bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
1 Samuel 1
1 Samuel 1
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 2 →
1
Padaali munthu wina dzina lake Elikana, wa ku Ramataimu-Zofimu ku dziko lamapiri la Efuremu. Anali mwana wa Yerohamu, mwana wa Elihu, mwana wa Tohu, mwana wa Zufu, wa fuko la Efuremu.
2
Elikanayo anali wamitala, mkazi wina dzina lake anali Hana, winayo anali Penina. Penina anali ndi ana, koma Hana analibe.
3
Chaka ndi chaka Elikana ankapita ku Silo kuchokera ku mzinda kwao, kukapembedza ndi kukapereka nsembe kwa Chauta Wamphamvuzonse. Ku Siloko kunali ana aŵiri a Eli, Hofeni ndi Finehasi, amene anali ansembe a Chauta.
4
Tsiku limene Elikana ankapereka nsembe, ankapatsako magawo a nsembeyo kwa mkazi wake Penina ndi kwa ana ake aamuna ndi aakazi.
5
Ndipo ngakhale ankakonda Hana, ankangompatsa gawo limodzi chifukwa choti Chauta sadampatse ana.
6
Tsono chifukwa choti Chauta sadampatse ana, mkazi mnzake uja ankangomnyodola ndi kumpeputsa, kuti amkwiyitse.
7
Zimenezi zinkachitika chaka ndi chaka. Nthaŵi zonse akamapita ku nyumba ya Chauta, mkazi mnzakeyo ankamputa. Nchifukwa chake Hana ankangolira, ndipo sankafuna ndi kudya komwe.
8
Mwina Elikana mwamuna wake ankamufunsa kuti, “Hana, kodi watani apa ukulira ndi kuwoneka wachisoni ndiponso sukufuna kudya? Kodi kwa iwe ineyo sindikuposa ana aamuna khumi?”
9
Tsiku lina iwo atatha kudya ku Silo kuja, Hana adaimirira nakapemphera. Nthaŵi imeneyo nkuti Eli, wansembe uja, ali pa mpando pambali pa khomo la Nyumba ya Chauta.
10
Hanayo ankavutika kwambiri mumtima mwake, ndipo adapemphera kwa Chauta, akulira ndi mtima woŵaŵa.
11
Adalumbira kuti, “Inu Chauta Wamphamvuzonse, muyang'ane kuzunzika kwanga ndipo muyankhe pemphero langa, osandiiŵala ine mdzakazi wanu. Ndithu mukandipatsa mwana wamwamuna, ine ndidzampereka mwanayo kwa Inu Chauta masiku onse a moyo wake, ndipo pamutu pake sipadzapita lumo.”
12
Iyeyo akupemphera chotero pamaso pa Chauta, Eli ankamuyang'ana pakamwa.
13
Hana ankalankhula chamumtima, milomo yake yokha ndiyo inkagwedezeka, koma mau ake sankamveka. Nchifukwa chake Eli adamuyesa woledzera.
14
Tsono adamufunsa kuti, “Mai, kodi mukhala chiledzerere mpaka liti? Pitani, akayambe watha vinyo mwamwayu.”
15
Koma Hana adayankha kuti, “Iyai mbuyanga, sindidamwe vinyo kapena chakumwa chaukali chilichonse. Munthune ndili ndi chisoni choopsa. Ndakhala ndikulira kwa Chauta chifukwa cha chisoni changachi.
16
Musayese kuti ine mdzakazi wanu ndine mkazi wachabechabe, pakuti nthaŵi yonseyi ndakhala ndikuulula kwa Chauta nkhaŵa yanga yaikulu ndi zovuta zanga.”
17
Apo Eli adamuyankha kuti, “Pitani ndi mtendere, Mulungu wa Israele akupatseni zimene mwampemphazo.”
18
Tsono Hana adati, “Mundikomerebe mtima mdzakazi wanune.” Pompo mkaziyo adachoka nakadya, ndipo sadaonekenso wachisoni.
19
M'maŵa mwake Elikana ndi banja lake adadzuka m'mamaŵa, ndipo atatha kupembedza Chauta, adabwerera kwao ku Rama. Elikana adakhala ndi mkazi wake Hana, ndipo Chauta adamkumbuka Hanayo.
20
Motero Hana adaima, ndipo adabala mwana wamwamuna namutcha dzina loti Samuele, kunena kuti, “Ndidachita kumpempha kwa Chauta.”
21
Tsono Elikana ndi banja lake lonse adapitanso kukatsira nsembe ya chaka ndi chaka kwa Chauta, ndi kukakwaniritsa lonjezo lake.
22
Koma Hana sadapite nao chifukwa adaauza mwamuna wake kuti, “Malinga mwanayu akaleka kuyamwa, ndidzapita naye kuti ndikampereke kwa Chauta, ndipo adzakhala komweko moyo wake wonse.”
23
Elikana mwamuna wake adamuuza kuti, “Uchite zimene zikukukomera, uyembekeze mpaka mwanayo ataleka kuyamwa. Kungoti Chauta achitedi monga momwe afunira.” Choncho mkaziyo adatsalira, namalera mwana wake uja mpaka atamletsa kuyamwa.
24
Atamuletsa kuyamwa, adapita naye ku nyumba ya Chauta ku Silo. Adatenga ng'ombe yamphongo ya zaka zitatu, ufa wa makilogramu khumi, ndi thumba lachikopa la vinyo. Ngakhale mwanayo anali wamng'ono ndithu, adapita nayebe.
25
Kumeneko adapha ng'ombe yamphongo ija ndipo mwanayo adampereka kwa Eli.
26
Tsono Hana adati, “Inu mbuyanga, ndikunenetsa kuti ndithudi ine ndine mkazi uja amene ndidaaimirira pano pamaso panu, ndikupemphera kwa Chauta.
27
Mwana uyu ndidachita kupempha, ndipo Chauta wandipatsa chopempha changacho.
28
Nchifukwa chake ndampereka kwa Chauta. Moyo wake wonse mwanayu adzakhala wake wa Chauta.” Ndipo onsewo adapembedza Chauta kumeneko.
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 2 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24
25
26
27
28
29
30
31