bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
2 Samuel 9
2 Samuel 9
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
← Chapter 8
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 10 →
1
Tsiku lina Davide adafunsa kuti, “Kodi alipo wina aliyense wa banja la Saulo amene adatsalako? Ndikufuna kuti ndimchitire chifundo chifukwa cha Yonatani.”
2
Panali mtumiki wina wa banja la Saulo, dzina lake Ziba. Ameneyo adamuitana kuti apite kwa Davide. Tsono mfumu idamufunsa kuti, “Kodi iwe ndiwe Ziba?” Iye adayankha kuti, “Ndine amene, mtumiki wanu.”
3
Apo mfumu idamufunsa kuti, “Kodi palibe wina aliyense wa pa banja la Saulo amene adatsalako? Ndikufuna kuti ndimchitire chifundo monga momwe ndidalonjezera kwa Mulungu?” Ziba adayankha kuti, “Padakali mwana wamwamuna wa Yonatani. Iyeyo ngwopunduka miyendo.”
4
Mfumu idamufunsa kuti, “Ali kuti?” Ziba adayankha kuti, “Ali ku nyumba ya Makiri, mwana wa Amiyele, ku Lodebara.”
5
Pamenepo mfumu Davide adatuma anthu kuti akamtenge, ndipo iwo adakamtengadi ku nyumba ya Makiri mwana wa Amiyele, ku Lodebara.
6
Pamene Mefiboseti, mwana wa Yonatani, mwana wa Saulo, adafika kwa Davide, adaŵerama pamaso pake, napereka ulemu. Tsono Davide adati, “Mefiboseti!” Iyeyo adayankha kuti, “Ndabwera ine mtumiki wanu.”
7
Davide adamuuza kuti, “Usaope. Ndifuna kukuchitira chifundo chifukwa cha Yonatani bambo wako, ndipo ndidzakubwezera dera lonse la Saulo mbuyako. Udzadya nane pamodzi masiku onse.”
8
Iyeyo adamuŵeramira, nati, “Kodi ine mtumiki wanu ndine yani, kuti musamale galu wakufa ngati ine?”
9
Tsono mfumu idaitana Ziba mtumiki wa Saulo, nimuuza kuti, “Zinthu zonse zimene zidaali za Saulo ndi zonse za pa banja pake ndazipereka kwa mwana wa mbuyako Saulo.
10
Tsono iwe, ana ako ndi atumiki ako, muzidzamlimira iyeyo, ndi kumabwera ndi zinthu zokolola zakumunda, kuti banja la mbuyako likhale ndi chakudya. Koma Mefiboseti adzadya ndi ine masiku onse.” Ziba anali ndi ana aamuna 15 ndi atumiki 20.
11
Tsono adauza mfumu kuti, “Mtumiki wanune ndidzachita zonse potsata zimene inu mbuyanga mfumu mwalamula.” Choncho Mefiboseti ankadya ndi Davide ngati mmodzi mwa ana a mfumu.
12
Mefiboseti anali ndi mwana wamng'ono, dzina lake Mika. Ndipo anthu onse amene ankakhala m'nyumba ya Ziba, adasanduka atumiki a Mefiboseti.
13
Choncho Mefibosetiyo adakhala ku Yerusalemu, poti iyeyo ankadya ku nyumba ya mfumu masiku onse. Koma tsono anali wolumala mapazi onse aŵiri.
← Chapter 8
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 10 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24