bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
2 Samuel 10
2 Samuel 10
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
← Chapter 9
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 11 →
1
Pambuyo pake Nahasi mfumu ya Aamoni adamwalira, ndipo Hanuni mwana wake adaloŵa ufumu m'malo mwake.
2
Tsono Davide adati, “Ndidzakhala naye mokhulupirika Hanuni, mwana wa Nahasi, monga momwe bambo wake adaandichitira zabwino.” Motero Davide adatuma atumiki kuti akampepese Hanuni chifukwa cha imfa ya bambo wake. Tsono atumiki a Davidewo adakafika m'dziko la Aamoni.
3
Koma akalonga a Aamoni adafunsa Hanuni mbuyawo kuti, “Kodi mukuganiza kuti m'mene Davide wakutumizirani anthu odzakupepesanimu, ndiye kuti akuchitira bambo wanu ulemu? Osati Davide watuma atumiki akewo kwa inu kuti adzafufuze ndi kuzonda mzindawu, ndipo kuti akauwona, auwononge?”
4
Choncho Hanuni adagwira atumiki a Davide aja, naŵameta ndevu mwachiperengedzu. Kenaka adaŵadulira zovala zao pakati mpaka m'chiwuno, naŵabweza kwao.
5
Tsono Davide adamva zimenezo, adatuma anthu kuti akaŵachingamire, chifukwa iwowo anali ndi manyazi kwambiri. Ndipo mfumu idati, “Mukaŵauze kuti abakhala ku Yeriko mpaka ndevu zitamera, pambuyo pake ndiye adzabwere kuno.”
6
Tsono Aamoni atazindikira kuti adziputira mkwiyo wa Davide, adatuma anthu kukalemba ntchito Asiriya a ku Beterehobu ndi a ku Zoba, ankhondo apansi okwanira 20,000. Adalembanso mfumu ya ku Maaka ndi anthu ake okwanira 1,000, ndiponso anthu a ku Tobu okwanira 12,000.
7
Davide atamva zimenezo, adatuma Yowabu ndi gulu lake lonse la ankhondo, amphamvu okhaokha.
8
Pamenepo Aamoni adatuluka nandanda pa mizere yankhondo pa khomo la chipata cha mzinda. Koma Asiriya a ku Zoba ndi a ku Rehobu, ndiponso anthu a ku Tobu ndi a ku Maaka, anali paokha ku malo opanda mitengo.
9
Yowabu ataona kuti nkhondo yamkhalira kumaso ndi kumbuyo komwe, adasankhula ankhondo amphamvu pakati pa Aisraele, naŵandanditsa moyang'anana ndi Asiriyawo.
10
Anthu ena onse otsala adaŵaika m'manja mwa Abisai, mbale wake, ndipo adaŵandanditsa moyang'anana ndi Aamoni.
11
Tsono Yowabu adauza Abisai kuti, “Ngati Asiriya andipose mphamvu, iweyo udzandithandize. Koma ngati Aamoni akupose mphamvu, ndiye kuti ineyo ndidzabwera kudzakuthandiza.
12
Limba mtima, ndipo tichite chamuna chifukwa cha anthu athu, ndiponso chifukwa cha mizinda ya Mulungu wathu. Chauta achite zimene zimkomere.”
13
Choncho Yowabu ndi anthu ake adasendera pafupi ndi Asiriya aja kuti amenyane nawo nkhondo, koma Asiriyawo adathaŵa iye akufika.
14
Tsono Aamoni ataona kuti Asiriya athaŵa, nawonso adathaŵa pofika Abisai, nakaloŵa mu mzinda. Apo Yowabu adaleka kumenyana ndi Aamoni, nabwerera ku Yerusalemu.
15
Koma Asiriya ataona kuti agonjetsedwa ndi Aisraele, adasonkanitsa ankhondo ao onse.
16
Hadadezere mfumu yao adatuma amithenga kuti akabwere nawo Asiriya anzao amene anali patsidya pa mtsinje wa Yufurate. Ndipo adafika nawo ku Helamu pamodzi ndi Sobaki, mtsogoleri wa ankhondo wa Hadadezere.
17
Davide atamva zimenezi, adasonkhanitsa ankhondo onse a Aisraele, naoloka mtsinje wa Yordani, nakafika ku Helamu. Apo Asiriya adandanda kuti alimbane ndi Davide, ndipo adamenyana nayedi.
18
Koma pambuyo pake Asiriyawo adathaŵa, kuthaŵa Aisraele. Pamenepo Davide adapha anthu apa magaleta okwanira 700, ndi ankhondo okwera pa akavalo okwanira 40,000. Adamvulaza kwambiri Sobaki, mtsogoleri wa gulu lao la ankhondo uja, kotero kuti adafera pomwepo.
19
Tsono mafumu onse amene ankatumikira Hadadezere, ataona kuti agonjetsedwa ndi Aisraele, adapangana nawo za mtendere, ndipo adayamba kutumikira Aisraelewo. Motero Asiriya nawonso adaopa kumathandizanso Aamoniwo.
← Chapter 9
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 11 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24