bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
1 Samuel 27
1 Samuel 27
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
← Chapter 26
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 28 →
1
Davide adaganiza mumtima mwake kuti, “Tsiku lina Saulo adzandipha. Palibe china chimene ndingachitepo, koma kuthaŵira ku dziko la Afilisti. Choncho Saulo adzaleka kumandifunafuna m'dziko la Aisraele, ndipo ndidzapulumuka kwa iye.”
2
Tsono Davide adanyamuka, ndipo pamodzi ndi ankhondo 600 amene anali naye, adapita kwa Akisi, mwana wa Maoki, mfumu ya ku Gati.
3
Adakhala ndi Akisi ku Gati, iyeyo pamodzi ndi anthu ake, aliyense ndi banja lake. Davide anali ndi akazi ake aŵiri, Ahinowamu wa ku Yezireele ndi Abigaile wa ku Karimele, mkazi wamasiye wa Nabala.
4
Saulo atamva kuti Davide wathaŵira ku Gati, sadamfunefunenso.
5
Pambuyo pake Davide adauza Akisi kuti, “Ngati ndapeza kuyanja pamaso panu, mundipatse malo pa mudzi wina m'dziko mwanu kuti ndizikhala kumeneko. Kodi ine mtumiki wanu ndizikhaliranji pamodzi ndi inu mu mzinda wanu waufumu?”
6
Choncho tsiku limenelo Akisi adapatsa Davide mudzi wa Zikilagi. Nchifukwa chake mudzi wa Zikilagi ngwa mafumu a Yuda mpaka lero lino.
7
Motero Davide adakhala ku dziko la Afilisti chaka chimodzi ndi miyezi inai.
8
Tsono Davide ndi anthu amene anali naye ankapita kwa Agesuri, Agerizi, ndi Aamaleke nakaŵathira nkhondo onsewo. Mitundu imeneyi inali nzika za dzikolo kuyambira kale. Dziko lao linkafika ku Suri ndipo linkachita malire ndi dziko la Ejipito.
9
Pa maulendo ake ankhondowo Davide ankapha anthu a m'dzikolo, osasiyapo wamoyo mwamuna kapena mkazi. Koma ankatenga nkhosa, ng'ombe, abulu, ngamila, ndi zovala, ndipo zonsezo ankabwerera nazo kwa Akisi.
10
Akisi akafunsa kuti, “Kodi munakamenya nkhondo ndi yani lero?” Davide ankati, “Tinakamenya nkhondo kumwera kwa Yuda,” mwina ankati, “Ku dziko la Ayeramiyele,” mwina ankati, “Ku dziko la Akeni.”
11
Davide sankasiya wamoyo, mwamuna kapena mkazi, kuwopa kuti wopulumukayo angakanene ku Gati kuti, “Davide adatichita zakutizakuti.” Davide ankachita choncho nthaŵi zonse pamene ankakhala ku dziko la Afilisti.
12
Ndipo Akisi adamkhulupirira Davide namaganiza kuti, “Davide wadzisandutsa munthu woipa wodedwa ndi anthu ake omwe Aisraele. Nchifukwa chake adzakhala mtumiki wanga pa moyo wake wonse.”
← Chapter 26
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 28 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24
25
26
27
28
29
30
31