bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
1 Samuel 14
1 Samuel 14
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
← Chapter 13
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 15 →
1
Tsiku lina Yonatani, mwana wa Saulo, adauza mnyamata womnyamulira zida zake zankhondo kuti, “Tiye tiwolokere tipite ku kaboma kankhondo ka Afilisti tsidya ilo.” Koma sadauze bambo wake.
2
Saulo ankakhala m'malire a Gibea patsinde pa mtengo wa makangaza ku Migironi. Anthu amene anali naye analipo 600 pamodzi.
3
Panalinso Ahiya, wansembe amene ankavala efodi. Iyeyo anali mwana wa Ahitubi, mbale wa Ikabodi mwana wa Finehasi. Finehasiyo anali mwana wa Eli, wansembe wa Chauta ku Silo. Tsono anthu sankadziŵa kuti Yonatani wachokapo.
4
Pampata pamene Yonatani ankafuna kudzerapo kuti akafike ku kaboma kankhondo kaja, panali thanthwe lotsetsereka mbali ina, ndi lina lotsetsereka mbali inanso. Dzina la thanthwe lina ankati Bozezi, ndipo linalo ankati Sene.
5
Thanthwe lina linali kumpoto kuyang'anana ndi Mikimasi, ndipo linalo linali kumwera kuyang'anana ndi Geba.
6
Yonatani adauza mnyamata wake uja kuti, “Tiye tiwolokere tipite ku kaboma kankhondo ka anthu osaumbalidwaŵa. Mwina mwake Chauta atigwirira ntchito. Pakuti palibe chomletsa Chauta kutipambanitsa ngakhale tikhale ochepa chotani.”
7
Mnyamata wakeyo adati, “Muchite zonse monga momwe mtima wanu ufunira. Ine ndili nanu, ndipo monga momwe mukuganizira inu, ine mmomwemonso.”
8
Tsono Yonatani adati, “Tiwolokere kwa anthuwo, ndipo tikadziwonetse kwa iwo.
9
Akatiwuza kuti, ‘Dikirani mpaka tikupezeni,’ tikangoima pamalo pathu, osapita kwa iwowo.
10
Koma akanena kuti, ‘Bwerani kuno,’ ife tikapitadi, pakuti Chauta waapereka anthuwo m'manja mwathu. Chimenechi chidzakhala chizindikiro kwa ife.”
11
Choncho aŵiriwo adadziwonetsa ku kaboma kankhondo ka Afilisti. Tsono Afilisti adati, “Taonani Ahebri akutuluka m'maenje m'mene ankabisala.”
12
Ndipo anthu akukabomawo adafuulira Yonatani ndi mnyamata wake uja kuti, “Tabwerani kuno, muwona!” Apo Yonatani adauza mnyamata wakeyo kuti, “Unditsate, Chauta wapereka anthuŵa m'manja mwa Aisraele.”
13
Choncho Yonatani adakwera chokwaŵa, mnyamata wake uja akumtsata pambuyo. Tsono Yonatani adaŵathira nkhondo Afilistiwo ndi kumaŵagwetsa, mnyamata wake uja nkumaŵapha pambuyo pa iyeyo.
14
Anthu amene Yonatani ndi mnyamata wake uja adapha nthaŵi yoyamba analipo ngati makumi aŵiri, ndipo adaŵaphera pa malo ochepa okwanira ngati theka la ekala.
15
Tsono Afilisti onse m'dzikomo adasokonezeka ndi mantha aakulu. Ankhondo a ku kaboma kankhondo kaja ndi anzao enanso ankanjenjemera kwambiri. Kudachita chivomezi ndipo kugwedezeka kwa dziko kudakulitsa mantha a Afilisti aja.
16
Alonda a Saulo a ku Gibea ku dziko la Benjamini poti ayang'ane, adangoona chigulu cha adani chikumwazikira uku ndi uku.
17
Tsono Saulo adauza anthu amene anali naye aja kuti, “Ŵerengani anthu, ndipo muwone amene achokapo.” Ataŵaŵerenga, adaona kuti Yonatani ndi mnyamata womnyamulira zida uja palibe.
18
Apo Saulo adauza Ahiya kuti, “Bwera nayo kuno efodiyo.” Nthaŵi imeneyo efodiyo inali ndi Ahiya pamaso pa Aisraele.
19
Pamene Saulo ankalankhula ndi wansembeyo, phokoso linkakulirakulira ku zithando za Afilisti. Tsono Saulo adauza wansembe uja kuti, “Leka, usaombeze!”
20
Pamenepo Saulo pamodzi ndi anthu amene anali naye adasonkhananso napita kukamenya nkhondo, ndipo adaona Afilisti akungophana okhaokha. Motero kunali chisokonezo chachikulu kwambiri.
21
Ahebri ena amene kale adaali pamodzi ndi Afilistiwo, ndipo anali atapita nao ku zithandozo, iwonso adatembenuka nakhala pamodzi ndi Aisraele a mbali ya Saulo ndi Yonatani.
22
Chimodzimodzinso Aisraele amene adaabisala m'dziko lamapiri la Efuremu, atamva kuti Afilisti akuthaŵa, nawonso adaŵathamangira Afilistiwo naŵathira nkhondo.
23
Ndipo nkhondoyo idapitirira mpaka kubzola mzinda wa Betaveni. Umu ndimo m'mene Chauta adapulumutsira Aisraele tsiku limenelo.
24
Koma ankhondo a Aisraele adavutika tsiku limene lija, pakuti Saulo adaŵaopseza pakunena kuti, “Atembereredwe amene adye kanthu kusanade, ndisanalipsire adani anga.” Motero panalibe ndi mmodzi yemwe amene adalaŵa chakudya.
25
Tsono onse adaloŵa m'nkhalango ina m'mene munali uchi.
26
Ataloŵa m'nkhalangomo, adangoona uchi ukukha pansi, koma panalibe amene adatengako kuika pakamwa, poti ankaopa temberero lija.
27
Koma Yonatani anali asanamve za temberero la bambo wake lija. Choncho adatosa chisa cha njuchi ndi nsonga ya ndodo imene inali m'manja mwake, naika uchi wake pakamwa naadya. Atatero m'maso mwake mudachita kuti ngwee.
28
Tsono mmodzi mwa anthuwo adati, “Bambo wanu waopseza anthu pakunena kuti, ‘Atembereredwe amene adye kanthu lero.’ Nchifukwa chake anthuŵa akuchita ngati akomoke ndi njala.”
29
Tsono Yonatani adati, “Bambo wanga wavutitsa anthu onse. Taonani ine m'maso mwanga mwayera, chifukwa ndalaŵako uchiwu.
30
Kukadakhala bwino kwambiri, anthu akadadya mwaufulu lero zofunkha zimene adazipeza kwa adani ao. Zidakatero bwenzi tsopano lino titapha Afilisti ambiri.”
31
Tsikulo Aisraele adapha Afilisti kuyambira ku Mikimasi mpaka ku Ayaloni. Koma Aisraelewo anali pafupi kukomoka nayo njala.
32
Motero adathamangira pa zofunkha, ndipo adatenga nkhosa, ng'ombe ndi makonyani, nazipha. Ndipo adazidya pamodzi ndi magazi omwe.
33
Koma ena adauza Saulo kuti, “Onani, anthu akuchimwira Chauta podyera kumodzi ndi magazi.” Saulo adati, “Mwaukira Chauta lero! Pezani mwala waukulu muukunkhunizire kuno.”
34
Ndipo adatinso, “Mwazikanani pakati pa anthu, muŵauze kuti, ‘Aliyense abwere ndi ng'ombe yake, kapena nkhosa yake, aziphere pompano, kenaka adye. Ndipo musachimwire Chauta podyera kumodzi ndi magazi.’ ” Motero aliyense mwa anthuwo adabwera ndi ng'ombe yake usiku umenewo, naiphera komweko.
35
Tsono Saulo adamangira Chauta guwa. Limeneli linali guwa loyamba limene Sauloyo adamangira Chauta.
36
Pamenepo Saulo adati, “Tiyeni tipite usiku, tilondole Afilisti, ndipo tilande zinthu zao mpaka m'maŵa kutacha. Tisasiyepo ndi mmodzi yemwe mwa iwo.” Anthuwo adati, “Chitani chilichonse chimene chikukukomerani.” Koma wansembe adati, “Tiyeni tiyambe tapempha nzeru kwa Mulungu.”
37
Tsono Saulo adafunsa Mulungu kuti, “Kodi tiŵalondole Afilistiŵa? Kodi muŵapereka m'manja mwathu?” Koma Mulungu sadamuyankhe kanthu tsiku limenelo.
38
Apo Saulo adati, “Bwerani kuno nonse atsogoleri a anthu. Tiwone ndi tchimo lanji lachitika lero.
39
Pali Chauta, Mpulumutsi wa Aisraele, wochimwayo ngakhale akhale mwana wanga Yonatani, afe ndithu.” Koma panalibe ndi mmodzi yemwe pakati pa anthu onsewo amene adamuyankha.
40
Tsono adauza Aisraelewo kuti, “Inu mukhale mbali imodzi, ine ndi mwana wanga Yonatani tikhalanso mbali ina.” Anthuwo adauza Saulo kuti, “Muchite zimene zikukomereni.”
41
Nchifukwa chake Saulo adati, “Inu Chauta, Mulungu wa Aisraele, chifukwa chiyani simudandiyankhe ine mtumiki wanu lero lino? Ngati wolakwa ndineyo kapena mwana wanga Yonatani, Inu Chauta, Mulungu wa Aisraele, aoneke ndi Urimu. Koma tchimolo likakhala la Aisraele, aoneke ndi Tumimu.” Maere adagwera Yonatani ndi Saulo, anthu nkupulumuka.
42
Tsono Saulo adati, “Chitani maere pakati pa ine ndi mwana wanga Yonatani.” Ndipo maere adagwera Yonatani.
43
Apo Saulo adauza Yonatani kuti, “Tandiwuza zimene wachita.” Yonatani adauza bambo wakeyo kuti, “Ndidalaŵako uchi pang'ono ndi nsonga ya ndodo yanga. Ndiye ai, chomwecho, ine ndili wokonzeka kuti ndife.”
44
Apo Saulo adati, “Mulungu andilange ine, ngakhale kundipha kumene, ngati suufa iwe Yonatani.”
45
Tsono anthu adafunsa Saulo kuti, “Kodi afe Yonatani amene wagwira ntchito yopulumutsa Aisraele kunkhondo? Sizingatheke mpang'ono pomwe. Pali Chauta wamoyo! Tsitsi nlimodzi lomwe la kumutu kwake silipezeka lothothoka. Zimene wachita lerozi, wamthandiza ndi Mulungu.” Motero anthu adamupulumutsa Yonatani, ndipo sadaphedwe.
46
Pambuyo pake Saulo adaleka kuŵathamangira Afilisti, ndipo Afilistiwo adabwerera kwao.
47
Pamene Saulo adakhala mfumu yolamulira Aisraele, adamenyana nkhondo ndi adani ake onse omzungulira. Adamenyana ndi Amowabu, Aamoni, Aedomu, mafumu a ku Zoba ndiponso Afilisti. Kulikonse kumene ankapita, ankaŵagonjetsa.
48
Adachita zamphamvu, ndipo adagonjetsa Aamaleke. Motero adapulumutsa Aisraele kwa anthu amene ankaŵalanda zinthu zao.
49
Ana aamuna a Saulo anali Yonatani, Isivi ndi Malikisuwa. Analinso ndi ana aŵiri aakazi, wamkulu anali Merabi, wamng'ono anali Mikala.
50
Mkazi wa Saulo anali Ahinowamu mwana wa Ahimaazi. Ndipo mkulu wa ankhondo a Saulo anali Abinere, mwana wa Nere, mbale wa bambo wa Saulo.
51
Kisi bambo wa Saulo ndipo Nere bambo wa Abinere, anali ana a Abiyele.
52
Pa moyo wake wonse Saulo ankakhalira kuchita nkhondo ndi Afilisti. Tsono ankati akaona munthu wamphamvu kapena wolimba mtima, ankamulemba m'gulu lake lankhondo.
← Chapter 13
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 15 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24
25
26
27
28
29
30
31