bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
2 Samuel 14
2 Samuel 14
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
← Chapter 13
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 15 →
1
Yowabu, mwana wa Zeruya, adaadziŵa kuti mtima wa mfumu uli pa Abisalomu.
2
Tsono adatuma anthu ku Tekowa kukatengako mkazi wanzeru kumeneko. Adauza mkaziyo kuti, “Ukhale ngati mfedwa, uvale zovala zaumasiye. Usadzole mafuta, koma ukhale ngati mkazi amene wakhala akulira masiku ambiri.
3
Ukatero upite kwa mfumu, ukalankhule nayo izi, izi.” Choncho Yowabu adauza mkaziyo mau oti akanene.
4
Mkazi wa ku Tekowayo atafika kwa mfumu, adadzigwetsa pansi, nalambira mfumu, ndipo adati, “Pepani amfumu, thandizeni.”
5
Mfumuyo idamufunsa kuti, “Chikukuvutani nchiyani, mai?” Mkaziyo adayankha kuti, “Ha! Munthune ndine mkazi wamasiye. Mwamuna wanga adafa.
6
Ndiye ine mdzakazi wanu ndinali ndi ana aamuna aŵiri, anawo ankamenyana kuminda. Panalibe wina aliyense woti aŵaleretse, choncho wina adakantha mnzake mpaka kumupha.
7
Tsono banja lonse landiwukira ine mdzakazi wanu, akunena kuti, ‘Utipatse mwana wako amene adapha mbale wake, kuti ife timuphe chifukwa cha mbale wake amene iye adaphayo.’ Motero anthuwo adzaononganso mloŵachuma. Anthuwo adzapha mwana wanga amene wanditsalira, ndipo dzina la mwamuna wanga silidzakumbukika, pakuti sipadzakhalanso mwana pa banja lathu.”
8
Apo mfumu idauza mkazi uja kuti, “Mai, pitani kunyumba kwanu, ndichitapo kanthu ineyo pa nkhaniyi.”
9
Mkazi wa ku Tekowa uja adauza mfumu kuti, “Inu amfumu, mlandu umenewu ugwere ine ndi banja la bambo wanga, inuyo mukhale osalakwa pamodzi ndi banja lanu lonse.”
10
Apo mfumu idati, “Ngati wina aliyense akunenerani kanthu kena kalikonse, mubwere naye kwa ine, ndipo sadzakuvutitsaninso.”
11
Tsono mkazi uja adanena kuti, “Chonde, amfumu mupemphe kwa Chauta Mulungu wanu, kuti wolipsira imfa ija asaphenso wina, kuti choncho mwana wanga asaonongeke.” Davide adati, “Pali Chauta wamoyo, mwana wanu sadzapwetekedwa mpang'ono pomwe.”
12
Tsono mkaziyo adati, “Chonde, mulole kuti ine mdzakazi wanu ndilankhule mau ena kwa inu mbuyanga mfumu.” Mfumuyo idamuuza kuti, “Lankhulani, mai.”
13
Apo mkazi uja adafunsa kuti, “Chifukwa chiyani nanga mwaganiza zoŵachita zinthu zotere anthu a Mulungu? Chifukwatu pochita zimenezi inu amfumu mwadziimba mlandu nokha, malinga nkuti simudaitanitse wopirikitsidwa uja kuti abwererenso kwao.
14
Paja madzi akatayika saoleka, ndiye tonsefe tiyenera kufa ndithu. Koma Mulungu safuna kuti moyo wa munthu utayike, tsono amakonza njira yakuti wopirikitsidwa asakhale wotayikiratu chonse.
15
Ndiye ine ndafika kuti ndidzalankhule ndi inu amfumu. Mwina mwake mungathe kudzachita zimene mdzakazi wanune ndikupempha.
16
Ndimaganiza kuti inu amfumu mutazimva, mudzandipulumutsa kwa munthu amene afuna kundiwononga ine pamodzi ndi mwana wanga, potero nkutichotsa pa kadziko kathu kamene adatipatsa Mulungu.
17
Choncho ine mdzakazi wanu ndidaaganiza kuti mau anu mbuyanga mfumu adzandipulumutsa, poti inu muli ngati mngelo wa Mulungu, podziŵa zabwino ndi zoipa. Chauta Mulungu wanu akhale nanu.”
18
Apo mfumu idamuyankha mkaziyo kuti, “Musandibisire kanthu kalikonse pa zimene ndikufunseni.” Mkazi uja adati, “Ai ndithu, mbuyanga mfumu sindikubisirani.”
19
Tsono mfumuyo idafunsa kuti, “Kodi zimenezi Yowabu sakuzidziŵa?” Mkaziyo adayankha kuti, “Pali inu nomwe, mbuyanga mfumu, palibe munthu amene angathe kupewa kuyankha chilichonse chimene inu mwafunsa. Kunena zoona, mtumiki wanu Yowabu ndiye amene adandiwuza kuti ndichite zimenezi. Iyeyo ndiye adandiwuza ine mdzakazi wanu mau onseŵa.
20
Mtumiki wanu Yowabu adachita zimenezi kuti asinthe mayendedwe ake a zinthu. Koma inu mbuyanga muli ndi nzeru zonga za mngelo wa Mulungu, mutha kudziŵa zinthu zonse za pa dziko lapansi.”
21
Pambuyo pake mfumu idauza Yowabu kuti, “Chabwino tsono, ndavomera kuti zimenezi zichitike. Pita, kamtenge mnyamata uja Abisalomu.”
22
Yowabu adaŵerama pansi, adalambira mfumu, naithokoza. Tsono adati, “Tsopano ndadziŵa kuti inu mbuyanga mfumu mwandikomera mtima, chifukwa mwavomera pempho langali.”
23
Choncho Yowabu adanyamuka, adapita ku Gesuri, nakatenga Abisalomu, nkubwera naye ku Yerusalemu.
24
Komabe mfumu idati, “Akhale payekha m'nyumba yakeyake. Asabwere pamaso panga.” Motero Abisalomu adakhala pa yekha m'nyumba yakeyake, osafika pamaso pa mfumu.
25
M'dziko lonse la Israele panalibe munthu wina aliyense wokongola ndi wochititsa kaso ngati Abisalomu. Kuyambira kumapazi mpaka kumutu analibe chilema chilichonse.
26
Chaka chilichonse ankameta tsitsi lake, chifukwa linkamlemera kwambiri. Ankati akalimeta Abisalomuyo, naliyesa pa sikelo tsitsilo, linkalemera makilogramu aŵiri, potsata muyeso wa mfumu.
27
Abisalomu anali ndi ana aamuna atatu, ndi mwana wamkazi mmodzi, dzina lake Tamara. Iyeyu anali mkazi wokongola.
28
Choncho Abisalomu adakhala zaka ziŵiri zathunthu mu Yerusalemu, osaonekera kwa mfumu.
29
Tsiku lina adatumiza mau kwa Yowabu opempha kuti amtume kwa mfumu. Koma Yowabu sadafike. Abisalomu adatumizanso mau kachiŵiri, koma Yowabu osafika ndithu.
30
Pamenepo Abisalomu adauza atumiki ake kuti, “Munda wa Yowabu uli pafupi ndi wanga, ndipo ali ndi barele m'menemo. Pitani kautentheni.” Pompo atumiki a Abisalomu adapita kukautentha mundawo.
31
Tsono Yowabu adanyamuka kupita kunyumba kwa Abisalomu, nakamufunsa kuti, “Bwanji atumiki ako atentha munda wanga?”
32
Abisalomu adayankha kuti, “Taona, ine ndinkatumiza mau kwa iwe kuti ndidzakutume kwa mfumu kukaifunsa kuti chifukwa chiyani ndidachoka ku Gesuri kubwera kuno? Kunali kwabwino koposa kuti ine ndizikhalabe konkuja.” Abisalomu adapitirira nati, “Ndipite basi kwa mfumu. Ngati ndili ndi cholakwa, mfumuyo ikandiphe.”
33
Apo Yowabu adapita kwa mfumu, nakakambira mfumuyo zimenezo. Tsono mfumu idaitana Abisalomu. Iye adabwera kwa mfumu, nadzigwetsa pansi pamaso pa mfumu. Ndipo mfumuyo idamlandira bwino pakumumpsompsona.
← Chapter 13
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 15 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24