bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
1 Samuel 10
1 Samuel 10
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
← Chapter 9
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 11 →
1
Tsono Samuele adatenga nsupa ya mafuta nathira mafutawo pamutu pa Saulo. Ndipo adamumpsompsona nati, “Chauta akukudzoza kuti ukhale mfumu ya anthu ake Aisraele. Udzalamulira anthu a Chauta ndi kuŵapulumutsa kwa adani oŵazungulira. Chizindikiro chakuti Chauta wakudzoza kuti ukhale mfumu yolamulira anthu ake, ndi ichi:
2
ukachoka pano lero, ukumana ndi anthu aŵiri ku manda a Rakele ku Zeliza m'dziko la Benjamini. Iwowo akuuza kuti abulu unkafuna aja adapezeka, ndiponso kuti bambo wako waleka kusamala za abuluwo, koma akudera nkhaŵa za iwe, akunena kuti, ‘Nditani ine m'mene mwana wanga sakuwonekamu?’
3
Tsono utabzola pamenepo, ufika pa mtengo wogudira wa ku Tabori. Kumeneko ukumana ndi anthu atatu, wina atanyamula anaambuzi atatu, wina atanyamula mitanda itatu ya buledi, ndipo wina atanyamula thumba lachikopa la vinyo, akupita kukapereka nsembe kwa Mulungu ku Betele.
4
Atakupatsa moni, akuninkhako mitanda iŵiri ya buledi, iwe uilandire.
5
Pambuyo pake mufika ku phiri la Mulungu ku Gibea kumene kuli gulu lankhondo la Afilisti. Ndipo kumeneko, pamene mukuyandikira mzindawo, mukumana ndi gulu la aneneri akutsika kuchokera ku kachisi ku phiri, akuimba zeze, ting'oma, chitoliro ndi pangwe, ndipo akulosa.
6
Pamenepo mzimu wa Chauta ukuloŵa mwamphamvu, ndipo nawenso uyamba kulosa nao, usinthika ndi kukhala munthu wina.
7
Tsono ukaona zizindikiro zimenezi, uchite chilichonse choyenera nthaŵi imeneyo, poti Mulungu ali nawe.
8
Udzatsogola ndiwe kupita ku Giligala. Patapita masiku asanu ndi aŵiri, ndidzabwera kudzapereka nsembe zopsereza ndi zamtendere. Kumeneko ndidzakulangiza zoti uchite.”
9
Pamene Saulo adatembenuka kuti asiyane ndi Samuele, mtima wake Mulungu adausandutsa winawina. Ndipo zizindikiro zonse zija zidachitikadi tsiku limenelo.
10
Atafika ku Gibea, adakumana ndi gulu la aneneri. Tsono mzimu wa Mulungu udamloŵa Sauloyo mwamphamvu, nayamba kulosa nao.
11
Onse amene ankamdziŵa kale, ataona kuti akulosa limodzi ndi aneneri, adayamba kufunsana kuti, “Chamchitikira nchiyani mwana wa Kisi? Kani Saulonso ali m'gulu la aneneri?”
12
Munthu wina wakomweko adayankhako nati, “Nanga enaŵa ndiye abambo ao ndani?” Nchifukwa chake padayambika chisudzo chakuti, “Kani Saulonso ali m'gulu la aneneri?”
13
Atatha kulosako, Saulo adapita ku kachisi ku phiri.
14
Mbale wa bambo wake wa Saulo ataona Sauloyo ndi mnyamata uja, adaŵafunsa kuti, “Mudaapita kuti?” Saulo adayankha kuti, “Tidaakafunafuna abulu. Titaona kuti sakupezeka, tidaapita kwa Samuele.”
15
Apo mbale wa bambo wakeyo adati, “Ndikukupempha, uzeko zimene adanena Samuele.”
16
Saulo adati, “Samuele adatiwuza bwino lomwe kuti abuluwo adapezeka.” Koma sadanene kanthu za nkhani ya ufumu ija imene Samuele adaamuuza.
17
Tsono Samuele adaitana anthu ku msonkhano wachipembedzo ku Mizipa.
18
Adauza Aisraele onse kuti, “Chauta, Mulungu wa Aisraele, akuti, ‘Ndidakutulutsani inu Aisraele ku dziko la Ejipito, ndipo ndidakupulumutsani kwa Aejipito ndi kwa mafumu onse amene ankakusautsani.’
19
Koma lero lino, inu mwamkana Mulungu wanu amene amakupulumutsani m'mavuto anu onse ndi m'masautso anu. Mukuti, ‘Iyai! Koma mutipatse mfumu yotilamulira.’ Nchifukwa chake tsono musonkhane pamaso pa Chauta potsata mafuko anu ndi mabanja anu.”
20
Choncho Samuele adasonkhanitsa mafuko onse a Aisraele, ndipo pochita maere, fuko la Benjamini ndilo lidasankhidwa.
21
Adasonkhanitsa fuko la Benjamini banja ndi banja, ndipo pochita maere, banja la Matiri ndilo lidasankhidwa. Potsiriza pake adasonkhanitsa anthu a m'banja la Matiri mmodzimmodzi, ndipo pochita maere, Saulo mwana wa Kisi, ndiye adasankhidwa. Koma pamene adamfunafuna, sadampeze.
22
Tsono anthuwo adafunsa Chauta kuti, “Mwati munthuyo wafika kuno?” Chauta adayankha kuti, “Inde, akubisala pakati pa katundu.”
23
Choncho adathamanga kukamtenga kumeneko. Ndipo ataimirira pakati pa anthu, ankaoneka wamtali, mwakuti anthu ena onse ankamugwa m'mapewa.
24
Tsono Samuele adafunsa anthu onsewo kuti, “Kodi mukumuwona munthu amene Chauta wamsankha? Palibe wina wonga ameneyu pakati pa anthu onse.” Ndipo anthu onse adafuula kuti, “Amfumu akhale ndi moyo wautali!”
25
Tsono Samuele adafotokozera anthu zinthu zoyenera mfumu pa maudindo ake. Ndipo adazilemba m'buku nakaliika bukulo pa malo oyera pamaso pa Chauta. Pambuyo pake Samuele adauza anthu kuti abwerere kwao.
26
Saulo nayenso adapita kwao ku Gibea, ndipo adatsakana naye anthu amphamvu amene Mulungu adaŵafeŵetsa mtima.
27
Koma anthu ena achabechabe adati, “Kodi munthu ameneyu angathe bwanji kutipulumutsa ife?” Ndipo adayamba kumnyoza Sauloyo, osampatsa ndi mphatso zomwe. Koma iye adangokhala chete.
← Chapter 9
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 11 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24
25
26
27
28
29
30
31