bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
1 Samuel 6
1 Samuel 6
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
← Chapter 5
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 7 →
1
Bokosi lachipangano la Chauta lidakhala m'dziko la Afilisti miyezi isanu ndi iŵiri.
2
Tsono Afilisti adaitana ansembe ao ndi anthu amaula naŵafunsa kuti, “Tichite nalo chiyani Bokosi lachipanganoli? Tiwuzeni. Kodi Bokosi limeneli tingalibwezere ku malo ake mwa njira yanji?”
3
Iwo adati, “Mukafuna kubwezera Bokosili, musalitumize lopanda kanthu, koma mwa njira iliyonse mulitumize pamodzi ndi mphatso, kuti ikhale nsembe yopepesera machimo. Pambuyo pake mudzachira, ndipo pamenepo mudzadziŵa chifukwa chiyani chilango cha Mulungu sichikukuchokani.”
4
Apo anthuwo adafunsa kuti, “Kodi nsembe yopepesera machimoyo idzakhale ya mtundu wanji?” Iwo adayankha kuti, “Idzakhale zifanizo zagolide za mafundo asanu ndi za mbeŵa zisanu kuŵerengetsa akalonga asanu a Afilisti, pakuti mliri womwewo unali pa inu nonse ndi pa akalonga anu.
5
Tsono mupange zifanizo za mafundo anu aja ndi za mbeŵa zimene zikuwononga m'dziko mwanu, ndipo mulemekeze Mulungu wa Aisraele. Mwina mwake sadzakuvutaninso, inu ndi milungu yanu ndi dziko lanu.
6
Chifukwa chiyani mukufuna kukhala okanika ngati Aejipito aja ndi Farao? Kodi Aejipitowo, Mulungu ataŵazunza, suja adaŵalola Aisraele kuti apite, ndipo adapitadi?
7
Ndiye inu, konzani galeta latsopano ndipo mutenge ng'ombe ziŵiri zazikazi zamkaka zimene sizidavalepo goli ndi kale lonse. Mumange ng'ombezo ku galeta, koma makonyani ake muŵasiye kumudzi kwanu.
8
Tsono mutenge Bokosi lachipanganolo, muliike pa galeta, ndipo pambali pake muikepo bokosi la zinthu zagolide zija zimene mukutumiza kwa Chauta, kuti zikhale nsembe yopepesera machimo. Pambuyo pake muzitaye ng'ombezo ndipo galeta lizipita.
9
Tsono muziliyang'ana. Likamangopita kulondola kwao kwa Bokosilo mpaka kukafika ku Betesemesi, ndiye kutidi ndi Mulungu wa Aisraele amene adatidzetsera zovuta zazikuluzi. Koma zikapanda kutero, tidzadziŵa kuti sindiye amene adatizunza, zidangochitika mwatsoka.”
10
Anthu aja adachitadi momwemo. Adatenga ng'ombe ziŵiri zamkaka nazimanga ku galeta, natsekera makonyani ake m'khola.
11
Ndipo adaika Bokosi lachipangano pa galeta, ndi bokosi lija m'mene munali mbeŵa zagolide ndi zifanizo za mafundo ao.
12
Tsono ng'ombezo zidapita molunjika potsata mseu waukulu wokafika ku Betesemesi, zikunka zikulira. Sizidacheukire kumanzere kapena kumanja, ndipo akalonga a Afilisti ankazitsata pambuyo, mpaka kukafika ku malire a ku Betesemesi.
13
Nthaŵiyo anthu a ku Betesemesi ankadula tirigu m'chigwa. Ndipo pamene adati tha, napenya Bokosi lachipanganolo likubwera, adakondwa.
14
Galeta lija lidafikira ku munda wa Yoswa ku Betesemesi ndi kuima komweko. Kumeneko kunali mwala waukulu. Tsono anthu am'mudzimo adaliŵaza nkhuni galetalo ndipo adapha ng'ombezo nazipereka kwa Chauta ngati nsembe yopsereza.
15
Alevi anali atatsitsa Bokosi lachipangano la Chauta ndi bokosi lina lija la pambali pake m'mene munali zinthu zagolide, naŵaika pa mwala waukuluwo. Ndipo anthu a ku Betesemesi adapereka nsembe zopsereza ndi nsembe zina kwa Chauta pa tsiku limenelo.
16
Akalonga asanu a Afilisti aja ataona zimenezo, adabwerera ku Ekeroni tsiku lomwelo.
17
Zifanizo zagolide za mafundo zija zimene Afilisti adapereka ngati nsembe zopepesera Chauta, zinkakhalira mizinda isanu: chimodzi chinali cha ku Asidodi, china cha ku Gaza, china cha ku Asikeloni, china cha ku Gati, china cha ku Ekeroni.
18
Nazonso zifanizo zagolide za mbeŵa adazipereka moŵerengetsa mizinda yonse ya Afilisti imene inali ya akalonga asanu aja. Ina inali mizinda yamalinga, ina inali midzi yapamtetete. Mwala waukulu uja umene adaikapo Bokosi lachipangano lija m'munda wa Yoswa ku Betesemesi, udakalipo mpaka pano ngati mboni.
19
Pambuyo pake Chauta adaphapo anthu 70 a ku Betesemesi chifukwa choti adaasuzumira m'Bokosi lachipangano, ndipo anzao adalira, popeza kuti Chauta adaapha anthu ambiri pakati pao.
20
Tsono anthu a ku Betesemesi adati, “Angathe ndani kuima pamaso pa Chauta, Mulungu woyerayu? Ndipo Bokosi lachipanganoli lidzapita kuti likachoka kuno?”
21
Choncho adatuma amithenga kwa nzika za ku Kiriyati-Yearimu kukanena kuti, “Afilisti abweza Bokosi lachipangano la Chauta. Bwerani kuno, mudzalitenge, kupita nalo kwanuko.”
← Chapter 5
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 7 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24
25
26
27
28
29
30
31