bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
1 Samuel 15
1 Samuel 15
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
← Chapter 14
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 16 →
1
Tsiku lina Samuele adauza Saulo kuti, “Paja Chauta adaatuma ine kuti ndikudzozeni, kuti mukhale mfumu ya anthu ake Aisraele. Nchifukwa chake tsono imvani uthenga wochokera kwa Chauta.
2
Chauta Wamphamvuzonse akunena kuti, ‘Ndidzalanga Aamaleke chifukwa cha kumenyana ndi Aisraele pa njira, pamene Aisraelewo ankachokera ku Ejipito.
3
Pitani tsono, mukaŵathire nkhondo Aamalekewo, mukaononge kwathunthu zinthu zao zonse. Musakasiyeko munthu ndi mmodzi yemwe, mukaphe amuna, akazi, ana ndi makanda omwe. Mukaphenso ng'ombe, nkhosa, ngamira ndi abulu onse.’ ”
4
Choncho Saulo adaitana ankhondo ake, naŵaŵerenga ku Telaimu. Ankhondo oyenda pansi analipo 200,000, ankhondo a ku Yuda analipo 10,000 pamodzi.
5
Ndipo Saulo adafika ku mzinda wa Aamaleke, naubisalira m'khwaŵa.
6
Tsono adauza Akeni kuti, “Muchoke pakati pa Aamaleke, kuti ndingakuwonongereni kumodzi. Pakuti inu mudachitira chifundo Aisraele muja ankachokera ku Ejipitomu.” Motero Akeni adachoka pakati pa Aamaleke.
7
Pamenepo Saulo adagonjetsa Aamaleke kuyambira ku Havila mpaka ku Suri, kuvuma kwa Ejipito.
8
Adamtenga wamoyo Agagi, mfumu ya Aamaleke, ndipo adapha anthu ena onse ndi lupanga.
9
Koma Saulo ndi anthu amene anali nawo, sadamuphe Agagi, sadaphenso nkhosa ndi ng'ombe zabwino koposa, anaang'ombe ndi anaankhosa onenepa, ndi zonse zimene zinkaoneka zabwino. Adangoononga zimene zinali zopanda ntchito ndi zachabechabe.
10
Tsono Chauta adauza Samuele kuti,
11
“Ndikumva chisoni kuti ndidampatsa ufumu Saulo. Wabwerera m'mbuyo, waleka kunditsata, ndipo sadamvere malamulo anga.” Pamenepo Samuele adapsa mtima, ndipo adadandaula kwa Chauta usiku wonse.
12
M'mamaŵa ndithu, Samuele adadzuka kuti akakumane ndi Saulo. Anthu adamuuza kuti, “Saulo adabwera ku Karimele, ndipo kumeneko adadziimikira mwala wa chikumbutso cha iye mwini. Tsono adachokapo napitirira mpaka ku Giligala.”
13
Samuele atafika kwa Saulo, Sauloyo adamuuza kuti, “Chauta akudalitseni. Ndachitadi zonse zimene Chauta adandilamula.”
14
Koma Samuele adati, “Nanga bwanji ndikumva nkhosa ndi ng'ombe zikulira?”
15
Saulo adayankha kuti, “Zimenezi adakazitenga kwa Aamaleke, pakuti anthu adasungako nkhosa ndi ng'ombe zabwino koposa, kuti akapereke nsembe kwa Chauta, Mulungu wanu. Koma zina zonse taziwononga kotheratu.”
16
Apo Samuele adamuuza kuti, “Basi, musapitirize! Imani ndikukambireni zimene Chauta wandiwuza usiku.” Tsono Saulo adati, “Nenani.”
17
Samuele adati, “Ngakhale kale munali wamng'ono pamaso pa anthu, tsopano mwasanduka mtsogoleri wa mafuko onse a Aisraele. Chauta adakudzozani kuti mukhale mfumu yomalamulira Aisraele.
18
Ndipo Chauta adakutumani kuti, ‘Pita, ukaononge kwathunthu Aamaleke, anthu oipa mtima aja, ndipo uchite nawo nkhondo mpaka kuŵatheratu onsewo.’
19
Chifukwa chiyani nanga simudamvere mau a Chauta? Chifukwa chiyani mudathamangira zofunkha ndi kuchita zoipira Chauta?”
20
Saulo adayankha kuti, “Iyai, inetu mau a Chauta ndidatsata, ndipo ndidapitadi kukachita zimene Chauta adandituma. Ndidagwira Agagi mfumu ya Aamaleke, ndipo ndidapha Aamaleke onse.
21
Koma pa zofunkha anthu adatengako nkhosa ndi ng'ombe, ndi zina zabwino kwambiri, zimene zinkayenera kuwonongedwa, kuti akazipereke nsembe kwa Chauta, Mulungu wanu, ku Giligala.”
22
Koma Samuele adati, “Kodi Chauta amakondwa ndi chiti: nsembe zopsereza ndi nsembe zina, kapena kumvera mau ake? Ndithu, ndi kumvera ndi kupereka nsembe kwabwino kwambiri nkumvera. Ndi kutchera khutu ndi kupereka mafuta ankhosa kwabwino kwambiri nkutchera khutu.
23
Kugalukira kuli ngati tchimo loombeza, kukhala wokanika kuli ngati tchimo lopembedza mafano. Popeza kuti mwakana mau a Chauta, Iyenso wakukanani kuti musakhalenso mfumu.”
24
Pamenepo Saulo adauza Samuele kuti, “Ndachimwa, ndalakwira lamulo la Chauta ndiponso malangizo anu, chifukwa chakuti ndinkaopa anthu ndipo ndinkamvera mau ao.
25
Nchifukwa chake tsono pepani, ndagwira mwendo, mundikhululukire tchimo langa, ndipo mubwerere nane pamodzi, kuti ndikampembedze Chauta.”
26
Koma Samuele adayankha kuti, “Sindibwerera nanu, popeza kuti mwakana mau a Chauta, Iyenso wakukanani kuti musakhalenso mfumu yolamulira Aisraele.”
27
Pamene Samuele ankatembenuka kuti azipita, Saulo adagwira mpendero wa mkanjo wake, ndipo mkanjowo udang'ambika.
28
Apo Samuele adamuuza kuti, “Chauta wachita ngati kung'amba ufumu wa Israele kuchoka kwa inu lero, ndipo waupereka kwa mnzanu wabwino koposa inuyo.
29
Mulungu Waulemerero wa Aisraele sanama kapena kusintha maganizo. Pakuti Iye si munthu, kuti athe kusintha maganizo.”
30
Tsono Saulo adati, “Inde ndachimwa, komabe chonde mundilemekeze pakati pa atsogoleri a anthu anga ndi pamaso pa Aisraele onse, ndipo mubwerere nane pamodzi, kuti ndikapembedze Chauta, Mulungu wanu.”
31
Choncho Samuele adabwereradi, natsagana ndi Saulo. Ndipo Sauloyo adapembedza Chauta.
32
Pambuyo pake Samuele adauza Saulo kuti, “Bwera nayeni kuno Agagi uja, mfumu ya Aamaleke.” Ndipo Agagiyo adafika kwa Samuele mokondwa, chifukwa adati, “Ndithudi, zoŵaŵa za imfa zapita!”
33
Koma Samuele adati, “Monga momwe lupanga lako lasandutsira akazi kuti akhale opanda ana, momwemonso mai wako adzakhala wopanda mwana pakati pa akazi ena.” Ndipo Samuele adapha Agagiyo namduladula patsogolo pa guwa la Chauta ku Giligala.
34
Tsono Samuele adapita ku Rama, koma Saulo adapita ku nyumba yake ku Gibea wa Saulo.
35
Samuele sadamuwonenso Saulo moyo wake wonse, koma ankamulira ndithu, popeza kuti Chauta adaamuchotsa Sauloyo kukhala mfumu yolamulira Aisraele.
← Chapter 14
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 16 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24
25
26
27
28
29
30
31