bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
1 Samuel 26
1 Samuel 26
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
← Chapter 25
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 27 →
1
Tsiku lina anthu a ku Zifi adabwera kwa Saulo ku Gibea, namuuza kuti, “Davide akubisala ku phiri la Hakila limene lili kuvuma kwa Yesimoni.”
2
Saulo adanyamuka napita ku chipululu cha Zifi atatenga ankhondo 3,000 osankhidwa, kuti akafunefune Davide kuchipululuko.
3
Adamanga zithando zankhondo pa phiri la Hakila, limene lili pambali pa mseu, chakuvuma kwa Yesimoni. Koma Davide adakhalabe kuchipululuko. Tsono ataona kuti Saulo akumlondola,
4
Davide adatuma anthu oti akazonde, ndipo adapezadi kuti Saulo wafika.
5
Ndiye Davide adanyamuka nakafika pa malo amene Saulo adaamangapo zithando zake. Ndipo adaona malo amene ankagonapo Sauloyo ndi Abinere mwana wa Nere, mkulu wa ankhondo a Saulo. Sauloyo ankagona m'zithandomo, ndipo gulu lonse lankhondo lidaamanga zithando pomzungulira.
6
Tsono Davide adafunsa Ahimeleki Muhiti ndi Abisai mkulu wa Yowabu, mwana wa Zeruya, kuti, “Kodi ndani apite nane ku zithando za Saulo?” Abisai adati, “Ine ndipita nanu.”
7
Choncho Davide ndi Abisai adakaloŵa ku zithando zankhondo usiku. Saulo anali gone m'chithando chake, atazika mkondo wake pansi cha kumutu kwake. Abinere ndi ankhondo onse adaagona momzungulira.
8
Abisai adauza Davide kuti, “Mulungu wapereka mdani wanu kwa inu lero. Bwanji tsono mundilole kuti ndimbaye ndi mkondo kamodzinkamodzi ndi kumkhomerera pansi, sindichita kumbaya kaŵiri.”
9
Koma Davide adamuuza kuti, “Ai, usamuphe. Ndani angathe kupweteka wodzozedwa wa Chauta nakhala wosachimwa?”
10
Ndipo adalamulira kuti, “Pali Chauta wamoyo, Chautayo ndiye adzamkanthe kapena pamene lidzafike tsiku lake lakumwalira, kapena pamene adzapite ku nkhondo nakaphedwa.
11
Chauta andiletse kuti ndisapweteke wodzodzedwa wake. Koma tsono tingotenga mkondo umene uli kumutu kwakewu ndi mtsuko wa madziwu, ndipo tizipita.”
12
Motero Davide adatenga mkondo ndi mtsuko wa madzi, zimene zinali kumutu kwa Saulo, nachokapo. Palibe amene adaona zimenezo ngakhale kuzidziŵa, ndipo panalibe wina aliyense amene adadzuka. Onse anali m'tulo, chifukwa chakuti Chauta adaaŵagonetsa tulo tofa nato.
13
Pambuyo pake Davide adakwerera mbali ina nakaimirira pamwamba pa phiri, pakati nkusiya mpata waukulu.
14
Tsono Davide adaitana gulu lankhondo ndi Abinere mwana wa Nere, naŵafunsa kuti, “Kodi sukumva iwe Abinere?” Abinere adayankha kuti, “Kodi ndiwe yani ukuitana mfumuwe?”
15
Davide adafunsa Abinere kuti, “Kodi sindiwe mwamuna? Ndani ali wofanafana nawe m'dziko la Israele? Nanga chifukwa chiyani sudamlonde mbuyako mfumu? Tsopano apa munthu wina anabwera kumeneko kuti adzaphe mbuyakoyo.
16
Zimene wachitazi si zabwino ai. Pali Chauta wamoyo, nonsenu muyenera kuphedwa chifukwa simudalonde mbuye wanu, wodzozedwa wa Chauta. Uyang'ane kumene kuli mkondo wa mfumu ndi mtsuko wa madzi, zimene zinali kumutu kwake.”
17
Saulo adazindikira liwu la Davide, ndipo adafunsa kuti, “Kodi liwu limeneli ndi lako, iwe mwana wanga Davide?” Davide adayankha kuti, “Inde, ndi liwu langadi, mbuyanga mfumu.
18
Chifukwa chiyani mbuyanga mukundilondola ine mtumiki wanu? Kodi ndachita chiyani? Kodi tchimo langa nlotani?
19
Nchifukwa chake tsono, mbuyanga mfumu, mumve mau a ine mtumiki wanu. Ngati ndi Chauta amene wautsa mtima wanu kuti mundiwukire, Chautayo apepesedwe ndi nsembe. Koma ngati ndi anthu, iwowo Chauta aŵatemberere, pakuti tsono andipirikitsa, kuti ndisakhale nao m'dziko la Chauta. Akuti, ‘Pita katumikire milungu ina.’
20
Ndiye inu tsono musalole kuti ndifere kutali ndi Chauta, pakuti mfumu ya Aisraele yatuluka kudzandifunafuna ine nthata, monga momwe amachitira munthu wosaka nkhwali ku thengo.”
21
Tsono Saulo adati, “Ndachimwa. Bwerera, mwana wanga Davide, sindidzakuchitanso choipa, popeza kuti moyo wanga wauwona ngati wa mtengo wapatali. Ndithu ndachita zauchitsiru ndipo ndachimwa kwambiri.”
22
Apo Davide adayankha kuti, “Suwu mkondo wanu, mfumu. Tumani mmodzi mwa ankhondowo adzatenge.
23
Chauta amadalitsa munthu wokhulupirika ndi wochita zabwino. Chauta anakuperekani m'manja mwanga lero, koma sindidaphe munthu wodzozedwa ufumu.
24
Monga ndakusungirani moyo wanu leromu, momwemonso Chauta ateteze moyo wanga, ndipo andipulumutse m'mavuto anga onse.”
25
Apo Saulo adauza Davide kuti, “Mulungu akudalitse mwana wanga Davide. Udzachita zazikulu, ndipo pa zonsezo udzapambana.” Choncho Davide adachokapo, ndipo Saulo adabwerera kwao.
← Chapter 25
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 27 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24
25
26
27
28
29
30
31