bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
1 Samuel 7
1 Samuel 7
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
← Chapter 6
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 8 →
1
Anthu a ku Kiriyati-Yearimu adadzatenga Bokosi lachipanganolo nakafika nalo ku nyumba ya Abinadabu pa phiri. Ndipo adasankha mwana wake, Eleazara, kuti akhale woyang'anira Bokosilo.
2
Kuyambira tsiku limene Bokosi lachipangano lija lidakhala ku Kiriyati-Yearimu, padapita nthaŵi yaitali ya zaka makumi aŵiri. Ndipo Aisraele onse adadandaulira Chauta kuti aŵathandize.
3
Pamenepo Samuele adauza mtundu wonse wa Aisraele kuti, “Ngati mukubwerera kwa Chauta ndi mtima wanu wonse, muchotse milungu yachilendo ndi Aasitaroti pakati panu, mtima wanu ukhale pa Chauta ndi kutumikira Iye yekha. Mukatero adzakupulumutsani kwa Afilisti.”
4
Choncho Aisraele adachotsa Abaala ndi Aasitaroti, nayamba kutumikira Chauta yekha.
5
Tsono Samuele adati, “Sonkhanitsani mtundu wonse wa Aisraele ku Mizipa, ndipo ine ndikupemphererani kwa Chauta.”
6
Choncho adasonkhana ku Mizipa, natunga madzi ndi kuŵathira pansi pamaso pa Chauta mopepesera, ndipo adasala chakudya tsiku limenelo, namanena kuti, “Tidachimwira Chauta.” Nku Mizipako kumene Samuele ankaweruza milandu ya Aisraele.
7
Afilisti atamva kuti Aisraele adasonkhana ku Mizipa, akalonga a Afilisti adapita kuti akachite nawo nkhondo. Aisraele atamva zimenezi, adachita nawo mantha Afilistiwo,
8
ndipo adauza Samuele kuti, “Musaleke kutidandaulira kwa Chauta, Mulungu wathu, kuti atipulumutse kwa Afilistiŵa.”
9
Choncho Samuele adatenga mwanawankhosa woyamwa, nampereka wathunthu ngati nsembe yopsereza kwa Chauta. Adapempherera Aisraele kwa Chauta, ndipo Chauta adamuyankha.
10
Pamene Samuele ankapereka nsembe yopsereza ija, Afilisti adasendera pafupi kuti amenyane ndi Aisraele. Koma Chauta adaŵaopsa Afilistiwo ndi mau onga bingu, naŵasokoneza, mwakuti adamwazikana pamaso pa Aisraele.
11
Tsono Aisraele adatuluka ku Mizipa naŵalondola Afilistiwo, mpaka kubzola Betekara, akuŵapha njira yonse.
12
Pambuyo pake Samuele adatenga mwala, nauimiritsa pakati pa Mizipa ndi Sene, ndipo adautcha dzina loti Ebenezeri, ndiye kuti “Mwala wachithandizo,” pakuti adati, “Mpaka pano Chauta wakhala akutithandiza.”
13
Choncho Afilisti adagonjetsedwa, ndipo sadaloŵenso m'dziko la Aisraele. Chauta ndiye ankalimbana ndi Afilisti nthaŵi yonse Samuele ali moyo.
14
Mizinda imene Afilisti anali atalanda idabwezedwanso kwa Aisraele, kuchokera ku Ekeroni mpaka ku Gati. Motero Aisraele adapulumutsa dziko lao kwa Afilisti. Panalinso mtendere pakati pa Aisraele ndi Aamori.
15
Samuele adatsogolera Aisraele moyo wake wonse.
16
Chaka ndi chaka ankapanga ulendo wozungulira, kupita ku Betele, Giligala ndi ku Mizipa, ndipo ankaweruza milandu ku malo onseŵa.
17
Pambuyo pake ankabwerera ku Rama, poti ndiko kunali kwao. Kumenekonso ankaweruza Aisraele, ndipo adamangirako Chauta guwa.
← Chapter 6
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 8 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24
25
26
27
28
29
30
31