bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
1 Samuel 13
1 Samuel 13
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
← Chapter 12
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 14 →
1
Saulo adaloŵa ufumu ali ndi zaka 30, ndipo adalamulira Aisraele zaka ngati 42.
2
Nthaŵi ina iye adasankha Aisraele 3,000. Mwa ameneŵa, 2,000 anali ndi Sauloyo ku Mikimasi ndi ku dziko lamapiri ku Betele, ndipo 1,000 anali ndi Yonatani ku Gibea m'dziko la Benjamini. Anthu ena onse otsala adaŵabweza kwao.
3
Yonatani adapha mkulu wa ankhondo wachifilisti amene anali ku Geba, ndipo Afilisti adamva zimenezi. Apo Saulo adatuma amithenga kuti alize lipenga lankhondo m'dziko lonselo, nanena kuti, “Ahebri amve.”
4
Ndipo Aisraele onse adamva mbiri yakuti Saulo adapha mkulu wa ankhondo wachifilisti, ndiponso kuti Afilisti anali ataipidwa kwambiri ndi Aisraele. Motero anthu adaitanidwa kuti abwere kwa Saulo ku Giligala.
5
Tsono Afilisti adasonkhana pamodzi kuti amenyane nkhondo ndi Aisraele. Adasonkhanitsa magaleta ankhondo 30,000, okwera pa akavalo 6,000 ndi ankhondo ochuluka ngati mchenga wa m'mbali mwa nyanja. Iwowo adapita nakamanga zithando zao ku Mikimasi, kuvuma kwa Betaveni.
6
Pamene Aisraele adaona kuti ali m'zoopsa, poti anali atapanikizidwadi kwambiri, adakabisala m'mapanga, m'maenje, m'matanthwe, m'makwaŵa ndi m'zitsime.
7
Ena adaoloka Yordani mpaka kukafika ku dziko la Gadi ndi ku Giliyadi. Saulo anali ku Giligalabe, ndipo anthu okhala naye anali njenjenje ndi mantha.
8
Sauloyo adadikira masiku asanu ndi aŵiri, monga momwe adaanenera Samuele. Koma Samueleyo sadafike ku Giligala, ndipo anthu adayamba kumthaŵira Saulo uja.
9
Choncho Saulo adati, “Bwera nayoni kuno nsembe yopserezayo pamodzi ndi nsembe zachiyanjano zija.” Ndipo Saulo adapereka nsembe yopsereza ija.
10
Atangomaliza kupereka nsembe yopserezayo, adangoona Samuele watulukira. Tsono Saulo adapita kukakumana naye ndi kumulonjera.
11
Samuele adamufunsa Sauloyo kuti, “Nanga nchiyaninso mwachitachi?” Iye adayankha kuti, “Pamene ndinaona kuti anthu akundithaŵira, ndipo kuti inuyo nthaŵi imene mudaanena ija simudabwere, ndiponso kuti Afilisti adasonkhana ku Mikimasi,
12
ndinati, ‘Tsopano Afilisti abwera kudzandithira nkhondo ku Giligala kuno, ine ndisanapemphe Chauta kuti andikomere mtima.’ Motero ndinadzikakamiza kupereka nsembe yopserezayi.”
13
Apo Samuele adamuuza kuti, “Mwachitatu zopusa. Simudatsate zimene Chauta, Mulungu wanu, adakulamulani. Mukadazitsata, bwenzi Chauta atakhazikitsa ufumu wanu pakati pa Aisraele mpaka muyaya.
14
Koma tsopano ufumu wanu sudzakhalitsa. Chauta wadzifunira yekha munthu wa kumtima kwake. Chauta wamsankha munthuyo kuti akhale mfumu yolamulira anthu ake, chifukwa inu simudatsate zimene Iye adakulamulani.”
15
Atatero Samuele adanyamuka ku Giligala napita ku Gibea ku dziko la Benjamini. Saulo adaŵerenga anthu amene anali naye, ndipo adapeza kuti alipo 600.
16
Tsono iyeyo ndi mwana wake Yonatani, pamodzi ndi anthu amene anali nawowo, adakhala ku Geba ku dziko la Benjamini. Koma Afilisti adamanga zithando zankhondo ku Mikimasi.
17
Ankhondo a Filisti adatuluka kuchoka ku zithando zao m'magulu atatu. Gulu limodzi lidalunjika ku Ofura ku dziko la Suwala.
18
Gulu lina lidalunjika ku Betehoroni, ndipo lina lidalunjika ku malire oyang'anana ndi chigwa cha Zeboimu chakuchipululu.
19
Nthaŵi imeneyi nkuti mulibe msuli ndi mmodzi yemwe m'dziko lonse la Israele, chifukwa Afilisti ankati, “Tisaŵalole Ahebri kuti azidzisulira okha malupanga ndi mikondo.”
20
Motero Mwisraele aliyense ankapita kwa Afilisti kukasanjitsa pulao kapena khasu lake, ndi kukanoletsa nkhwangwa yake kapena chikwakwa.
21
Mtengo wonoletsera nkhwangwa unali ndalama imodzi, ndipo mtengo wosanjitsira makasu ndi wosongoletsera zisonga unali ndalama ziŵiri.
22
Motero tsiku lankhondolo panalibe lupanga kapena mkondo m'manja mwa Mwisraele aliyense amene ankatsata Saulo ndi Yonatani. Koma Saulo ndi mwana wake Yonatani, iwo okha ndiwo anali nazo zida.
23
Tsono Afilisti adatuma kagulu kankhondo kukalonda mpata wa Mikimasi.
← Chapter 12
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 14 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24
25
26
27
28
29
30
31