bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
2 Samuel 13
2 Samuel 13
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
← Chapter 12
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 14 →
1
Abisalomu mwana wa Davide, anali ndi mlongo wake wokongola, dzina lake Tamara. Aminoni, mwana wina wa Davide, ankakonda Tamara.
2
Iye sankagona tulo chifukwa cha Tamara mlongo wake, mpaka kuchita kudwala. Tamarayo anali namwali wosadziŵa mwamuna, ndipo kunkaoneka kuti chinali chosatheka kuti Aminoniyo amchite chilichonse.
3
Koma Aminoni anali ndi bwenzi lake, dzina lake Yonadabu, mwana wa Simea, mbale wake wa Davide. Yonadabuyo anali munthu wochenjera kwambiri.
4
Tsiku lina Yonadabu adafunsa Aminoni kuti, “Kodi iwe, mwana wa mfumu, chifukwa chiyani umaoneka woonda m'maŵa masiku onse? Bwanji osandiwuza ine?” Aminoni adamuyankha kuti, “Ine ndikukonda Tamara, mlongo wa mkulu wanga Abisalomu.”
5
Tsono Yonadabu adamuuza kuti, “Kagone pabedi pako, ndipo uchite ngati wadwala. Bambo wako akafika kuti adzakuwone, umuuze kuti, ‘Mloleni Tamara, mlongo wanga, abwere andikonzere chakudya kuti ndidye. Adzandikonzere chakudyacho konkuno, ine ndikupenya, kuti ndichiwone, ndipo ndidzadyere m'manja mwake.’ ”
6
Choncho Aminoni adagona, nachita ngati wadwala. Mfumu itabwera kudzamuwona, Aminoniyo adauza mfumuyo kuti, “Chonde, mulole mlongo wanga Tamara abwere, kuti adzandiphikire chakudya ine ndikupenya, kuti ndidzadyere m'manja mwake.”
7
Davide adatumiza mau kwa Tamara kuti, “Upite kunyumba kwa mbale wako Aminoni, ukamphikire chakudya.”
8
Tamara adapitadi kunyumba kwa mbale wake Aminoni ku malo kumene ankagona. Adatenga ufa, naukanda, naumba makeke, Aminoniyo akupenya, ndipo adaphika makekewo.
9
Tsono adatenga chiwaya, nakhuthula makekewo, iye akupenya, koma Aminoniyo adakana kudya. Ndipo Aminoni adati, “Uzani anthu onse achoke.” Choncho anthu onse adachoka.
10
Tsono Aminoni adauza Tamara kuti, “Bwera nacho chakudya chija m'chipinda muno kuti ndidzadyere m'manja mwako.” Tamara adatenga makeke amene adaaphikawo, napita nawo kwa Aminoni, mbale wake, m'chipindamo.
11
Koma atafika nacho chakudyacho pafupi ndi Aminoni kuti adye, Aminoni adamgwira Tamara, namuuza kuti, “Bwera ugone nane, iwe Tamara.”
12
Koma Tamarayo adayankha kuti, “Iyai, mlongo wanga, usandikakamize. Zimenezi sizidachitikepo nkale lonse ku Israele. Usachite zauchitsiru zotere.
13
Kodi ine sindidzachita manyazi poyenda pakati pa anthu? Ndipo iwe udzakhala mmodzi mwa zitsiru pakati pa Aisraele. Nchifukwa chake tsono, chonde, ndapota nawe, ulankhule ndi amfumu, poti iwowo sadzandikaniza kuti ndikwatiwe nawe.”
14
Koma Aminoni sadamve zimene ankanena Tamarazo. Ndipo popeza kuti anali ndi mphamvu zoposa Tamara, Aminoniyo adamkakamiza Tamarayo nagona naye.
15
Pambuyo pake Aminoni adayamba kudana naye kwabasi Tamarayo, kotero kuti chidani chake ndi Tamara chidakula kwambiri kuposa chikondi chimene adaamkonda nacho. Ndipo Aminoniyo adauza Tamara kuti, “Dzuka, kazipita.”
16
Koma Tamarayo adati, “Iyai, mlongo wanga, kundipirikitsa chotere nkulakwa koposa zimene wandichitazi.” Koma Aminoni sadafune kumva zimene ankanena Tamarazo.
17
Pomwepo Aminoniyo adaitana mnyamata amene ankamtumikira, namuuza kuti, “Mtulutse mkaziyu, achoke pano, ndisamuwonenso, ndipo upiringidze chitseko iyeyo akatuluka.”
18
Nthaŵi imeneyo Tamara adaavala deresi lalitali, la manja aatali, monga momwe ankavalira ana achinamwali a mfumu, amene sadadziŵeko amuna. Tsono mnyamata wa Aminoni uja adatulutsa Tamara, napiringidza chitseko mkaziyo atatuluka.
19
Ndipo Tamara adadzithira phulusa kumutu, nang'amba chovala chake chachitali chimene adaavala. Ndipo adagwirira manja kumutu, namapita akulira mokweza njira yonse.
20
Apo Abisalomu, mlongo wa Tamarayo, adamufunsa kuti, “Monga Aminoni uja wakuchimwitsa? Komabe, iwe khala phee, mlongo wanga. Iye uja ndi mlongo wako. Zimenezi usavutike nazo.” Choncho Tamara ankakhala ngati wofedwa kunyumba kwa mlongo wake Abisalomu.
21
Davide atazimva zimenezi, adapsa nazo mtima zedi.
22
Koma Abisalomu sadanenepo kanthu kalikonse kabwino kapena koipa kwa Aminoni. Pakuti Abisalomuyo adaamuzonda kwambiri Aminoni chifukwa choti adaakakamiza Tamara mlongo wake kuchita naye zoipa.
23
Patapita zaka ziŵiri zathunthu, Abisalomu anali ndi anthu ake ku ntchito yometa nkhosa ku Baala-Hazori pafupi ndi Efuremu. Tsono adaitana ana aamuna onse a mfumu kuti akakhaleko.
24
Adapita kwa mfumu nati, “Amfumu, ine mtumiki wanu ndikukachita ntchito yometa nkhosa ndi anthu anga. Ndimati ngati nkotheka mudzakhale nafe inuyo amfumu pamodzi ndi atumiki anu.”
25
Koma mfumu idauza Abisalomu kuti, “Iyai, mwana wanga, tisachite kupita tonse, tingakakuvutitse.” Adayesera muno ndi muno kumuumiriza, komabe Davide sadapite nao, m'malo mwake adangomdalitsa Abisalomuyo.
26
Tsono Abisalomu adati, “Chabwino, ngati inu simupita, bwanji apite nao ndi mbale wanga Aminoniyu.” Apo mfumu idafunsa kuti, “Chifukwa chiyani ukufuna kuti iyeyu apite nao?”
27
Koma Abisalomu adamkakamiza ndithu mpaka Davide adalola kuti Aminoni pamodzi ndi ana onse aamuna a mfumu apite nao.
28
Tsono Abisalomu adalamula antchito ake kuti, “Muwonetsetse nthaŵi imene Aminoni akhale ataledzera ndi vinyo. Ndikakuuzani kuti, ‘Kanthani Aminoni!’ Pomwepo mumuphe. Musaope, nanga sindine ndakulamulani? Mulimbe mtima, ndipo muchite chamuna.”
29
Choncho atumiki a Abisalomu adamchita Aminoni monga momwe adaaŵalamulira Abisalomu. Zitatero, ana onse aamuna a mfumu adadzambatuka, aliyense adakwera pa bulu wake, nathaŵa.
30
Koma anthuwo akali m'njira, Davide adamva mphekesera zakuti Abisalomu wapha ana onse aamuna a mfumu, ndipo palibe ndi mmodzi yemwe amene watsalako.
31
Pompo mfumu idadzuka, ning'amba zovala zake, nkudzigwetsa pansi. Atumiki ake onse amene anali pafupi naye, nawonso adang'amba zovala zao.
32
Koma Yonadabu, mwana wa Simea, mbale wa Davide, adati, “Mbuyanga, musaganize kuti ana onse a inu mfumu aphedwa, Aminoni yekha ndiye waphedwa. Zimenezi zachitika poti nzimene Abisalomu adaatsimikiziratu kale, kuyambira pa tsiku limene Aminoni adakakamiza Tamara, mlongo wa Abisalomu, kuchita naye zoipa.
33
Nchifukwa chake tsono mbuyanga mfumu, musavutike ndi maganizo oti ana anu onse aamuna aphedwa. Aminoni yekha ndiye waphedwa.”
34
Nthaŵi imeneyo nkuti Abisalomu atathaŵa. Tsono mlonda wapalinga poyang'ana, adangoona anthu ambiri akuchokera ku mseu wa Horonaimu, m'mbali mwa phiri.
35
Atamva zimenezi Yonadabu adauza mfumu kuti, “Ana a mfumu abwera. Amfumu, monga momwe ndinakuuzirani muja, ndi m'mene zayendera.”
36
Tsono atangomaliza kulankhula, adangoona ana a mfumu akubwera, ndipo anawo adayamba kubuma maliro. Pomwepo mfumuyo nayonso idalira kwambiri pamodzi ndi atumiki ake.
37
Abisalomu adathaŵa ndithu napita kwa Talimai, mwana wa Amihudi, mfumu ya ku Gesuri. Ndipo Davide adalira maliro a mwana wake Aminoni nthaŵi yaitali.
38
Abisalomu adakhala ku Gesuri zaka zitatu.
39
Tsono mfumu Davide adagwidwa ndi chifundo chofuna kumlondola Abisalomuyo. Pamenepo nkuti Davideyo atatonthozedwa pa imfa ya Aminoni.
← Chapter 12
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 14 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24