bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
1 Samuel 21
1 Samuel 21
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
← Chapter 20
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 22 →
1
Davide adakafika ku Nobu kwa wansembe Ahimeleki. Ahimelekiyo adadzamchingamira akunjenjemera, namufunsa kuti, “Zatani kuti muli nokha popanda ndi mmodzi yemwe wokuperekezani?”
2
Davide adayankha kuti, “Mfumu yandituma ndipo yandilamula kuti ndisauze munthu wina aliyense zimene yanditumazo. Kunena za anthu anga, ndapangana nawo kuti tikakumane pa malo ena ake.
3
Kodi muli ndi chakudya? Mundipatseko mitanda isanu yabuledi kapena chakudya chilichonse chimene muli nacho pano.”
4
Wansembeyo adayankha kuti, “Pano ndilibe buledi wamba, koma alipo ndi buledi wachipembedzo. Ngati anthu anu sadakhale ndi akazi ao, angathe kudya.”
5
Davide adayankha kuti, “Kunena zoona, nthaŵi zonse tikakhala pa ulendo, timakhala odzimanga. Anthu anga amakhala odzimanga ngakhale pa ulendo wamba, nanji lero pamene tili pa ulendo woterewu!”
6
Apo wansembeyo adapereka buledi wachipembedzo kwa Davide, pakuti kunalibe buledi wina, koma buledi yekha woperekedwa kwa Chauta. Buledi wake ndi amene anali atamchotsa pamaso pa Chauta kuti akaikepo wina wamoto.
7
Tsiku limenelo munthu wina mwa antchito a Saulo anali pomwepo, pakuti adaayenera kuchita mwambo wachipembedzo ku nyumba ya Chauta. Munthuyo dzina lake anali Doegi Mwedomu, kapitao wa abusa a Saulo.
8
Davide adafunsa Ahimeleki kuti, “Kodi kulibe mkondo kuno kapena lupanga? Paja ine sindidabwere ndi lupanga langa kapena zida zanga chifukwa ntchito ya mfumuyo inali yofulumira.”
9
Wansembeyo adayankha kuti, “Lupanga la Goliyati Mfilisti uja amene mudamupha ku chigwa cha Ela, nlokulunga m'nsalu paseli pa chovala cha efodi. Ngati mufuna, mungathe kutenga limenelo, chifukwa kulibenso lina kuno, koma lokhalo.” Davide adati, “Palibe lina lofanafana ndi limenelo. Patseni lomwelo.”
10
Tsiku lomwelo Davide adanyamuka kuthaŵa Saulo, ndipo adapita kwa Akisi mfumu ya ku Gati.
11
Tsono nduna za Akisi zidamufunsa Akisiyo kuti, “Kodi ameneyu si Davide, mfumu ya dziko? Kodi iyeyu si uja pomuvinira ankamuimbira kuti, “ ‘Saulo wapha zikwi, inde, koma Davide wapha zikwi khumikhumi!’ ”
12
Mau ameneŵa Davide adamloŵa mu mtima kwambiri, ndipo adayamba kuwopa Akisi mfumu ya ku Gati.
13
Choncho adasintha khalidwe lake pamaso pao, nadzisandutsa ngati wamisala, namangolembalemba pa zitseko za chipata, malovu ali chuchuchu kutsikira ku ndevu.
14
Tsono Akisi adauza nduna zake kuti, “Mukuwona kuti munthuyu ngwamisala. Chifukwa chiyani tsono mwabwera naye kwa ine?
15
Kodi ndikusoŵa anthu amisala kuti muzibwera naye kuno munthu ameneyu, namachita zamisala zake pamaso panga? Ha! Munthu wotereyu angaloŵe bwanji m'nyumba mwanga muno?”
← Chapter 20
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 22 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24
25
26
27
28
29
30
31