima, kuti mwanayo akhale moyo?’
23
Koma tsopano mwanayo wafa. Nanga ndizikaniranjinso zakudya? Kodi ndingathe kumbwezanso? Ine ndidzapitadi kumene kuli iyeko, koma iyeyo sadzabwereranso kwa ine.”
24
Tsono Davide adatonthoza mtima wa mkazi wake Bateseba, nakaloŵa kwa mkaziyo. Pambuyo pake mkazi uja adabala mwana wamwamuna, ndipo Davide adamutcha dzina lake Solomoni. Chauta adamkonda mwanayo,
25
ndipo adatumiza mau kudzera mwa mneneri Natani kuti mwanayo dzina lake likhale Yedidiya, chifukwa Chauta adaamkonda.
26
Nthaŵi imeneyo Yowabu ndi ankhondo a Aisraele ankathira nkhondo Raba, likulu la Aamoni, ndipo anali pafupi kuulanda.
27
Adatuma amithenga kwa Davide kukamuuza kuti, “Ndauthira nkhondo mzinda wa Raba, ndipo ndalanda nkhokwe yake ya madzi.
28
Tsono inu musonkhanitse ankhondo onse otsala, ndipo bwerani mudzauzinge ndi zithando mzindawo ndi kuulanda, kuwopa kuti ine ndikalanda mzindawo, ungamatchedwe dzina langa.”
29
Choncho Davide adasonkhanitsa ankhondo ake onse, ndipo adapita ku Raba, nakauthira nkhondo mzindawo, nkuulanda.
30
Tsono Davide adaivula chisoti kumutu mfumu ya Aamoni. Chisoticho chinkalemera makilogramu agolide, ndipo pa chisotipo panali mwala wamtengowapatali. Davide adachivala chisoticho, natenga zofunkha zochuluka mumzindamo.
31
Adaŵatulutsa anthu amumzindamo, nakaŵagwiritsa ntchito ndi masowo ndi mapiki ndi nkhwangwa, ndi kuŵaumbitsa njerwa. Umu ndimo m'mene adachitira ndi mizinda yonse ya Aamoni. Pambuyo pake Davide adabwerera ku Yerusalemu pamodzi ndi ankhondo onse.
← Chapter 11
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 13 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24