bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
1 Samuel 11
1 Samuel 11
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
← Chapter 10
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 12 →
1
Patapita ngati mwezi umodzi, Nahasi Mwamoni adanka ndi gulu lankhondo kukazinga mzinda wa Yabesi m'dziko la Giliyadi. Tsono anthu onse a mu mzinda wa Yabesi adapempha Nahasiyo kuti, “Muchite nafe chipangano, ndipo tidzakutumikirani.”
2
Koma Nahasi adaŵauza kuti, “Ndidzachita nanu chipangano pokhapokha aliyense nditamkolowola diso la ku dzanja lamanja, kuti pakutero ndichititse manyazi Aisraele onse.”
3
Akuluakulu a ku Yabesi adamuyankha kuti, “Mutiyembekeze masiku asanu ndi aŵiri, kuti titumize mithenga ku dziko lonse la Aisraele. Tsono ngati sipaoneka wina wotipulumutsa, pamenepo tidzadzipereka kwa inu.”
4
Pamene amithenga adafika kwao kwa Saulo ku Gibea, nauza anthu nkhaniyo, onse adayamba kulira motaya mtima.
5
Nthaŵi imeneyo nkuti Saulo akuchokera ku munda, akuyenda pambuyo pa ng'ombe zantchito. Tsono adafunsa kuti, “Chaŵavuta anthu nchiyani kuti azilira?” Pamenepo adamuuza nkhani ya anthu a ku Yabesi ija.
6
Saulo atamva zimenezi, pomwepo mzimu wa Mulungu udamloŵa mwamphamvu, ndipo adapsa mtima kwabasi.
7
Mwa ng'ombe zija adapatulapo ziŵiri nazipha, ndipo adazidula nthulinthuli. Kenaka adatuma amithenga aja kuti akapereke nthulizo ku dziko lonse la Israele, ndi kumakanena kuti, “Umu ndimo m'mene adzaichitira ng'ombe ya aliyense amene sadzatsata Saulo ndi Samuele.” Apo anthuwo adagwidwa ndi mantha oopa Chauta ndipo onse adanyamuka ndi mtima umodzi.
8
Saulo adaŵasonkhanitsa ku Bezeki, naŵaŵerenga. Aisraele analipo 300,000, Ayuda analipo 30,000.
9
Ndipo adauza amithenga a ku Yabesi aja kuti, “Mukaŵauze anthu akwanu kuti maŵa, dzuŵa likuwomba mtengo, adzapulumutsidwa.” Anthu a ku Yabesi atamva uthengawu, adasangalala zedi.
10
Nchifukwa chake adauza Nahasi kuti, “Maŵa tidzadzipereka kwa inu, ndipo mutichite chilichonse chimene chikukomereni.”
11
M'maŵa mwake, Saulo adagaŵa anthu ake m'magulu atatu. Ndipo adaloŵa pakati pa zithando zankhondo za Aamoni m'mamaŵa kusanache, napha Aamoniwo mpaka masana dzuŵa litatentha. Tsono amene adapulumuka adangoti balala, aliyense kwayekhakwayekha.
12
Apo anthu adamufunsa Samuele kuti, “Ndani amene ankanena kuti, ‘Kodi Saulo nkutilamulira ife?’ Bwera nawoni anthuwo kuti tiŵaphe.”
13
Koma Saulo adati, “Palibe munthu ndi mmodzi yemwe amene aphedwe lero lino, pakuti lero Chauta wagwira ntchito yopulumutsa Aisraele.”
14
Tsono Samuele adauza anthuwo kuti, “Tiyeni tipite ku Giligala, tikatsimikizenso ufumu wa Saulo kumeneko.”
15
Choncho Aisraele onse adapita ku Giligala ndipo kumeneko adalonga Sauloyo ufumu pamaso pa Chauta. Anthu adapereka nsembe zachiyanjano pamaso pa Chauta, ndipo Saulo pamodzi ndi Aisraele onse adasangalala zedi kumeneko.
← Chapter 10
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 12 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24
25
26
27
28
29
30
31