bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
1 Samuel 19
1 Samuel 19
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
← Chapter 18
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 20 →
1
Saulo adalamula mwana wake Yonatani ndi akuluakulu onse kuti aphe Davide. Koma Yonatani ankakonda Davide kwambiri.
2
Choncho adakauza Davide kuti, “Iwe, abambo anga akufuna kukupha. Ndiye uchenjere, m'maŵa ukakhale kwina kobisalika.
3
Ine ndidzapita ndi kukaima pakhundu pa bambo wanga kuminda kumene iwe ukabisaleko, tsono ndidzalankhula ndi bambo wanga za iwe. Chilichonse chimene ndidzamve, ndidzakuuza.”
4
Tsono Yonatani adaterodi ndipo adakanena zabwino za Davide kwa bambo wake, namuuza kuti, “Atate, musachimwire mtumiki wanu Davide, poti sadakuchimwireni, koma amakuchitirani zabwino.
5
Paja adaaika moyo wake pa minga pakupha Goliyati Mfilisti uja. Pambuyo pake Chauta adachita zazikulu pakupambanitsa Aisraele pa nkhondo. Inu mudaona zimenezo ndi kukondwera nazo. Chifukwa chiyani tsono mukufuna kuchimwira munthu wosalakwa, pofuna kumupha Davideyu?”
6
Saulo adamvera mau a Yonatani, ndipo adalumbira kuti, “Mulungudi! Davideyo sadzaphedwa!”
7
Tsono Yonatani adaitana Davide namuuza zonsezo. Choncho Yonatani adabwera naye kwa Saulo, ndipo Davideyo ankatumikira Saulo monga kale.
8
Nkhondo ina idabukanso. Davide adapita kukamenyana ndi Afilisti. Adapha Afilisti ambiri, kotero kuti iwowo adathaŵa.
9
Tsiku lina mzimu woipa uja udatsikira Saulo pa nthaŵi yomwe anali m'nyumba mwake, mkondo uli m'manja, Davide akuimba zeze.
10
Pomwepo Saulo adayesa kubaya Davide ndi kumkhomera ku chipupa. Koma Davide adauleŵa mkondowo, kotero kuti udangolasa chipupa. Ndipo adathaŵa napulumuka.
11
Usiku womwewo Saulo adatuma anthu kunyumba kwa Davide kuti akambisalire, kuti choncho akamuphe Davide m'maŵa. Koma Mikala, adauza mwamuna wake Davide kuti, “Mukapanda kupulumutsa moyo wanu usiku uno, maŵa muphedwa.”
12
Choncho Mikala adamtulutsira Davideyo pa windo, ndipo adathaŵa.
13
Mikalayo adatenga fano lam'nyumba naligoneka pa bedi, naika mtsamiro wa ubweya wambuzi kumutu kwake kwa fanolo, nalifunditsa nsalu.
14
Pamene anthu a Saulo aja adafika kuti adzamgwire Davide, Mikala adati, “Davide akudwala.”
15
Koma Saulo adaŵatumanso anthuwo kuti akamgwire ndithu Davideyo. Adaŵauza kuti, “Mubwere naye kuno, mumnyamulire pabedi pomwepo kuti ndidzamuphe.”
16
Anthuwo atakaloŵa, adangoona fano pabedipo ndi mtsamiro wa ubweya wambuzi kumutu kwake kwa fanolo.
17
Atamva zimenezi Saulo adafunsa Mikala kuti, “Chifukwa chiyani wandinyenga chotere pa kulola kuti mdani wanga athaŵe?” Mikala adayankha kuti, “Davide adaandiwuza kuti, ‘Undilole ndipite. Ngati sutero, ndikupha.’ ”
18
Choncho Davide adathaŵa napulumuka, nakafika kwa Samuele ku Rama. Adafotokozera Samuele zonse zimene Saulo adamuchita. Tsono Davideyo pamodzi ndi Samuele adakakhala ku Nayoti.
19
Saulo atamva kuti Davide ali ku Nayoti ku Rama,
20
pompo adatumanso anthu kuti akamgwire. Anthuwo adaona gulu la aneneri akuvina namalosa, Samuele akuŵatsogolera. Pamenepo mzimu wa Mulungu udaŵaloŵa anthuwo ndipo nawonso adayamba kulosa.
21
Saulo atazimva zimenezo, adatuma anthu ena, ndipo nawonso adayamba kulosa. Adatumanso anthu ena kachitatu, nawonso adayamba kulosa.
22
Choncho Saulo mwini wake adanyamuka napita ku Rama, nakafika pa chitsime chachikulu chimene chili ku Seku. Ndipo adafunsa kuti, “Kodi Samuele ndi Davide ali kuti?” Munthu wina adati, “Ali ku Nayoti ku Rama.”
23
Saulo adachoka napita ku Nayoti ku Rama. Nayenso mzimu wa Mulungu udamloŵa ndipo ankayenda akuvina namalosa mpaka kukafika ku Nayoti ku Rama.
24
Nayenso adavula zovala zake namalosa pamaso pa Samuele, kenaka nkugona chamaliseche tsiku lonse, usana ndi usiku. Choncho padayambika chisudzo chakuti, “Kani Saulonso ali m'gulu la aneneri?”
← Chapter 18
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 20 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24
25
26
27
28
29
30
31